Ezekieli 32:1-32

32  M’chaka cha 12, m’mwezi wa 12, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova analankhula nanenso kuti:  “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza Farao, mfumu ya Iguputo. Uuze mfumuyo kuti, ‘Iwe wawonongedwa ngakhale kuti unali ngati mkango wamphamvu pakati pa mitundu ina ya anthu.+ “‘Unali ngati chilombo cham’nyanja.+ Nthawi zonse unali kuyenda mwamphamvu ngati madzi m’mitsinje yako, ndipo unali kuvundula madzi ndi mapazi ako ndi kudetsa mitsinjeyo.’  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzakuphimba ndi ukonde+ wanga pogwiritsa ntchito khamu la anthu ambiri a mitundu ina, ndipo iwo adzakukola ndi khoka langa.+  Ndidzakusiya pamtunda ndiponso ndidzakuponya kuchigwa.+ Ndidzachititsa kuti zolengedwa zonse zouluka m’mlengalenga zitere pa iwe. Ndidzakhutitsa zilombo zakutchire ndi nyama yako.+  Mnofu wako ndidzauika m’mapiri, ndipo m’zigwa ndidzadzazamo zotsalira za mtembo wako.+  Ndidzachititsa dziko kumwa zinthu zotuluka m’thupi mwako. Ndidzalichititsa kumwa magazi+ ako m’mapiri. Mitsinje idzadzaza ndi zinthu zotuluka m’thupi mwako.’  “‘Ndikadzakuzimitsa, ndidzaphimba kumwamba n’kuchititsa mdima nyenyezi zake. Dzuwa ndidzaliphimba ndi mitambo ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.+  Zounikira zonse zakumwamba ndidzazichititsa mdima chifukwa cha iwe, ndipo ndidzagwetsa mdima m’dziko lako,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.  “‘Ndidzakhumudwitsa mitima ya anthu ambiri a mitundu ina ndikadzatenga ena mwa anthu ako ndi kuwapititsa kudziko lina, kwa anthu a mitundu ina, kumayiko amene sukuwadziwa.+ 10  Ndidzachititsa mantha anthu ambiri a mitundu ina chifukwa cha iwe.+ Ndikadzawaloza ndi lupanga langa kumaso,+ mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha. Kuyambira pa tsiku limene udzaphedwe, aliyense wa iwo azidzanjenjemera nthawi zonse chifukwa choopa kufa.’+ 11  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Lupanga la mfumu ya Babulo lidzafika pa iwe.+ 12  Ndidzachititsa khamu la anthu ako kuphedwa ndi malupanga a anthu amphamvu. Anthu onsewo ndi olamulira ankhanza a mitundu ina ya anthu.+ Iwo adzawononga zonse zimene Iguputo amazinyadira ndipo khamu lake lonse lidzawonongedwa.+ 13  Ndidzawononga ziweto zake zonse ndi kuzichotsa m’mbali mwa madzi.+ Phazi la munthu komanso ziboda za chiweto sizidzavundulanso madziwo.’+ 14  “‘Pa nthawi imeneyo ndidzayeretsa madzi awo, ndipo madzi a m’mitsinje yawo adzayenda ngati mafuta,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 15  “‘Ndikadzasandutsa dziko la Iguputo bwinja ndipo zinthu zonse za m’dzikolo zikadzawonongedwa,+ komanso ndikadzapha anthu onse okhala m’dzikolo, anthu a mitundu ina adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 16  “‘Imeneyi ndi nyimbo yoimba polira ndipo anthu adzaiimba. Ana aakazi a mitundu ina ya anthu adzaiimba. Nyimbo imeneyi adzaimbira Iguputo ndi khamu lake lonse,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 17  M’chaka cha 12, pa tsiku la 15 la mwezi, Yehova analankhula nanenso kuti: 18  “Iwe mwana wa munthu, lirira khamu la ku Iguputo ndi kulengeza kuti lidzatsikira kumanda.