Ezekieli 40:1-49

40  M’chaka cha 25 kuchokera pamene tinatengedwa kupita ku ukapolo,+ kuchiyambi kwa chakacho, pa tsiku la 10 la mwezi woyamba, m’chaka cha 14 kuchokera pamene mzinda unawonongedwa,+ pa tsiku limeneli dzanja la Yehova linandikhudza,+ ndipo iye ananditengera kumalo enaake.+  M’masomphenya a Mulungu, iye ananditengera m’dziko la Isiraeli ndi kundikhazika paphiri lalitali kwambiri.+ Mbali ya kum’mwera paphiripo panali chinachake chooneka ngati mzinda.+  Kenako ananditengera kumeneko ndipo ndinaonako munthu wamwamuna. Munthuyo anali kuoneka wonyezimira ngati mkuwa.+ M’manja mwake munali chingwe cha fulakesi* ndi bango loyezera,+ ndipo anaima pachipata.  Tsopano munthuyo anayamba kulankhula nane kuti: “Iwe mwana wa munthu,+ ona ndi maso ako, imva ndi makutu ako, ndipo uike mtima wako pa zonse zimene ndikuonetse, chifukwa wabweretsedwa kuno kuti ine ndikuonetse zinthu zimenezi. Ukauze nyumba ya Isiraeli zonse zimene uone kuno.”+  Ndiyeno ndinaona kuti panali nyumba yomwe inali ndi mpanda wozungulira nyumba yonseyo. M’manja mwa munthu uja munali bango loyezera. Bangolo linali lalitali kukwana mikono* 6 potengera muyezo wa mkono ndi chikhatho. Tsopano munthuyo anayamba kuyeza mpandawo, ndipo anapeza kuti unali wochindikala bango limodzi komanso kuchokera pansi kupita m’mwamba unali wautali bango limodzi.  Kenako anafika pachipata chimene chinayang’ana kum’mawa+ ndipo anakwera pamasitepe ake. Pamenepo iye anayamba kuyeza malo apafupi ndi khomo la kanyumba ka pachipatako+ ndipo anapeza kuti malowo anali bango limodzi m’lifupi. Malo apafupi ndi khomo la mbali ina ya kanyumbako analinso bango limodzi m’lifupi mwake.  Chipinda cha alonda chinali bango limodzi m’litali ndi bango limodzi m’lifupi. Kuchokera pachipinda cha alonda kukafika pachipinda china cha alonda+ panali mikono isanu. Malo apafupi ndi khomo la kanyumbako, pafupi ndi khonde lamkati anali bango limodzi.  Ndiyeno anayeza khonde la kanyumbako loyang’ana kubwalo lakunja, ndipo anapeza kuti linali bango limodzi.+  Anayeza khonde la kanyumba ka pachipata n’kupeza kuti linali mikono 8. Zipilala zake zam’mbali zinali mikono iwiri. Khonde la kanyumbako linali loyang’ana kubwalo lakunja. 10  Zipinda za alonda za pachipata cha kum’mawa zinalipo zitatu mbali iyi ndi zitatu mbali inayo. Miyezo ya zipinda zitatuzo inali yofanana, ndipo zipilala zam’mbali zinalinso zofanana, mbali iyi ndi mbali inayo. 11  Kenako anayeza m’lifupi mwa malo apafupi ndi khomo la kanyumba ka pachipata n’kupeza mikono 10. Anayezanso m’litali mwa chipata n’kupeza mikono 13. 12  Malo otchinga ndi mpanda, kutsogolo kwa zipinda za alonda, anali mkono umodzi. Kumbali zonse kunali malo otchinga ndi mpanda okwana mkono umodzi. Chipinda chilichonse cha alonda chinali mikono 6 mbali iyi ndiponso mikono 6 mbali inayo. 13  Iye anapitiriza kuyeza kanyumba ka pachipatako kuchokera padenga* la chipinda chimodzi cha alonda kukafika padenga la chipinda china cha alonda ndipo anapeza mikono 25.+ Khomo la chipinda cha alonda cha mbali iyi linali moyang’anizana ndi khomo la chipinda cha mbali inayo. 14  Kenako anayeza zipilala zam’mbali ndipo anapeza kuti zinali zazitali mikono 60 kuchokera pansi kupita m’mwamba. Zipilala zam’mbalizo zinali zoyang’ana kubwalo, m’zipata zonse. 15  Kuchokera kutsogolo kwa khomo lakunja la kanyumba ka pachipata, kukafika kutsogolo kwa khonde limene linali kukhomo lamkati la kanyumbako, panali mikono 50. 16  Zipinda za alondazo komanso zipilala zimene zinali m’mbali mwa zipindazo zinali ndi mawindo okhala ndi mafelemu aakulu mkati koma aang’ono kunja+ kuzungulira kanyumba konseko. Umu ndi mmenenso zinalili ndi mawindo apakhonde. Mkati mwa kanyumbako munali mawindo aakulu mkati, kuzungulira mbali zonse ndipo pazipilala zam’mbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza.