Ezekieli 45:1-25

45  “‘Anthu inu, pogawana dzikoli kuti likhale cholowa chanu,+ mudzapatule malo ena ndi kuwapereka kwa Yehova+ monga gawo loyera.+ M’litali mwa malo amenewo mudzakhale mikono 25,000, ndipo m’lifupi mudzakhale mikono 10,000.+ Malo onsewo adzakhale gawo loyera.  Pamalo amenewa padzakhale malo oyera okwana mikono 500 m’litali ndi mikono 500 m’lifupi. Malowa adzakhale ofanana mbali zonse.+ Kumbali zake zonse kudzakhale malo odyetserako ziweto okwana mikono 50.+  Kuchokera pa miyezo ya malo amenewa, udzayeze malo okwana mikono 25,000 m’litali ndi mikono 10,000 m’lifupi. M’malo amenewa mudzakhale malo opatulika amene ndi malo oyera koposa.+  Malo oyerawa adzakhale gawo la ansembe m’dzikoli.+ Ansembewo ndi atumiki a pamalo opatulika ndipo amayandikira kwa Yehova ndi kumutumikira.+ Malo amenewa adzakhale awo kuti adzamangepo nyumba zawo. Adzakhalenso malo opatulika omangapo nyumba yopatulika.  “‘Kudzakhalenso malo okwana mikono 25,000 m’litali ndi mikono 10,000 m’lifupi.+ Malo amenewa adzakhale a Alevi, atumiki a pa Nyumbayo. Aleviwo adzakhale ndi zipinda 20 zodyeramo chakudya.+  “‘Anthu inu mudzapereke malo okwana mikono 5,000 m’lifupi ndi mikono 25,000 m’litali kuti adzakhale malo a mzinda. Malo amenewa adzakhale moyandikana ndi chopereka chopatulika,+ ndipo adzakhale a anthu a nyumba yonse ya Isiraeli.  “‘Malo a mtsogoleri wa anthu adzakhale kumbali iyi ndi kumbali ina ya chopereka chopatulika+ ndi ya malo a mzinda. Adzakhale pafupi ndi chopereka chopatulika komanso pafupi ndi malo a mzindawo. Malo a mtsogoleriwo adzakhale kumadzulo ndi kum’mawa. M’litali mwake adzakhale ofanana ndi magawo a malo amene mafuko a Isiraeli adzalandire, kuchokera kumalire a kumadzulo kukafika kumalire a kum’mawa.+  Malo amenewa adzakhale cholowa cha mtsogoleriyo mu Isiraeli. Atsogoleri anga sadzazunzanso anthu anga,+ ndipo adzagawa dzikoli kwa anthu a nyumba ya Isiraeli malinga ndi mafuko awo.’+  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndatopa nanu inu atsogoleri a Isiraeli!’+ “‘Siyani ziwawa ndi kulanda zinthu za anthu anga.+ Muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ Lekani kulanda zinthu za anthu anga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 10  ‘Anthu inu muzikhala ndi masikelo olondola, muyezo wa efa* wolondola ndi mitsuko* yoyezera yolondola.+ 11  Muyezo wa efa ndi wa mtsuko woyezera uzikhala wofanana komanso wosasinthasintha. Muyezo wa mtsuko uzikhala wokwanira gawo limodzi mwa magawo 10 a homeri.* Gawo limodzi mwa magawo 10 la muyezo wa homeri lizifanana ndi muyezo wa efa.+ Muzipeza miyezo yoyenera ya zimenezi potengera muyezo wa nthawi zonse wa homeri. 12  Sekeli+ limodzi lizikwana magera 20.+ Muzitenga masekeli 20, masekeli 25 ndi masekeli 15 kuti ukhale muyezo wanu wa mane.’ 13  “‘Pa tirigu wanu wokwana homeri, muzitengapo gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa kuti likhale chopereka chanu. Pa balere wanu wokwana homeri muzipereka gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. 14  Poyeza mafuta oti muzipereka, muzigwiritsa ntchito mtsuko woyezera monga muyezo wanu wa nthawi zonse. Mtsukowo uzikwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa kori.