Ezekieli 34:1-31

34  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, losera zoipa zimene zidzachitikire abusa a Isiraeli. Losera, ndipo uuze abusawo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka abusa a Isiraeli,+ amene akungodzidyetsa okha!+ Kodi abusa ntchito yawo si kudyetsa nkhosa?+  Inu mukudya mafuta,+ ndipo mukuvala zovala zaubweya wa nkhosa. Mukupha+ nyama zonenepa,+ koma nkhosa simukuzidyetsa.  Nkhosa zodwala simunazilimbitse+ ndipo zamatenda simunazichiritse. Yothyoka mwendo simunaimange mwendo wothyokawo. Nkhosa zomwazika simunazibweze ndipo zosochera simunazifufuze kuti muzipeze.+ Munali kuzilamulira mouma mtima komanso mwankhanza.+  Pang’ono ndi pang’ono zinamwazikana chifukwa chakuti zinalibe m’busa.+ Choncho zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakutchire ndipo zinapitiriza kumwazikana.+  Nkhosa zanga+ zinasochera m’mapiri onse ndi m’zitunda zonse zitalizitali.+ Zinabalalika padziko lonse lapansi, ndipo panalibe wozifufuza ndi kuziyang’anayang’ana.  “‘“Choncho abusa inu, imvani mawu a Yehova.  ‘“Pali ine Mulungu wamoyo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, “nkhosa zanga zinali kungobedwa ndipo zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakutchire. Nkhosa zanga zinalibe m’busa, ndipo abusa anga sanazifunefune koma anali kumangodzidyetsa okha,+ osadyetsa nkhosa zanga.”’  Chotero abusa inu, imvani mawu a Yehova. 10  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi ine ndilanga abusawo.+ Ndiwauza kuti andibwezere nkhosa zanga ndipo ndiwaletsa kudyetsa nkhosa zangazo.+ Abusawo sadzadzidyetsanso okha.+ Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwawo ndipo sizidzakhalanso chakudya chawo.’”+ 11  “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.+ 12  Ndidzasamalira nkhosa zanga ngati mmene amachitira munthu amene amadyetsa gulu la nkhosa+ zake pamene ali pakati pa nkhosa zimene zinabalalika.+ Pa tsiku la mitambo ndi mdima wandiweyani, ndidzapulumutsa nkhosazo kuchokera m’malo onse kumene zinabalalikira.+ 13  Nkhosa zanga ndidzazitulutsa+ pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzazisonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko ena ndi kuzibweretsa m’dziko lawo.+ Ndidzazidyetsa m’mapiri a ku Isiraeli, m’mphepete mwa mitsinje komanso m’malo onse a m’dzikolo okhalako anthu.+ 14  Nkhosazo ndidzazidyetsera m’malo a msipu wabwino ndipo zizidzakhala m’mapiri ataliatali a ku Isiraeli.+ Kumeneko zizidzagona pansi m’malo abwino kwambiri.+ Zizidzadya msipu wobiriwira bwino m’mapiri a ku Isiraeli.” 15  “‘“Ine ndidzadyetsa nkhosa zanga,+ ndipo ndidzazigonetsa pansi,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 16  “Nkhosa zosochera ndidzazifunafuna,+ zomwazika ndidzazibweza. Yothyoka mwendo ndidzaimanga mwendo wothyokawo. Yodwala ndidzailimbitsa, koma yonenepa+ ndi yamphamvu ndidzaiwononga. Ndidzaipatsa chiweruzo monga chakudya chake.”+ 17  “‘Koma inu nkhosa zanga, imvani zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena. Iye wanena kuti: “Ine ndidzaweruza mwachilungamo pakati pa nkhosa ndi nkhosa inzake komanso pakati pa nkhosa zamphongo ndi mbuzi zamphongo.+ 18  Kodi mukuona ngati n’chinthu chaching’ono kuti inu muzidya msipu wabwino kwambiri+ koma msipu wotsala n’kuupondaponda ndi mapazi anu? Kodi mukuona ngati n’chinthu chaching’ono kuti inu muzimwa madzi oyera koma madzi otsala muziwadetsa mwa kuwapondaponda ndi mapazi anu? 19  Kodi nkhosa zanga zizidya msipu wa pamalo odyetserapo ziweto umene inu mwaupondaponda ndi mapazi anu? Kodi zizimwa madzi amene mwawadetsa powapondaponda ndi mapazi anu?” 20  “‘Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kwa iwo kuti: “Ndithu ine ndidzapereka chiweruzo pakati pa nkhosa yonenepa ndi nkhosa yowonda. 21  Ndidzachita zimenezi chifukwa chakuti munali kukankha nkhosa ndi nthiti zanu ndiponso mapewa anu. Munali kugunda ndi nyanga zanu nkhosa zonse zodwala mpaka kuzibalalitsira kunja.+ 22  Ine ndidzapulumutsa nkhosa zanga, ndipo sizidzabedwanso.+ Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa inzake. 23  Ndidzazipatsa m’busa mmodzi,+ amene ndi mtumiki wanga Davide,+ ndipo adzazidyetsa. Iye adzakhala m’busa wawo ndipo adzazidyetsadi.+ 24  Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wawo,+ ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mtsogoleri pakati pawo.+ Ine Yehova ndanena zimenezi. 25  “‘“Ine ndidzachita nazo pangano la mtendere.+ Ndidzachotsa zilombo zolusa zakutchire m’dzikomo.+ Nkhosazo zidzakhala m’chipululu popanda choziopsa ndipo zizidzagona m’nkhalango.+ 26  Nkhosazo komanso malo ozungulira phiri langa ndidzawasandutsa dalitso.+ Ndidzagwetsa mvula yambiri pa nthawi yake. Kudzagwa mvula yambiri yamadalitso.+ 27  Mtengo wam’munda udzabereka zipatso.+ Nthaka idzatulutsa zokolola zake.+ Iwo adzakhala m’dziko lawo mwabata.+ Ndikadzathyola goli lawo+ ndi kuwapulumutsa m’dzanja la amene anali kuwagwiritsa ntchito monga akapolo,+ adzadziwa kuti ine ndine Yehova. 28  Iwo sadzabedwanso ndi anthu a mitundu ina.+ Chilombo chakutchire sichidzawadyanso. Adzakhala mwabata popanda wowaopsa.+ 29  “‘“Ndidzawapatsa munda wotchuka+ ndipo sadzafa ndi njala m’dzikomo.+ Mitundu ina ya anthu sidzawanyozanso.+ 30  ‘Iwo adzadziwa kuti ine, Yehova Mulungu wawo, ndili nawo limodzi+ ndiponso kuti iwowo, a nyumba ya Isiraeli ndi anthu anga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’+ 31  “‘Koma inu nkhosa zanga,+ nkhosa zimene ndikuzisamalira, ndinu anthu ochokera kufumbi. Ine ndine Mulungu wanu,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi