Ezekieli 46:1-24

46  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chipata choyang’ana kum’mawa cha bwalo lamkati+ chizikhala chotseka+ kwa masiku ogwira ntchito 6.+ Pa tsiku la sabata, ndi pa tsiku lokhala mwezi chipatacho chizitsegulidwa.+  Mtsogoleri wa anthu azilowa kuchokera panja n’kufika pakhonde la kanyumba ka pachipata+ ndipo aziima pafupi ndi felemu la chipatacho.+ Ndiyeno ansembe azimuperekera nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zake zachiyanjano. Mtsogoleriyo azigwada ndi kuwerama pakhomo la kanyumba ka pachipata,+ kenako azituluka koma chipatacho chisamatsekedwe kufikira madzulo.  Anthu a m’dzikoli azigwada ndi kuwerama pamaso pa Yehova pakhomo la kanyumba ka pachipata chimenechi pa masiku a sabata ndi pa masiku okhala mwezi.+  “‘Nsembe yopsereza yathunthu imene mtsogoleri wa anthu azipereka kwa Yehova pa tsiku la sabata, izikhala ana a nkhosa amphongo okwana 6 ndi nkhosa yamphongo imodzi. Nyama zonsezi zizikhala zopanda chilema.+  Popereka nkhosa yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa.+ Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse.+ Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+  Pa tsiku lokhala mwezi,+ azipereka ng’ombe yaing’ono yamphongo yopanda chilema kuchokera pagulu la ziweto. Aziperekanso ana a nkhosa amphongo 6 ndi nkhosa imodzi yamphongo. Nyama zonsezi zizikhala zopanda chilema.+  Popereka ng’ombe yaing’ono yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Popereka nkhosa yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa, azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+  “‘Mtsogoleri+ wa anthu akamalowa, azidzera mbali ya kukhonde ya kanyumba ka pachipata. Potuluka azidzeranso komweko.+  Anthu a m’dzikoli akafika pamaso pa Yehova kuti adzam’gwadire ndi kumuweramira pa nyengo za chikondwerero,+ munthu amene walowa kudzera pachipata cha kumpoto+ azidzatulukira pachipata cha kum’mwera.+ Amene walowera pachipata cha kum’mwera azidzatulukira pachipata cha kumpoto. Munthu aliyense asadzatulukire pachipata chimene analowera. Aliyense azidzangoyenda kupita kutsogolo mpaka kukatuluka. 10  Pamene anthuwo akulowa, mtsogoleri amene ali pakati pawo azilowa nawo limodzi, ndipo pamene akutuluka nayenso azituluka.+ 11  Pa nthawi ya zikondwerero+ ndi pa nyengo ya zikondwerero zanu, azipereka ng’ombe yaing’ono yamphongo pamodzi ndi nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Aziperekanso nkhosa yamphongo pamodzi ndi nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+ 12  “‘Mtsogoleri wa anthu akapereka kwa ansembe nsembe yopsereza yathunthu+ kuti ikhale nsembe yaufulu, kapena akapereka nsembe zachiyanjano kuti zikhale nsembe yaufulu yoperekedwa kwa Yehova, munthu wina azimutsegulira chipata cha kum’mawa.+ Mtsogoleriyo azipereka kwa ansembe nsembe yake yopsereza yathunthu ndi nsembe zake zachiyanjano mofanana ndi mmene amachitira pa tsiku la sabata.+ Akatero azituluka ndipo munthu wina azitseka chipatacho iye akatuluka.+ 13  “‘Tsiku ndi tsiku uzipereka kwa ansembe mwana wa nkhosa wamphongo wopanda chilema wosakwanitsa chaka. Uzim’pereka m’mawa uliwonse monga nsembe yopsereza yathunthu yoperekedwa kwa Yehova.+ 14  Popereka kwa ansembe mwana wa nkhosayo, uziperekanso nsembe yambewu m’mawa uliwonse yokwanira gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. Uziperekanso mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini kuti aziwawaza mu ufa wosalala.+ Lamulo lopereka nsembe yambewu kwa Yehova nthawi zonse lidzakhalapo mpaka kalekale. 15  M’mawa uliwonse, iwo azipereka kwa ansembe mwana wa nkhosa wamphongo, nsembe yambewu ndi mafuta, kuti zikhale nsembe yopsereza yathunthu ya nthawi zonse.’ 16  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Mtsogoleri wa anthu akapereka mphatso kwa mwana wake aliyense wamwamuna monga cholowa chake, mphatsoyo idzakhala chuma cha mwanayo. Chimenecho ndi chuma cha anawo ndipo chidzakhala cholowa chawo. 17  Koma akapereka cholowa kwa mmodzi wa antchito ake ngati mphatso kuchokera pa cholowa chake, cholowacho chidzakhala cha wantchitoyo mpaka chaka cha ufulu,+ kenako chidzabwezedwa kwa mtsogoleriyo. Koma cholowa choperekedwa kwa ana ake chidzakhala chawo mpaka kalekale. 18  Mtsogoleri wa anthu asamatenge cholowa chilichonse cha anthu ndi kuwakakamiza kuchoka m’malo awo.+ Ana ake aamuna aziwapatsa cholowa kuchokera pamalo amene ali nawo, kuti anthu anga asamwazikane ndi kuchoka m’malo awo.’”+ 19  Kenako munthu uja ananditenga n’kundilowetsa pakhomo+ limene linali pafupi ndi chipata chopita kuzipinda zodyeramo zopatulika. Zipindazi zinali za ansembe ndipo zinayang’ana kumpoto.+ M’mbali mwa zipindazo, kumbali ya kumadzulo ndinaonako malo. 20  Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Amenewa ndi malo amene ansembe aziwiritsirapo nsembe ya kupalamula+ ndi nsembe yamachimo,+ komanso pamene aziphikirapo nsembe yambewu.+ Aziphikira pamenepa kuti asamatulutse chilichonse kupita nacho kubwalo lakunja ndi kuyeretsa anthu.”+ 21  Kenako ananditengera kubwalo lakunja ndi kundipititsa pansanamira zinayi za m’makona a bwalolo. Kumeneko ndinaona kuti pafupi ndi nsanamira yoyamba ya pakona panali bwalo, chimodzimodzinso pafupi ndi nsanamira inayo. 22  M’makona onse anayi a bwalolo munali mabwalo ang’onoang’ono okwana mikono 40 m’litali ndi mikono 30 m’lifupi. Mabwalo onsewo anali ndi miyezo yofanana, ndipo anali ndi tinyumba tapakona. 23  Panali kakhoma kamiyala kuzungulira mkati monse mwa tinyumba tonse tinayi tapakonato. M’munsi monse mwa kakhoma kameneko munali malo ophikirapo.+ 24  Kenako anandiuza kuti: “Izi ndi nyumba zowiritsiramo nyama. Kumeneku n’kumene atumiki a pa Nyumbayi amawiritsirako nsembe zimene anthu amapereka.”+

Mawu a M'munsi