* Mitsuko 10 izikwana homeri chifukwa mitsuko 10 imakwana homeri. 15  Muzipereka nkhosa imodzi kuchokera pagulu la nkhosa zanu. Muzipereka nkhosa imodzi pa ziweto 200 zilizonse mu Isiraeli.+ Muzipereka nsembe zimenezi pamodzi ndi nsembe zambewu,+ nsembe yopsereza yathunthu+ ndi nsembe zachiyanjano+ kuti muziphimba machimo a anthu,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 16  “‘Anthu onse a m’dzikoli azidzapereka zopereka zimenezi+ kwa mtsogoleri mu Isiraeli.+ 17  Mtsogoleri+ wa anthu adzapatsidwa udindo woyang’anira nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa.+ Iye azidzayang’anira nsembezo pa nthawi ya zikondwerero,+ pa masiku okhala mwezi,+ pa nthawi ya masabata+ ndi pa nthawi ya zikondwerero zonse za nyumba ya Isiraeli.+ Mtsogoleriyo ndi amene azidzapereka kwa ansembe nyama za nsembe yamachimo, nsembe yambewu, nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zachiyanjano kuti aphimbe machimo a nyumba ya Isiraeli.’ 18  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘M’mwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, uzitenga ng’ombe yamphongo yaing’ono yopanda chilema+ kuchokera pagulu la ziweto, ndipo uziyeretsa malo opatulika ku machimo.+ 19  Wansembe azitenga ena mwa magazi a nsembe yamachimo ndi kuwapaka pafelemu+ la Nyumbayi ndi pamakona anayi a chigawo chachitatu cha guwa lansembe.+ Aziwapakanso pafelemu la kanyumba ka pachipata cha bwalo lamkati. 20  Muzichitanso zimenezi pa tsiku la 7 la mweziwo chifukwa cha munthu aliyense amene walakwa komanso chifukwa cha munthu aliyense amene walakwitsa+ zinthu chifukwa chosadziwa. Anthu inu muziperekera Nyumbayi nsembe yophimba machimo.+ 21  “‘M’mwezi woyamba, pa tsiku la 14 la mweziwo, muzichita pasika.+ Muzichita chikondwerero chimenechi kwa masiku 7 ndipo muzidya mikate yopanda chofufumitsa.+ 22  Pa tsiku limeneli, mtsogoleri azipereka kwa ansembe ng’ombe yaing’ono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo ake ndi a anthu onse a m’dzikoli.+ 23  Kwa masiku 7 a chikondwererocho,+ iye azipatsa ansembe nyama zoti ziperekedwe kwa Yehova monga nsembe yopsereza yathunthu. Azipereka ng’ombe zazing’ono zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7. Nyama zimenezi zizikhala zopanda chilema ndipo azizipereka tsiku ndi tsiku kwa masiku 7.+ Aziperekanso mbuzi yamphongo tsiku ndi tsiku monga nsembe yamachimo.+ 24  Popereka ng’ombe iliyonse yaing’ono yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Popereka nkhosa iliyonse yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Pa muyezo uliwonse wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+ 25  “‘M’mwezi wa 7, pa tsiku la 15 la mweziwo, pa nthawi ya chikondwerero,+ mtsogoleri azipereka kwa wansembe zinthu zofanana ndi zimenezi kwa masiku 7.+ Azipereka nsembe yamachimo yofanana ndi imeneyi, nsembe zopsereza zathunthu zofanana ndi zimenezi, nsembe yambewu yofanana ndi imeneyi ndiponso mafuta ofanana ndi amenewa.’”

Mawu a M'munsi

“Muyezo wa efa” ndi wofanana ndi chitini chamalita 22.
Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.