+ 17  Kenako anandipititsa kubwalo lakunja. Kumeneko ndinaona zipinda zodyeramo+ ndipo pansi pa bwalo lonselo panali powaka miyala. Pabwalo lowaka miyalalo panali zipinda zodyeramo zokwana 30.+ 18  M’lifupi mwa malo owaka miyala am’mbali mwa tinyumba ta zipata munali mofanana ndendende ndi m’litali mwa tinyumbato. Amenewa anali malo owaka miyala a m’munsi. 19  Munthu uja anapitiriza kuyeza kuchokera kutsogolo kwa kanyumba ka pachipata cha m’munsi kukafika kutsogolo kwa bwalo lamkati. Malo amenewa anali mikono 100, kum’mawa ndi kumpoto. 20  Bwalo lakunja linali ndi kanyumba ka pachipata kamene kanayang’ana kumpoto. Iye anayeza m’litali ndi m’lifupi mwake. 21  Zipinda zake za alonda zinali zitatu mbali iyi ndiponso zitatu mbali inayo. Miyezo ya zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake, inali yofanana ndi miyezo ya kanyumba ka pachipata choyamba chija. M’litali mwake kanali mikono 50 ndipo m’lifupi mwake kanali mikono 25. 22  Miyezo ya mawindo ake, khonde lake ndi zithunzi zake za mtengo wa kanjedza,+ inali yofanana ndi miyezo ya zinthu zomwezi za kanyumba ka pachipata kamene kanayang’ana kum’mawa. Anthu akafuna kulowa m’kanyumbako anali kukwera masitepe 7, ndipo khonde lake linali kutsogolo kwa anthuwo. 23  Chipata cha bwalo lamkati chinayang’anizana ndi chipata cha kumpoto. Chipata cha kum’mawa cha bwalo lamkati nachonso chinayang’anizana ndi chipata cha kum’mawa. Munthu uja anayezanso mikono 100 kuchokera pachipata kukafika pachipata china. 24  Kenako ananditengera kumbali ya kum’mwera. Kumeneko ndinaonakonso kanyumba ka pachipata kamene kanayang’ana kum’mwera.+ Iye anayeza zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake ndipo miyezo yake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba ta zipata zina zija. 25  Kanyumba ka pachipata kameneka ndi khonde lake zinali ndi mawindo ofanana ndi a tinyumba ta zipata zina zija kuzungulira kanyumbako. M’litali, kanyumbako kanali mikono 50 ndipo m’lifupi kanali mikono 25. 26  Kanyumba kameneka kanali ndi masitepe 7 okwerera m’chipatacho,+ ndipo kutsogolo kwawo kunali khonde. Pazipilala zimene zinali m’mbali mwa khondelo, chimodzi mbali iyi ndi china mbali inayo, panali zithunzi za mtengo wa kanjedza. 27  Bwalo lamkati linali ndi chipata kumbali ya kum’mwera. Ndipo iye anayeza kuchokera pachipata kulowera kum’mwera kukafika pachipata china. Mtunda umenewo unakwana mikono 100. 28  Kenako ananditengera m’bwalo lamkati kudzera pachipata cha kum’mwera. Munthu uja anayeza kanyumba ka pachipata cha kum’mwera ndipo miyezo yake inali yofanana ndi tinyumba tina tija. 29  Miyezo ya zipinda za alonda za kanyumba ka pachipatako, zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba tina tija. Kanyumba ka pachipata konseko ndi khonde lake zinali ndi mawindo. M’litali mwake kanyumba kameneka kanali mikono 50 ndipo m’lifupi mwake kanali mikono 25.+ 30  Tinyumba tonse ta zipata zolowera m’bwalo lamkati tinali ndi khonde. M’litali mwake khondelo linali mikono 25 ndipo m’lifupi linali mikono isanu. 31  Khonde lake linayang’ana kubwalo lakunja. Pazipilala zake zam’mbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza+ ndipo masitepe olowera m’kanyumba ka pachipatako analipo 8.+ 32  Kenako ananditengera m’bwalo lamkati kudzera mbali ya kum’mawa. Kumeneko iye anayeza kanyumba ka pachipatako ndipo miyezo yake inali yofanana ndi tinyumba tina tija. 33  Miyezo ya zipinda za alonda za kanyumba ka pachipatako, zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba tina tija. Kanyumba ka pachipata konseko ndi khonde lake zinali ndi mawindo. M’litali mwake, kanyumba kameneka kanali mikono 50 ndipo m’lifupi mwake kanali mikono 25. 