Ezekieli 33:1-33
33 Yehova analankhula nane kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, lankhula ndi anthu a mtundu wako+ ndipo uwauze kuti,“‘Ndikabweretsa lupanga m’dziko,+ ndipo mogwirizana anthu a m’dzikolo akasankha munthu kuti akhale mlonda wawo,+
3 mlondayo akaona lupanga likubwera m’dzikomo iye n’kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa kuchenjeza anthu,+
4 munthu akamva kulira kwa lipengalo koma osachitapo kanthu,+ lupanga n’kubwera ndi kumupha, magazi ake adzakhala pamutu pake.+
5 Iye anamva kulira kwa lipenga koma sanalabadire chenjezolo. Magazi ake adzakhala pamutu pake. Ngati iye akanalabadira chenjezo, akanapulumutsa moyo wake.+
6 “‘Koma mlondayo akaona lupanga likubwera, iye osaliza lipenga,+ anthu osamva chenjezo lililonse, lupangalo n’kufika ndi kupha anthu, anthuwo adzaphedwa chifukwa cha zolakwa zawo,+ koma magazi awo ndidzawafuna kuchokera m’manja mwa mlondayo.’+
7 “Koma iwe mwana wa munthu, ine ndakuika kuti ukhale mlonda wa nyumba ya Isiraeli.+ Umve mawu ochokera pakamwa panga ndi kundichenjezera anthuwo.+
8 Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa ndithu,’+ koma iwe osanena mawu alionse ochenjeza woipayo kuti asiye njira yake,+ iyeyo poti ndi woipa adzafa chifukwa cha zolakwa zake,+ koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera m’manja mwako.
9 Koma iweyo ukachenjeza munthu woipa kuti asiye njira zake ndi kubwerera, koma iye osasiya njira zake zoipa ndi kubwerera, munthuyo adzafa chifukwa cha zoipa zake.+ Koma iweyo udzapulumutsa moyo wako.+
10 “Choncho iwe mwana wa munthu, uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Anthu inu mwanena kuti: “Tingakhale bwanji ndi moyo, popeza kuti kupanduka kwathu ndi machimo athu zili pa ife ndipo tikuwola+ chifukwa cha zimenezi?”’+
11 Auze kuti, ‘“Pali ine Mulungu wamoyo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa,+ koma ndimafuna kuti munthu woipa abwerere+ kusiya njira zake n’kukhala ndi moyo.+ Bwererani! Bwererani ndi kusiya njira zanu zoipa.+ Muferenji inu a nyumba ya Isiraeli?”’+
12 “Iwe mwana wa munthu, uza anthu a mtundu wako kuti, ‘Munthu wolungama akapanduka, chilungamo chake sichidzamupulumutsa pa tsiku la kupanduka kwake.+ Koma munthu woipa akabwerera n’kusiya zoipa zakezo, sadzafa chifukwa cha zoipazo pa tsiku limene adzabwerere n’kuzisiya.+ Komanso munthu wolungama sadzakhalabe ndi moyo chifukwa cha chilungamo chake pa tsiku limene adzachimwe.+
13 Ndikauza munthu wolungama kuti: “Iwe udzakhalabe ndi moyo,” ndiyeno iyeyo n’kudalira kwambiri kulungama kwakeko n’kuchita zinthu zopanda chilungamo,+ zochita zake zonse zolungama zija sizidzakumbukiridwa. Iye adzafa chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene anachita.+
14 “‘Ndikauza munthu woipa kuti: “Udzafa ndithu,”+ ndiyeno iye n’kubwerera kusiya machimo akewo,+ n’kuyamba kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo,+
15 akabweza chinthu chimene anatenga kwa munthu amene anakongola zinthu zake,+ akabweza zinthu zimene analanda mwauchifwamba,+ n’kuyamba kuyenda motsatira malamulo opatsa moyo mwa kupewa kuchita zinthu zopanda chilungamo,+ munthuyo adzakhalabe ndi moyo,+ sadzafa ayi.
