Ezekieli 6:1-14
6 Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana kumapiri a Isiraeli ndipo ulosere+ kwa iwo.+
3 Unene kuti, ‘Inu mapiri a Isiraeli, imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa:+ Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kwa mapiri, zitunda,+ mitsinje ndi zigwa: “Ine ndidzakubweretserani lupanga ndipo ndidzawononga malo anu okwezeka.+
4 Maguwa anu ansembe adzasiyidwa.+ Maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzaphwanyidwa, ndipo anthu anu ophedwa ndidzawagwetsera pamaso pa mafano anu onyansa.*+
5 Ndidzaika mitembo ya ana a Isiraeli pamaso pa mafano awo onyansa, ndipo mafupa anu ndidzawamwaza kuzungulira maguwa anu ansembe.+
6 M’malo anu onse okhala,+ mizinda idzawonongedwa+ ndipo malo okwezeka adzasakazidwa kuti akhale mabwinja ndiponso kuti maguwa anu ansembe akhale osakazidwa.+ Chotero maguwa anu ansembewo adzaphwanyidwa+ ndipo mafano anu onyansa sadzakhalaponso.+ Maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzagwetsedwa+ ndipo ntchito za manja anu zidzafafanizidwa.
7 Mitembo ya anthu ophedwa a mtundu wanu idzakhala pakati panu,+ ndipo inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+
8 “‘“Zimenezi zikadzachitika, ndidzachititsa kuti ena a inu asaphedwe ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu, mukadzamwazikana kupita kumayiko osiyanasiyana.+
9 Opulumuka anu akadzagwidwa n’kutengedwa kukakhala pakati pa mitundu ina ya anthu, ndithu adzandikumbukira.+ Adzakumbukira mmene ndinamvera kupweteka chifukwa cha mtima wawo wadama umene unawachititsa kundipandukira.+ Adzakumbukiranso mmene ndinamvera kupweteka chifukwa cha maso awo othamangira mafano awo onyansa pofuna kuchita nawo zadama.+ Iwo adzachita manyazi ochita kuonekera pankhope zawo, chifukwa cha zinthu zonse zoipa ndi zonyansa zimene anachita.+
10 Ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova. Sikuti ndangonena pachabe+ zoti ndidzawabweretsera tsoka limeneli.”’+
11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ombani m’manja+ ndipo pondani pansi mwamphamvu ndi mapazi anu. Munene kuti: “Kalanga ine!” chifukwa cha zoipa zonse zonyansa za nyumba ya Isiraeli.+ Pakuti iwo adzaphedwa ndi lupanga,+ njala+ ndi mliri.+
12 Yemwe ali kutali+ adzaphedwa ndi mliri. Yemwe ali pafupi adzaphedwa ndi lupanga. Yemwe watsala ali wotetezeka adzafa ndi njala, ndipo ukali wanga ndidzauthetsera pa iwo.+
13 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ Adzadziwa zimenezi mitembo ya anthu awo ikadzakhala pakati pa mafano awo onyansa+ kuzungulira maguwa awo onse ansembe,+ paphiri lililonse lalitali,+ pansonga zonse za mapiri,+ pansi pa mtengo uliwonse waukulu wamasamba obiriwira,+ ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wanthambi zambiri.+ Amenewa ndiwo malo amene anali kuperekerapo nsembe zafungo lokhazika mtima pansi kwa mafano awo onse onyansa.+
14 Ndidzawatambasulira dzanja langa powalanga+ ndipo dziko lawo ndidzalisandutsa bwinja. Malo awo onse okhala adzakhala bwinja loipa kuposa chipululu cha Dibula, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”
Mawu a M'munsi
^ Mawu amene anawagwiritsa ntchito m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”