34  Khonde lake linayang’ana kubwalo lakunja. Pazipilala zake zam’mbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza kumbali iyi ndi kumbali inayo, ndipo masitepe olowera m’kanyumba ka pachipatako analipo 8. 35  Kenako ananditengera kuchipata cha kumpoto.+ Kumeneko iye anayeza kanyumba ka pachipatako ndipo miyezo yake inali yofanana ndi tinyumba tina tija.+ 36  Iye anayeza zipinda za alonda, zipilala zake zam’mbali ndi khonde lake. Kanyumba ka pachipata konseko kanali ndi mawindo. M’litali mwake, kanyumba kameneka kanali mikono 50 ndipo m’lifupi mwake kanali mikono 25. 37  Zipilala zake zam’mbali zinayang’ana kubwalo lakunja. Pazipilala zam’mbalizo panali zithunzi za mtengo wa kanjedza kumbali iyi ndi kumbali inayo.+ Masitepe olowera m’kanyumba ka pachipatako analipo 8. 38  Pafupi ndi zipilala zam’mbali mwa tinyumba ta zipatazo panali chipinda chodyeramo. Kumeneko n’kumene anali kutsukira nsembe yopsereza yathunthu.+ 39  Pakhonde la kanyumba ka pachipatako panali matebulo awiri kumbali iyi ndi matebulo ena awiri kumbali inayo. Pamatebulowo anali kupherapo nsembe yopsereza yathunthu,+ nsembe yamachimo+ ndi nsembe ya kupalamula.+ 40  Kunja kwa kanyumba ka pachipata cha mbali ya kumpoto, kukhomo lolowera m’kanyumbako, kunali matebulo awiri. Kumbali inayo, pafupi ndi khonde la kanyumbako, kunalinso matebulo awiri. 41  Kunja kwa kanyumba ka pachipatako kunali matebulo anayi ndipo mkati mwa kanyumbako munalinso matebulo anayi. Matebulo onse amene anali kupherapo nyama analipo 8. 42  Matebulo anayi a nsembe zopsereza zathunthuwo anali amiyala yosema. M’litali mwake anali mkono umodzi ndi hafu, m’lifupi mwake anali mkono umodzi ndi hafu ndipo kuchokera pansi kufika pamwamba anali aatali mkono umodzi. Pamatebulo amenewa analinso kuikapo zida zophera nyama ya nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina. 43  Mashelefu oikamo katundu anali chikhatho chimodzi m’lifupi mwawo. Mashelefuwo anawaika kuzungulira khoma lonse lamkati ndipo anawalimbitsa kwambiri. Pamatebulo aja anali kuikapo nyama ya nsembe yoperekedwa monga mphatso.+ 44  Kunja kwa kanyumba ka pachipata chamkati kunali zipinda zodyeramo oimba.+ Zipinda zimenezi zinali m’bwalo lamkati kumbali ya chipata cha kumpoto. Zipindazo zinayang’ana kum’mwera. Chipinda chimodzi chinali mbali ya kuchipata cha kum’mawa, ndipo chinayang’ana kumpoto. 45  Pamenepo munthu uja anandiuza kuti: “Chipinda chodyeramo ichi, chimene chayang’ana kum’mwera, ndi cha ansembe amene akutumikira panyumbayi.+ 46  Chipinda chodyeramo chimene chayang’ana kumpoto ndi cha ansembe ogwira ntchito paguwa lansembe,+ omwe ndi ana a Zadoki.+ Iwo ndi ochokera mwa ana a Levi ndipo amayandikira Yehova ndi kum’tumikira.”+ 47  Munthu uja anayezanso bwalo lamkati. Iye anapeza kuti m’litali mwake, linali mikono 100 ndipo m’lifupi linalinso mikono 100. Bwalolo linali lofanana mbali zonse zinayi. Kutsogolo kwa nyumbayo kunali guwa lansembe. 48  Kenako ananditengera pakhonde la nyumbayo.+ Pamenepo anayeza chipilala cham’mbali cha khondelo ndipo anapeza kuti chinali mikono isanu mbali iyi ndi mikono isanu mbali inayo. M’lifupi mwa khomo la nyumbayo munali mikono itatu mbali iyi ndi mikono itatu mbali inayo. 49  Khonde la nyumbayo linali mikono 20 m’litali mwake ndi mikono 11 m’lifupi. Kuti munthu afike pakhondepo anali kukwera masitepe. Pafupi ndi zipilala zam’mbalizo panali nsanamira, imodzi mbali iyi, ina mbali inayo.+

Mawu a M'munsi

“Fulakesi” ndi mbewu imene anali kulima ku Iguputo. Anali kuigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu, ndipo “chikhatho” chinali masentimita 7.4. Kuphatikiza zimenezi zimakwana pafupifupi masentimita 51.8 ndipo zimaimira muyezo wotchedwa “mkono wautali.” Choncho bango loyezera la mikono 6 linali lalitali mamita 3.11.
Kapena kuti “patsindwi.”