Ezekieli 37:1-28
37 Dzanja la Yehova linali pa ine+ moti mzimu wa Yehova unanditenga+ ndi kukandikhazika m’chigwa mmene munali mafupa okhaokha.+
2 Iye anandiyendetsa m’chigwamo kuti ndione mafupa onsewo. Ndinaona kuti m’chigwamo munali mafupa ambiri ndipo anali ouma kwambiri.+
3 Ndiyeno anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa awa angakhale ndi moyo?” Pamenepo ndinayankha kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndinu amene mukudziwa bwino zimenezo.”+
4 Ndiyeno anandiuza kuti: “Losera zokhudza mafupa amenewa ndipo uwauze kuti, ‘Inu mafupa ouma, imvani mawu a Yehova:
5 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mafupa awa kuti: “Ndiika mpweya mwa inu ndipo mukhala amoyo.+
6 Ndidzakuikirani mitsempha ndi kukupatsani mnofu. Ndidzakukutani ndi khungu ndi kuika mpweya mwa inu ndipo mudzakhala ndi moyo.+ Choncho mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+
7 Ine ndinalosera mmene anandiuzira.+ Pamene ndinali kulosera, panayamba kumveka phokoso la mafupa kuti gobedegobede! Pa nthawiyo mafupawo anali kubwera pamodzi n’kumalumikizana.
8 Kenako ndinangoona mitsempha ndi mnofu zitakuta mafupawo ndipo khungu linabwera pamwamba pake. Koma m’mafupawo munalibe mpweya.
9 Tsopano anandiuza kuti: “Losera kwa mphepo. Iwe mwana wa munthu, losera ndipo uuze mphepoyo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe mphepo! Bwera kuchokera kumbali zonse zinayi ndi kuwomba anthu ophedwawa+ kuti akhalenso ndi moyo.”’”+
10 Pamenepo ndinalosera monga mmene anandiuzira ndipo mpweya unalowa mwa anthuwo. Iwo anakhala ndi moyo ndipo anaimirira.+ Anali khamu lalikulu la gulu lankhondo.
11 Iye anandiuzanso kuti: “Iwe mwana wa munthu, mafupawa akuimira nyumba yonse ya Isiraeli.+ Iwo akunena kuti, ‘Mafupa athu auma ndipo tilibenso chiyembekezo chilichonse.+ Atilekanitsa ndi anzathu ndipo tili kwatokhatokha.’
12 Choncho losera, uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzatsegula manda anu,+ inu anthu anga, ndipo ndidzakutulutsani m’mandamo ndi kukubweretsani m’dziko la Isiraeli.+
13 Inu anthu anga, ine ndikadzatsegula manda anu n’kukutulutsani m’mandamo, mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’+
14 ‘Ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhala amoyo.+ Ndidzakukhazikani m’dziko lanu ndipo mudzadziwa kuti ine Yehova ndinanena zimenezi ndipo ndazichita,’ watero Yehova.”+
15 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:
16 “Koma iwe mwana wa munthu, tenga ndodo+ ndi kulembapo kuti, ‘Ndodo ya Yuda ndi anzake, ana a Isiraeli.’+ Utengenso ndodo ina ndi kulembapo kuti, ‘Ndodo ya Yosefe yoimira Efuraimu+ komanso anzawo onse a nyumba ya Isiraeli.’+
17 Ndiyeno uziike pamodzi kuti zikhale ndodo imodzi. Chotero ndodozo zidzakhala ndodo imodzi m’dzanja lako.+
18 Anthu a mtundu wako akayamba kukufunsa kuti, ‘Kodi sutiuza kuti zinthu izi zikutanthauza chiyani?’+
19 Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga ndodo ya Yosefe imene ili m’dzanja la Efuraimu. Ndodo imeneyi ikuimiranso mafuko a Isiraeli omwe ndi anzake a Efuraimu. Ndidzaika mafukowo pandodo ya Yuda ndipo ndodo ziwirizo zidzakhala ndodo imodzi.+ Ndodozo zidzakhala ndodo imodzi m’dzanja langa.”’
20 Ndodo zimene wazilembazo zikhale m’dzanja lako pamaso pawo.+
21 “Uwauzenso kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga ana a Isiraeli kuchokera pakati pa mitundu ina ya anthu kumene anapita. Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko owazungulira ndipo ndidzawabweretsa m’dziko lawo.+
22 Ndidzawaphatikiza kuti akhale mtundu umodzi m’dzikolo,+ m’mapiri a Isiraeli. Onsewo adzakhala ndi mfumu imodzi+ ndipo sadzakhalanso mitundu iwiri kapena kugawanika kukhala maufumu awiri.+
23 Iwo sadzadziipitsanso ndi mafano awo onyansa, zinthu zawo zonyansa ndi zochita zawo zonse zophwanya malamulo.+ Ndidzawapulumutsa ku machimo onse amene anali kuchita m’malo awo okhala, ndipo ndidzawayeretsa.+ Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.+
24 “‘“Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo.+ Onse adzakhala ndi m’busa mmodzi.+ Iwo adzayenda motsatira zigamulo zanga+ ndipo adzasunga malamulo anga+ ndi kuwatsatira.+
25 Anthu amenewa adzakhala m’dziko limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu anakhalamo.+ Adzakhala m’dzikomo+ pamodzi ndi ana awo ndiponso zidzukulu zawo mpaka kalekale.+ Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wawo mpaka kalekale.+
26 “‘“Ndidzachita nawo pangano la mtendere,+ moti adzakhala m’pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale.+ Ine ndidzawakhazikitsa m’dzikolo, ndidzawachulukitsa+ ndipo ndidzakhazikitsa malo anga opatulika pakati pawo mpaka kalekale.+
27 Iwo adzakhala muhema wanga.+ Ine ndidzakhaladi Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.+
28 Malo anga opatulika akadzakhala pakati pawo mpaka kalekale, mitundu ina ya anthu idzadziwa kuti ine Yehova+ ndikuyeretsa Isiraeli.”’”+