Ezekieli 42:1-20

42  Munthu uja ananditengera+ kubwalo lakunja kudzera mbali ya kumpoto.+ Kumeneko anandipititsa kumdadada wa zipinda zodyeramo+ zimene zinali kutsogolo kwa mpata waukulu,+ ndiponso kumpoto kwa nyumba imene inali kumadzulo.  Kuchokera pakhomo la mbali ya kumpoto, khoma la kutsogolo kwa nyumba zodyeramo linali mikono 100 m’litali ndi mikono 50 m’lifupi.  Kuchokera pampata waukulu wa mikono 20 umene unali m’bwalo lamkati+ kukafika pamalo owaka miyala+ amene anali m’bwalo lakunja, panali nyumba ziwiri zoyang’anizana, zomwe zinali ndi zipinda zodyeramo. Nyumbazo zinali ndi mizere itatu ya zipinda zosanjikizana ndipo zipindazo zinali ndi makonde.+  Pakati pa zipinda zodyeramo panali njira yolowera mkati ya mikono 10 m’lifupi mwake.+ Panalinso kanjira ka mkono umodzi, kotuluka m’zipindazo kulowa m’njira ina ija. Makomo a zipindazo analoza mbali ya kumpoto.  Zipinda zodyeramo zam’mwamba zinali zocheperapo chifukwa chakuti makondewo anatengako malo ena a zipindazo. Zipinda zimenezi zinali zocheperapo kusiyana ndi zapakati komanso zapansi.  Zipindazo zinali m’mizere itatu yosanjikizana+ ndipo zinalibe zipilala ngati za m’mabwalo. N’chifukwa chake zipinda zam’mwamba zinali zazing’ono kusiyana ndi zipinda zapakati komanso zapansi.  Mpanda wamiyala umene unali kunja, unali pafupi ndi zipinda zodyeramo zimene zinali mbali ya kubwalo lakunja, moyang’anizana ndi zipinda zina zodyeramo. Mpandawo unali mikono 50 m’litali mwake.  Zipinda zodyeramo zimene zinali kumbali ya bwalo lakunja zinali mikono 50 m’litali mwake, ndipo zimene zinali mbali ya ku kachisi zinali mikono 100 m’litali mwake.  Kum’mawa kwa zipinda zapansi za nyumba yodyeramo, kunali khomo limene munthu anali kulowera kuchokera m’bwalo lakunja. 10  Kumbuyo kwa mpanda wamiyala wa bwalo umene unali mbali ya kum’mawa, moyang’anizana ndi mpata waukulu+ komanso nyumba imene inali kumadzulo, kunali zipinda zodyeramo.+ 11  Kutsogolo kwa zipinda zodyeramozo kunali njira yofanana ndi ya zipinda zodyeramo za mbali ya kumpoto. M’litali ndi m’lifupi mwa zipindazo munali mofanana ndi mwa zipinda za kumpoto.+ Makomo otulukira a zipindazo, kamangidwe ka zipindazo ndiponso makomo ake olowera, zinali zofanana ndi zipinda za kumpoto zija. 12  Khomo limene linali koyambirira kwa njira, linali lofanana ndi makomo a zipinda zodyeramo zimene zinali mbali ya kum’mwera. Munthu akamabwera kuzipindazo anali kudutsa m’njira imeneyi, yomwe inali m’mphepete mwa mpanda wamiyala umene unali kum’mawa.+ 13  Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Zipinda zodyeramo za kumpoto ndi za kum’mwera zimene zili moyang’anizana ndi mpata waukulu+ ndi zopatulika. M’zipinda zimenezi, ansembe otumikira+ Yehova amadyeramo zinthu zopatulika koposa.+ Mmenemo amaikamo zinthu zopatulika koposa, nsembe yambewu, nsembe yamachimo ndi nsembe ya kupalamula, chifukwa malo amenewa ndi oyera.+ 14  Ansembe akalowa m’zipindazo asamatuluke m’malo oyerawo kupita kubwalo lakunja. Akafuna kutuluka, zovala zawo zimene amavala nthawi zonse potumikira,+ azizisiya m’zipindazo chifukwa n’zopatulika. Ndiyeno azivala zovala zina+ n’kupita kumene kuli anthu.” 15  Choncho anamaliza kuyeza nyumba yamkati, ndipo ananditulutsa kudzera pachipata chimene chinayang’ana kum’mawa.+ Kenako anayeza malo onsewo. 16  Iye anayeza mbali ya kum’mawa ndi bango loyezera+ ndipo malo onsewo anakwana mabango 500. 17  Anayezanso mbali ya kumpoto ndi bango loyezera ndipo malo onsewo anakwana mabango 500. 18  Anayezanso mbali ya kum’mwera ndi bango loyezera ndipo malowo anakwana mabango 500. 19  Kenako anazungulira kupita mbali ya kumadzulo. Kumeneko anayeza malowo ndi bango loyezera ndipo anakwana mabango 500. 20  Anayeza malo onsewo mbali zonse zinayi. Malo onsewo anali ndi mpanda+ wokwana mabango 500 m’litali ndi mabango 500 m’lifupi mwake.+ Mpandawo unali kusiyanitsa zinthu zopatulika ndi zinthu zodetsedwa.+

Mawu a M'munsi