Ezekieli 39:1-29

39  “Iwe mwana wa munthu, losera zoipa zimene zidzachitikire Gogi.+ Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndithana nawe iwe Gogi, mtsogoleri wamkulu wa Meseke+ ndi Tubala.+  Ndidzakubweza ndi kukutsogolera.+ Ndidzakutenga kuchokera kumadera akutali kwambiri a kumpoto,+ n’kukubweretsa kumapiri a ku Isiraeli.  Ndidzakuphumitsa uta m’dzanja lako lamanzere, ndipo ndidzachititsa kuti mivi yako igwe pansi kuchoka m’dzanja lako lamanja.  Iwe udzafera m’mapiri a ku Isiraeli+ limodzi ndi magulu ako onse a asilikali ndi anthu a mitundu ina amene adzakhale nawe. Ndidzakuperekani kwa mbalame zodya nyama, mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zakutchire kuti mukhale chakudya chawo.”’+  “‘Iweyo udzagwera panthaka,+ pakuti ine ndanena zimenezi,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.  “‘Ndidzatumiza moto ku Magogi+ ndi kwa anthu amene akukhala mwabata m’zilumba,+ ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.  Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Aisiraeli. Sindidzalolanso kuti dzina langa lidetsedwe,+ ndipo mitundu ina ya anthu idzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ Woyera wa ku Isiraeli.’+  “‘Tamvera! Zimene ulosiwu ukunena zidzachitika ndipo zidzakwaniritsidwa,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Ine ndakhala ndikunena za tsiku limenelo.+  Anthu okhala m’mizinda ya Isiraeli adzakoleza moto pogwiritsa ntchito zida zankhondo. Zida zake ndizo zishango zazing’ono, zishango zazikulu, mauta, mivi, zobayira ndi mikondo ing’onoing’ono. Adzakoleza moto+ pogwiritsa ntchito zida zimenezi kwa zaka 7. 10  Iwo sadzanyamula mitengo kutchire kapena kutola nkhuni kunkhalango, chifukwa chakuti adzakoleza moto pogwiritsa ntchito zida zankhondozo.’ “‘Adzalanda zinthu za anthu amene anali kuwalanda zinthu zawo,+ ndipo adzatenga katundu wa anthu amene anali kutenga katundu wawo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 11  “‘Pa tsiku limenelo Gogi+ ndidzam’patsa malo kuti akhale manda ake mu Isiraeli. Ndidzam’patsa chigwa cha kum’mawa kwa nyanja, chomwe ndi chigwa cha anthu ongodutsa. Chigwacho chidzatseka njira ya anthu ongodutsawo. Kumeneko iwo adzaika m’manda Gogi pamodzi ndi khamu lake lonse, ndipo adzatcha chigwacho kuti Chigwa cha Khamu la Gogi.+ 12  Kwa miyezi 7, a nyumba ya Isiraeli adzakhala akuika m’manda Gogi ndi khamu lake kuti ayeretse dzikolo.+ 13  Anthu onse a m’dzikolo adzagwira ntchito yofotsera mitembo. Iwo adzatchuka chifukwa cha ntchito imeneyi pa tsiku limene ine ndidzalemekezeke,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 14  “‘Padzakhala amuna amene azidzagwira ntchito nthawi zonse. Iwo azidzayenda m’dzikolo n’kumafotsera mitembo pamodzi ndi anthu ongodutsa. Amenewa azidzakwirira mitembo yotsalira pamtunda. Adzachita zimenezi kuti ayeretse dziko lapansi. Iwo adzakhala akufunafuna mitembo kwa miyezi 7. 15  Anthu ongodutsa akamadzadutsa m’dzikolo, wina n’kuona fupa la munthu, azidzaikapo chizindikiro mpaka anthu ofotsera aja atakafotsera fupalo m’Chigwa cha Khamu la Gogi.+ 16  Kumeneko kudzakhala mzinda wotchedwanso Hamona, ndipo anthu adzayeretsa dzikolo.’+ 17  “Koma kwa iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Uza mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zonse zakutchire+ kuti: “Sonkhanani mubwere kuno. Sonkhanani pamodzi kuzungulira nsembe yanga imene ndikukuperekerani. Imeneyi ndi nsembe yaikulu m’mapiri a ku Isiraeli.+ Mukabwera mudzadya nyama ndi kumwa magazi.+ 18  Mudzadya mnofu wa anthu amphamvu,+ mudzamwa magazi a atsogoleri a dziko lapansi, nkhosa zamphongo, ana a nkhosa amphongo,+ mbuzi zamphongo ndi ng’ombe zamphongo.+ Zonsezi ndi nyama zonenepa za ku Basana.+ 19  Inu mudzadya mafuta ndi kukhuta,+ ndipo mudzamwa magazi mpaka kuledzera nawo. Zimenezi zidzachokera pa nsembe yanga imene ndidzakuperekereni.”’ 20  “‘Inu mudzakhuta patebulo langa. Mudzadya nyama ya mahatchi, ya okwera magaleta, ya anthu amphamvu ndi ankhondo a mitundu yosiyanasiyana,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 21  “‘Ndidzasonyeza ulemerero wanga pakati pa mitundu ya anthu. Mitundu yonse ya anthu idzaona chiweruzo chimene ndidzapereke+ ndiponso mphamvu za dzanja langa.+ 22  Kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo, a nyumba ya Isiraeli adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Mulungu wawo.+ 23  Anthu a mitundu ina adzadziwa kuti a nyumba ya Isiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo chifukwa cha zolakwa zawo.+ Adzadziwa kuti anali kundichitira zinthu zosakhulupirika. N’chifukwa chake ine ndinawabisira nkhope yanga+ n’kuwapereka m’manja mwa adani awo ndipo onsewo anaphedwa ndi lupanga.+ 24  Ndinawachitira zinthu mogwirizana ndi zonyansa zimene anachita komanso chifukwa chakuti anaphwanya malamulo,+ moti ndinawabisira nkhope yanga.’ 25  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Tsopano ndibweretsa ana a Yakobo omwe anatengedwa kupita kumayiko ena,+ ndipo ndichitira chifundo nyumba yonse ya Isiraeli.+ Nditeteza dzina langa loyera kuti lisadetsedwe.*+ 26  Akadzakhala m’dziko lawo mwabata+ popanda wowaopsa,+ adzakhala atachita manyazi mokwanira+ chifukwa cha zinthu zonse zosakhulupirika zimene anandichitira.+ 27  Ndikadzawabweretsa kuchokera ku mitundu ina ya anthu ndi kuwasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumayiko a adani awo,+ ndidzadziyeretsa pakati pawo pamaso pa mitundu yambiri ya anthu.’+ 28  “‘Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo, ndikadzawapititsa kumayiko ena n’kuwabwezanso kudziko lawo onse pamodzi.+ Kumayikowo ndidzatengako Aisiraeli onse moti sindidzasiyako aliyense.+ 29  Sindidzawabisiranso nkhope yanga+ chifukwa panyumba ya Isiraeli, ndidzatsanulirapo mzimu wanga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Ndidzadzipereka kwambiri chifukwa cha dzina langa loyera.”