Ezekieli 38:1-23

38  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu,+ yang’ana Gogi wa kudziko la Magogi,+ mtsogoleri wamkulu wa Meseke+ ndi Tubala,+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzam’chitikire.  Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndithana nawe iwe Gogi, mtsogoleri wamkulu wa Meseke ndi Tubala.  Ndithu ine ndidzakubweza n’kukukola chibwano ndi ngowe.+ Kenako ndidzakukokera pafupi limodzi ndi gulu lako lonse lankhondo,+ mahatchi ako ndi asilikali ako okwera pamahatchi. Asilikali onsewa ndi ovala mwaulemerero.+ Iwo ndi khamu lalikulu lonyamula zishango zazikulu ndi zazing’ono, ndipo onsewo ndi aluso lomenya nkhondo pogwiritsa ntchito malupanga.+  Udzabwera pamodzi ndi asilikali a ku Perisiya,+ Itiyopiya+ ndi Puti.+ Onsewa adzanyamula zishango zazing’ono ndipo adzavala zisoti.  Udzabweranso ndi Gomeri+ ndi magulu ake onse a asilikali, komanso ndi ana a Togarima+ ochokera kumadera akutali kwambiri a kumpoto. Iwo adzabwera ndi magulu awo onse a asilikali. Chotero iwe udzabwera ndi mitundu yambiri ya anthu.+  “‘“Konzeka, iwe ndi khamu lako lonse+ limene lasonkhana kwa iwe. Nonse mukhale okonzeka ndipo iwe ukhale mtsogoleri wawo.  “‘“Pakapita masiku ambiri, ine ndidzatembenukira kwa iwe. Pakatha zaka zambiri, iwe udzapita kudziko+ la anthu amene anapulumutsidwa ku lupanga ndi kubwerera kwawo. Udzapita kudziko la anthu amene anasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera ku mitundu ina ya anthu+ n’kukakhala kumapiri a ku Isiraeli. Dziko lawo linali kuwonongedwa nthawi zonse ndipo tsopano muli anthu amene anachokera m’mayiko a anthu a mitundu ina. Onsewo akukhala m’dzikoli mwabata.+  Iwe udzabwera m’dzikolo ngati mphepo yamkuntho.+ Iweyo, magulu ako onse a asilikali, pamodzi ndi anthu ambiri a mitundu ina, mudzaphimba dzikolo ngati mitambo.”’+ 10  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsikulo maganizo adzakubwerera mumtima mwako+ ndipo udzaganiza zochita chiwembu choipa kwambiri.+ 11  Udzanena kuti: “Ndipita kukaukira dziko lokhala ndi midzi yopanda mipanda.+ Ndipita kukaukira anthu amene akukhala mwabata, popanda chowasokoneza. Ndikaukira anthu onsewo amene akukhala m’midzi yopanda mipanda+ ndipo alibe zotsekera ndiponso zitseko.” 12  Udzapita kumeneko kuti ukalande+ ndi kutengako zinthu zambiri, ndiponso kuti ukaukire dziko lowonongedwa limene tsopano mukukhala anthu.+ Udzapita kukaukira anthu amene anasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera ku mitundu ina,+ amene akusonkhanitsa chuma ndi katundu,+ komanso amene akukhala pakatikati+ pa dziko lapansi. 13  “‘Sheba,+ Dedani,+ amalonda a ku Tarisi+ ndi mikango yawo yonse yamphamvu+ adzakufunsa kuti: “Kodi wasonkhanitsa khamu lako kuti udzalande zinthu zambiri? Kodi ukufuna kudzatenga siliva, golide, chuma ndi katundu?”’ 14  “Chotero losera, iwe mwana wa munthu, ndipo uuze Gogi kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Anthu anga Aisiraeli akamadzakhala mwabata, ndithu iwe udzadziwa zimenezo.+ 15  Udzabwera kuchokera kumalo ako, kumadera akutali a kumpoto.+ Udzabwera ndi mitundu yambiri ya anthu. Anthuwo adzakhala khamu lalikulu, adzakhala chigulu chachikulu chankhondo. Onsewo adzabwera atakwera pamahatchi.+ 16  Ndithu iwe udzabwera ngati mitambo kudzaphimba dzikolo ndi kudzaukira anthu anga Aisiraeli.+ Zimenezi zidzachitika m’masiku otsiriza, ndipo ine ndidzakubweretsa kuti uukire dziko langa.+ Ndidzachita izi kuti anthu a mitundu ina adzandidziwe pamene ndidzadziyeretse pamaso pawo, kudzera mwa iwe Gogi.”’+ 17  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Kodi iwe ndiwe+ yemwe uja amene ndinkakunena kale kudzera mwa atumiki anga, aneneri a Isiraeli? Aneneriwo ankalosera chaka ndi chaka m’masiku amenewo kuti ndidzakutumiza kwa iwo kuti ukawaukire.’+ 18  “‘Pa tsiku limenelo, tsiku limene Gogi adzabwere m’dziko la Isiraeli, mkwiyo wanga udzatulukira m’mphuno mwanga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 19  ‘Ine ndidzalankhula mwaukali wanga+ woyaka moto komanso nditakwiya kwambiri.+ Ndithudi, pa tsikulo m’dziko la Isiraeli mudzachitika chivomezi chachikulu.+ 20  Chifukwa cha ine, nsomba zam’nyanja, zolengedwa zouluka zam’mlengalenga, zilombo zakutchire, zokwawa zonse zimene zimakwawa panthaka ndiponso anthu onse amene ali padziko lapansi, adzanjenjemera.+ Mapiri adzagwetsedwa,+ misewu yotsetsereka idzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi.’ 21  “‘Ndidzamubweretsera lupanga m’madera anga onse a m’mapiri kuti limuwononge,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ ‘Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.+ 22  Ine ndidzamuweruza+ ndi mliri+ ndiponso magazi.+ Ndidzamugwetsera mvula yamphamvu, matalala,+ moto+ ndi sulufule. Ndidzagwetsa zimenezi pa iyeyo, pagulu lake la asilikali ndi pa mitundu yambiri ya anthu amene adzakhale kumbali yake.+ 23  Ndidzadzilemekeza, kudziyeretsa+ ndi kuchititsa kuti mitundu yambiri ya anthu indidziwe, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+

Mawu a M'munsi