16 Palibe tchimo ngakhale limodzi mwa machimo onse amene anachita limene lidzakumbukiridwe ndi kumulanga nalo.+ Iye anachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo. Choncho adzakhalabe ndi moyo.’+
17 “Anthu a mtundu wako anena kuti, ‘Njira za Yehova n’zopanda chilungamo,’+ komatu njira zawo ndiye zopanda chilungamo.
18 “Munthu wolungama akasiya chilungamo chake n’kumachita zinthu zopanda chilungamo, ayenera kufa chifukwa cha zochita zakezo.+
19 Munthu woipa akasiya kuchita zinthu zoipa n’kuyamba kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, adzakhalabe ndi moyo chifukwa cha zochita zake zolungamazo.+
20 “Anthu inu mwanena kuti, ‘Njira za Yehova n’zopanda chilungamo.’+ Inu a nyumba ya Isiraeli, ine ndidzaweruza aliyense wa inu malinga ndi njira zake.”+
21 Ndiyeno m’chaka cha 12 kuchokera pamene tinatengedwa ukapolo, m’mwezi wa 10, pa tsiku lachisanu la mweziwo, kunafika munthu amene anapulumuka kuchokera ku Yerusalemu. Iye anandiuza+ kuti: “Mzinda uja wawonongedwa!”+
22 Tsopano madzulo, munthu wopulumuka uja asanafike, dzanja la Yehova linandikhudza.+ Ndipo Mulungu anatsegula pakamwa panga, wopulumuka uja asanafike m’mawa. Pakamwa panga panatseguka ndipo ndinayambanso kulankhula.+
23 Yehova anayamba kundiuza kuti:
24 “Iwe mwana wa munthu, anthu okhala m’malo owonongedwa+ akulankhula za dziko la Isiraeli kuti, ‘Abulahamu anali munthu mmodzi koma anatenga dzikoli.+ Ife tilipo ambiri, choncho dzikoli laperekedwa kwa ife kuti likhale lathu.’+
25 “Choncho auze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inu mumadya nyama limodzi ndi magazi ake,+ mumayang’anitsitsa mafano anu onyansa+ ndipo mumakhetsa magazi.+ Kodi pamenepa ndinu oyenera kutenga dzikoli kuti likhale lanu?+
26 Mumadalira lupanga lanu.+ Mwachita zinthu zonyansa+ ndipo aliyense wa inu waipitsa mkazi wa mnzake.+ Kodi pamenepa ndinu oyenera kutenga dzikoli kuti likhale lanu?”’+
27 “Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndithu anthu amene ali m’malo owonongedwa adzaphedwa ndi lupanga.+ Munthu amene ali kutchire ndidzam’pereka kwa chilombo cholusa kuti akhale chakudya chake.+ Anthu amene ali m’malo otetezeka ndi m’mapanga+ adzafa ndi mliri.
28 Dzikolo ndidzalisandutsa bwinja+ ndiponso malo owonongeka. Ndidzathetsa mphamvu zimene dzikolo limanyadira.+ Mapiri a mu Isiraeli adzawonongedwa+ ndipo sipadzapezeka wodutsamo.
29 Dzikolo ndikadzalisandutsa bwinja ndiponso malo owonongeka+ chifukwa cha zonyansa zonse zimene achita,+ iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’
30 “Koma iwe mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akukambirana za iwe m’mbali mwa mpanda ndi m’makomo a nyumba.+ Aliyense akuuza m’bale wake kuti, ‘Bwerani mudzamve mawu a Yehova.’+
31 Iwo adzabwera kwa iwe ngati mmene amachitira nthawi zonse ndipo adzakhala pamaso pako ngati anthu anga.+ Adzamva mawu ako koma sadzawatsatira,+ chifukwa ndi pakamwa pawo, akulankhula za zilakolako zawo zonyansa ndipo mtima wawo uli pa kupeza phindu mopanda chilungamo.+
32 Kwa iwo uli ngati munthu woimba nyimbo zachikondi. Uli ngati munthu wa mawu anthetemya komanso wodziwa kuimba choimbira cha zingwe.+ Iwo adzamva ndithu mawu ako, koma palibe amene adzawatsatire.+
33 Koma mawu ako akadzakwaniritsidwa, pakuti adzakwaniritsidwa ndithu,+ iwo adzadziwa kuti pakati pawo panalidi mneneri.”+