Ezekieli 48:1-35

48  “Mayina a mafuko ndi awa. Fuko la Dani+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kumalire a kumpoto a dzikolo, m’mbali mwa msewu wa ku Heteloni+ wopita kumalire a Hamati.+ Malire a gawolo chakumpoto, akafikenso ku Hazara-enani,+ kumalire a Damasiko kufupi ndi Hamati. Gawolo likhale ndi malire kumbali ya kum’mawa ndi kumbali ya kumadzulo.  Fuko la Aseri+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Dani.  Fuko la Nafitali+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Aseri.  Fuko la Manase+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Nafitali.  Fuko la Efuraimu+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Manase.  Fuko la Rubeni+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Efuraimu.  Fuko la Yuda+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Rubeni.  Anthu inu mupereke gawo lina monga chopereka chanu. Gawolo lichite malire ndi gawo la fuko la Yuda ndipo likhale mikono 25,000 m’lifupi.+ M’litali mwake lifanane ndi magawo a mafuko aja. Malire a gawolo ayambire kum’mawa kukafika kumadzulo. Malo opatulika akhale pakati pa gawo limeneli.+  “Gawo loti mupereke kwa Yehova monga chopereka chanu likhale mikono 25,000 m’litali, ndipo m’lifupi likhale mikono 10,000. 10  Gawo limeneli likhale chopereka chopatulika cha ansembe.+ Mbali ya kumpoto, gawoli likhale mikono 25,000 m’litali mwake. Mbali ya kumadzulo likhale mikono 10,000 m’lifupi. Mbali ya kum’mawa likhale mikono 10,000 m’lifupi, ndipo mbali ya kum’mwera gawoli likhale mikono 25,000 m’litali. Pakati pa gawo limeneli pakhale malo opatulika a Yehova.+ 11  Gawo limeneli likhale la ansembe opatulika, ana a Zadoki,+ amene amanditumikira. Iwo sanandisiye ngati mmene anandisiyira Alevi amene anatsata ana a Isiraeli.+ 12  Ansembewo akhale ndi gawo lawo kuchokera pa gawo limene mupereke. Gawolo likhale lopatulika koposa ndipo lichite malire ndi gawo la Alevi.+ 13  “Alevi akhale ndi gawo+ pafupi ndi gawo la ansembe. M’litali mwake likhale mikono 25,000 ndipo m’lifupi likhale mikono 10,000. Malo onsewo akhale aatali mikono 25,000 ndipo m’lifupi mwake akhale okwana mikono 10,000.+ 14  Aleviwo asagulitse mbali iliyonse ya malowo kapena kuwasinthanitsa ndi chilichonse. Aliyense asapereke malo abwino kwambiriwo kwa munthu wa fuko lina pakuti ndi malo opatulika kwa Yehova.+ 15  “Malo otsala okwana mikono 5,000 m’lifupi ndi mikono 25,000 m’litali, akhale malo odetsedwa a mzinda.+ Malo amenewa akhale okhalamo anthu ndi odyetserako ziweto. Pakati pa malowa pakhale mzinda.+ 16  Miyezo ya mzindawo ikhale motere: Mbali ya kumpoto, mzindawo ukhale wautali mikono 4,500. Mbali ya kum’mwera ukhale wautali mikono 4,500. Mbali ya kum’mawa ukhale wautali mikono 4,500, ndipo mbali ya kumadzulo ukhalenso mikono 4,500. 17  Mzindawo ukhale ndi malo odyetserako ziweto.+ Mbali ya kumpoto malowo akhale aatali mikono 250. Mbali ya kum’mwera akhale mikono 250. Mbali ya kum’mawa akhale mikono 250, ndipo mbali ya kumadzulo malowo akhalenso mikono 250. 18  “Malo otsala akhale aatali mofanana ndi malo omwe ndi chopereka chopatulika.