Ezekieli 9:1-11

9  Kenako iye analankhula mokuwa ine ndikumva, kuti: “Uzani anthu amene asankhidwa kuti awononge mzindawu kuti abwere pafupi. Aliyense anyamule chida chake chowonongera.”  Ndiyeno ndinaona amuna 6 akubwera kuchokera kuchipata chakumtunda+ choyang’ana kumpoto, aliyense atanyamula chida chake chophwanyira. Pakati pawo panali munthu mmodzi atavala zovala zansalu.+ M’chiuno mwake munali kachikwama ka mlembi, konyamuliramo inki ndi zolembera. Anthuwo analowa mkati n’kuima pambali pa guwa lansembe lamkuwa.+  Tsopano ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli+ unachoka pamwamba pa akerubi+ pamene unali, ndipo unapita pakhomo la malo opatulika.+ Kenako Mulungu anayamba kulankhula mofuula kwa munthu wovala zovala zansalu uja,+ yemwe m’chiuno mwake munali kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera.  Pamenepo Yehova anauza munthu uja kuti: “Uyendeyende mumzinda wonse wa Yerusalemu, ndipo ulembe chizindikiro pamphumi za anthu amene akuusa moyo* ndi kubuula+ chifukwa cha zonyansa zonse zimene zikuchitika mumzindawu.”+  Ndiyeno iye anauza amuna ena aja ine ndikumva, kuti: “M’tsatireni ameneyu. Muyendeyende mumzindamo n’kumapha anthu. Diso lanu lisamve chisoni ndipo inuyo musachite chifundo.+  Mupheretu nkhalamba, anyamata, anamwali, tiana, ndi amayi.+ Koma musayandikire munthu aliyense amene ali ndi chizindikiro,+ ndipo muyambire pamalo anga opatulika.”+ Chotero iwo anayambira kupha akuluakulu amene anali panyumbapo.+  Iye anawauzanso kuti: “Ipitsani nyumbayi ndipo mudzaze mabwalo ake ndi mitembo ya anthu ophedwa.+ Pitani!” Iwo anapitadi n’kukapha anthu mumzindamo.  Pamene amunawo anali kupha anthu, ine ndinatsala ndekha wamoyo, ndipo ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ Kenako ndinafuula kuti: “Kalanga ine,+ Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kodi muwononga otsala onse a Isiraeli pamene mukukhuthulira ukali wanu pa Yerusalemu?”+  Iye anandiyankha kuti: “Zolakwa za nyumba ya Isiraeli ndi Yuda+ n’zazikulu kwambiri.+ Dziko lawo ladzaza ndi magazi okhetsedwa,+ ndipo mumzindamo mwadzaza zaukathyali,+ pakuti iwo akunena kuti, ‘Yehova wachokamo m’dziko muno,+ ndipo Yehova sakuona.’+ 10  Chotero inenso diso langa silimva chisoni+ ndipo sindichita chifundo.+ Ndiwabwezera mogwirizana ndi njira zawo.”+ 11  Tsopano munthu wovala zovala zansalu uja, yemwe m’chiuno mwake munali kachikwama konyamuliramo inki ndi zolembera, anabwera n’kudzanena kuti: “Ndachita monga momwe munanditumira.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.