Ezekieli 7:1-27

7  Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti:  “Iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza dziko la Isiraeli, kuti: ‘Mapeto! Mapeto afika kumalekezero anayi a dzikoli.+  Tsopano mapeto akufikira,+ ndipo ndikutumizira mkwiyo wanga. Ndikuweruza mogwirizana ndi njira zako+ ndipo ndikubwezera chifukwa cha zonyansa zako zonse.  Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo. Ine ndidzakubwezera mogwirizana ndi njira zako, ndipo ukamadzalangidwa udzaona zotsatirapo za zinthu zako zonyansa zimene zili pakati pako.+ Chotero anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Tsoka! Tsoka loti silinaonekepo likubwera.+  Mapeto akubwera,+ ali m’njira. Akufikira mwadzidzidzi. Akubwera ndithu.+  Nkhata yamaluwa ya tsoka ibwera kwa inu anthu okhala m’dzikoli. Nthawi ikwana. Tsikulo layandikira.+ M’dzikoli muli chisokonezo, osati phokoso lachisangalalo lomveka m’mapiri.  “‘Posachedwapa, ndikukhuthulirani ukali wanga,+ ndipo mkwiyo wanga ndiuthetsera pa inu.+ Ndikuweruzani mogwirizana ndi njira zanu,+ ndipo ndikubwezerani chifukwa cha zonyansa zanu zonse.  Diso langa silidzakumverani chisoni+ ndipo sindidzakuchitirani chifundo.+ Ndidzakubwezerani mogwirizana ndi njira zanu, ndipo mudzaona zotsatirapo za zinthu zanu zonyansa zimene zili pakati panu.+ Ndiyeno anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, amene ndikukuphani.+ 10  “‘Taona! Tsikulo likubwera.+ Nkhata yamaluwa ya tsoka ili m’njira.+ Ndodo yachita maluwa.+ Kudzikuza kwaphuka.+ 11  Chiwawa chasanduka ndodo ya zoipa.+ Anthuwo paokha, chuma chawo, ndiponso kutchuka kwawo, sizidzawapulumutsa ku chilango. 12  Nthawi idzakwana, tsikulo lidzafika. Wogula asasangalale+ ndipo wogulitsa asalire, pakuti mkwiyo wa Mulungu wayakira khamu lonselo. 13  Wogulitsa sadzabwerera ku chinthu chimene chinagulitsidwa akadali ndi moyo, pakuti masomphenyawo ndi akhamu lonselo. Palibe amene adzabwerere kapena kukhalabe ndi moyo kudzera m’zolakwa zake. 14  “‘Iwo aliza lipenga+ ndipo aliyense wakonzeka, koma palibe amene akupita kunkhondo chifukwa mkwiyo wanga wayakira khamu lonselo.+ 15  Lupanga+ lili panja ndipo mliri ndi njala zili mkati.+ Yemwe ali kutchire adzaphedwa ndi lupanga, ndipo amene ali mumzinda njala ndi mliri zidzawasakaza.+ 16  Anthu awo opulumuka adzathawa+ ndipo adzakhala pamapiri ngati njiwa za m’zigwa,+ aliyense akulira chifukwa cha zolakwa zake. 17  Anthu onse ataya mtima+ ndipo mawondo onse akungochucha madzi.*+ 18  Iwo avala ziguduli,*+ ndipo thupi lawo lonse likunjenjemera.+ Pankhope zawo zonse pali manyazi+ ndipo m’mitu yawo yonse muli mipala.+ 19  “‘Siliva wawo adzamuponyera mumsewu ndipo golide wawo adzaipidwa naye. Siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa m’tsiku la mkwiyo waukulu wa Yehova.+ Iwo sadzakhuta ndipo m’matumbo mwawo simudzadzaza, pakuti chumacho chakhala chowapunthwitsa ndiponso chowachititsa zolakwa.+ 20  Aliyense akunyada chifukwa cha chinthu chake chokongoletsera. Iwo agwiritsira ntchito siliva ndi golide kupangira mafano awo onyansa,+ ndi zinthu zawo zonyansa.+ N’chifukwa chake ndidzachititse kuti zinthu zimenezi adzaipidwe nazo.+ 21  Ndidzazipereka m’manja mwa alendo kuti zikhale zawo ndi kwa anthu oipa a padziko lapansi kuti azitenge,+ ndipo adzaziipitsa. 22  “‘Ine ndidzatembenuza nkhope yanga kuti ndisawayang’ane+ ndipo adzaipitsa malo anga obisika. Akuba adzalowa m’malowo n’kuipitsamo.+ 23  “‘Panga unyolo+ chifukwa dzikolo ladzaza ziweruzo za magazi,+ ndipo mumzindamo mwadzaza chiwawa.+ 24  Chotero ndidzabweretsa anthu oipa kwambiri a mitundu ina+ ndipo iwo adzalanda nyumba zawo.+ Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu+ ndipo malo awo opatulika adzaipitsidwa.+ 25  Anthu adzazunzika, adzafunafuna mtendere koma sudzapezeka.+ 26  M’dzikolo mudzakhala mavuto otsatizanatsatizana+ ndipo muzidzamveka mauthenga otsatizanatsatizana. Anthu azidzafunafuna masomphenya kwa mneneri.+ Ansembe sadzathanso kuphunzitsa malamulo aphindu. Anthu achikulire sadzaperekanso malangizo othandiza.+ 27  Mfumu idzalira,+ ndipo ngakhale mtsogoleri adzagwidwa ndi mantha.+ Manja a anthu a m’dzikolo adzanjenjemera chifukwa cha chisokonezo. Ndidzawachitira zinthu zogwirizana ndi njira zawo.+ Ndidzawaweruza mogwirizana ndi ziweruzo zawo.+ Chotero iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza kuti adzakodzedwa chifukwa cha mantha.
Ena amati “masaka.”