Ezekieli 35:1-15

35  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, yang’ana+ kudera lamapiri la Seiri+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzachitikire deralo.+  Uuze deralo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe dera lamapiri la Seiri,+ ine ndithana nawe. Nditambasula dzanja langa ndi kukukhaulitsa.+ Ndikusandutsa bwinja ndiponso malo owonongeka.+  Mizinda yako ndidzaisandutsa malo owonongeka ndipo iweyo ndidzakusandutsa bwinja.+ Udzadziwa kuti ine ndine Yehova,+  chifukwa chakuti unali ndi chidani chosatha+ ndi ana a Isiraeli ndipo unali kuwapha ndi lupanga.+ Unachita zimenezi pa nthawi ya tsoka lawo,+ pamene zolakwa zawo zinafika kumapeto.”’+  “‘Chotero pali ine Mulungu wamoyo, mlandu wa magazi udzakutsatira chifukwa ndinakonza zoti magazi ako akhetsedwe,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Ndithudi iwe unadana ndi amene unakhetsa magazi awo, choncho mlandu wa magazi udzakutsatira.+  Dera lamapiri la Seiri ndidzalisandutsa bwinja ndiponso malo owonongeka.+ Kumeneko sikudzapezeka aliyense wodutsako.+  M’mapirimo ndidzadzazamo anthu ophedwa. M’zitunda zako, m’zigwa zako ndi m’mitsinje yako yonse, mudzadzaza anthu ophedwa ndi lupanga.+  Ndidzakusandutsa malo omwe adzakhale owonongeka mpaka kalekale. M’mizinda yako simudzakhalanso anthu,+ ndipo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+ 10  “Iwe unanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi mayiko awiri awa zidzakhala zanga ndipo ife tidzatenga mayiko awiri onsewo.’+ Unanena zimenezi ngakhale kuti Yehova anali komweko.+ 11  ‘Chotero pali ine Mulungu wamoyo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘Ndidzachitapo kanthu mogwirizana ndi mkwiyo wako ndi nsanje imene unaisonyeza chifukwa chakuti unali kudana nawo,+ ndipo ndikadzakuweruza, iwo adzandidziwa.+ 12  Iwe udzadziwa kuti ine Yehova, ndinamva mawu onse achipongwe amene unanenera mapiri a ku Isiraeli.+ Pakuti iwe unanena kuti: “Mapiri aja awonongedwa. Aperekedwa kwa ife kuti akhale chakudya chathu.”+ 13  Anthu inu munalankhula modzitama kwa ine ndi pakamwa panu.+ Munachulukitsa mawu anu ondinyoza+ ndipo ineyo ndinamva mawuwo.’+ 14  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa nthawi imene dziko lonse lapansi lizidzasangalala, ine ndidzakusandutsa malo owonongeka. 15  Pakuti unali kusangalala chifukwa chakuti cholowa cha nyumba ya Isiraeli chinawonongedwa, ine ndidzachitanso chimodzimodzi kwa iwe.+ Iwe dera lamapiri la Seiri ndiponso Edomu yense, mudzasanduka bwinja,+ ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+

Mawu a M'munsi