+ Akhale mikono 10,000 kum’mawa ndiponso mikono 10,000 kumadzulo. Malo amenewo achite malire ndi malo omwe ndi chopereka chopatulika. Zokolola za pamalowo zizikhala chakudya cha otumikira mumzindawo.+ 19  Anthu a mafuko onse a Isiraeli otumikira mumzinda ndiwo azidzalima malo amenewa.+ 20  “Malo onse oti aperekedwewo akhale aatali mikono 25,000 mbali iyi ndi mikono 25,000 mbali inayo. Anthu inu mupereke malo ofanana mbali zonse kuti akhale chopereka chopatulika ndiponso malo a mzinda. 21  “Malo otsala a mbali iyi ndi mbali inayo ya chopereka chopatulika ndiponso ya mzinda+ akhale a mtsogoleri+ wa anthu. Kumbali ya kum’mawa, malowo achite malire ndi malo operekedwa aja ndipo akhale mikono 25,000 m’lifupi. Kumbali ya kumadzulo, malowo achite malire ndi malo operekedwa aja ndipo akhale mikono 25,000 m’lifupi. Malo a mtsogoleriwo achokere kumbali ya kum’mawa kukafika kumbali ya kumadzulo mofanana ndi magawo a mafuko aja.+ Malo omwe ndi chopereka chopatulika komanso malo opatulika a Nyumba ija akhale pakati pa malo a mtsogoleriwa. 22  “Malo a Alevi komanso malo a mzinda akhale pakati pa malo a mtsogoleri. Malo a mtsogoleriwo achite malire ndi gawo la fuko la Yuda+ komanso gawo la fuko la Benjamini. 23  “Pa mafuko ena otsalawo, fuko la Benjamini+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo. 24  Fuko la Simiyoni+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Benjamini. 25  Fuko la Isakara+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Simiyoni. 26  Fuko la Zebuloni+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Isakara. 27  Fuko la Gadi+ likhale ndi gawo limodzi. Gawolo liyambire kum’mawa kukafika kumadzulo ndipo lichite malire ndi gawo la fuko la Zebuloni. 28  Malire a kum’mwera a dzikolo akhale malire a gawo la fuko la Gadi a mbali ya kum’mwera. Malirewo achokere ku Tamara+ kukafika kumadzi a Meribati-kadesi,+ kuchigwa+ cha Iguputo, mpaka ku Nyanja Yaikulu.+ 29  “Anthu inu mugawe dziko limeneli pakati pa mafuko onse a Isiraeli kuti likhale cholowa chawo+ ndi magawo awo,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 30  “Makomo otulukira mumzinda akhale motere: Malire a mbali ya kumpoto a mzindawo akhale mikono 4,500.+ 31  “Mayina a zipata za mzinda akhale ofanana ndi mayina a mafuko a Isiraeli. Mbali ya kumpoto kukhale zipata zitatu. Kukhale chipata chimodzi chotchedwa Rubeni, chipata chimodzi chotchedwa Yuda, ndi chipata chimodzi chotchedwa Levi. 32  “Malire a mzindawo a mbali ya kum’mawa akhale mikono 4,500. Kumeneko kukhalenso zipata zitatu. Kukhale chipata chimodzi chotchedwa Yosefe, chipata chimodzi chotchedwa Benjamini, ndi chipata chimodzi chotchedwa Dani. 33  “Malire a mzindawo a mbali ya kum’mwera akhale mikono 4,500. Kumeneko kukhalenso zipata zitatu. Kukhale chipata chimodzi chotchedwa Simiyoni, chipata chimodzi chotchedwa Isakara, ndi chipata chimodzi chotchedwa Zebuloni. 34  “Malire a mzindawo a mbali ya kumadzulo akhale mikono 4,500. Kumeneko kukhalenso zipata zitatu. Kukhale chipata chimodzi chotchedwa Gadi, chipata chimodzi chotchedwa Aseri, ndi chipata chimodzi chotchedwa Nafitali. 35  “Kuzungulira mzindawo pakhale mtunda wokwana mikono 18,000. Kuyambira pa tsiku limenelo, dzina la mzindawo lidzakhala lakuti, Yehova Ali Kumeneko.”+

Mawu a M'munsi