+ Dzikolo ndi anthu a mitundu yamphamvu adzatsikira pansi pa nthaka+ limodzi ndi amene akutsikira kudzenje.+ 19  “‘Kodi ndiwe wosangalatsa kwambiri kuposa ndani?+ Tsikira kumanda ndipo uikidwa limodzi ndi anthu osadulidwa.’+ 20  “‘Aiguputo adzaphedwa pamodzi ndi anthu ophedwa ndi lupanga.+ Dzikolo laperekedwa ku lupanga. Anthu inu, kokerani kutali dzikolo ndi khamu lake lonse. 21  “‘Ku Mandako, atsogoleri a anthu amphamvu adzalankhula ndi iyeyo komanso amene anali kumuthandiza.+ Onsewo adzatsikira kumanda.+ Iwo adzaphedwa ndi lupanga ndipo adzaikidwa m’manda mofanana ndi anthu osadulidwa. 22  Kumeneko n’kumene kuli Asuri ndi khamu lake lonse.+ Manda a anthu a ku Asuri ali mozungulira mfumu yawo. Onsewo anaphedwa ndi lupanga.+ 23  Manda a Asuri ali pakatikati pa dzenje+ ndipo khamu lake lonse lazungulira manda akewo. Onsewo anaphedwa ndi lupanga chifukwa anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo. 24  “‘Kumandako n’kumene kuli Elamu+ ndi khamu lake lonse. Khamu lakelo linaikidwa mozungulira manda ake. Onsewo anaphedwa ndi lupanga. Iwo anatsikira kunthaka ali osadulidwa. Amenewa anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo, ndipo adzanyozeka limodzi ndi onse otsikira kudzenje.+ 25  Bedi lake aliika pakati pa anthu ophedwa,+ aliika pakati pa khamu lake lonse. Manda a anthu ake azungulira bedilo. Onsewo ndi anthu osadulidwa, ophedwa ndi lupanga+ chifukwa anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo. Adzanyozeka limodzi ndi amene akutsikira kudzenje. Iye waikidwa m’manda pakati pa anthu ophedwa. 26  “‘Kumeneko kulinso dziko la Meseke,+ Tubala+ ndi makamu awo onse. Manda awo ali mozungulira mfumu yawo. Onsewa ndi anthu osadulidwa, anthu olasidwa ndi lupanga chifukwa chakuti anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo. 27  Kodi amenewa sadzagona limodzi ndi anthu amphamvu+ amene anaphedwa pakati pa anthu osadulidwa? Kodi sadzagona limodzi ndi anthu amene anatsikira ku Manda limodzi ndi zida zawo zankhondo? Mitu yawo idzatsamira malupanga awo ndipo mafupa awo adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo,+ chifukwa anthu amphamvuwo anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo.+ 28  Koma iwe udzathyoledwa pakati pa anthu osadulidwa ndipo udzagona limodzi ndi anthu ophedwa ndi lupanga. 29  “‘Kumeneko n’kumene kuli Edomu,+ mafumu ake ndi atsogoleri ake onse. Amenewa anaikidwa m’manda akadali amphamvu. Anaikidwa pamodzi ndi ophedwa ndi lupanga.+ Iwo adzagona limodzi ndi anthu osadulidwa+ komanso anthu amene akutsikira kudzenje. 30  “‘Kumeneko n’kumene kuli nduna zonse za kumpoto. Kulinso Asidoni+ onse amene anatsikira kumanda ali amanyazi. Anatsikira kumeneko limodzi ndi ophedwa, ngakhale kuti anali ochititsa mantha chifukwa cha mphamvu zawo. Adzagona m’manda limodzi ndi ophedwa ndi lupanga ali osadulidwa. Iwo adzachita manyazi pamodzi ndi otsikira kudzenje.+ 31  “‘Amenewa ndiwo anthu amene Farao adzawaone ndipo mtima wake udzakhala pansi poona khamu lake lonse.+ Farao ndi gulu lake lonse lankhondo adzakhala m’gulu la anthu ophedwa ndi lupanga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 32  “‘Zimenezi zidzamuchitikira chifukwa anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo.+ Farao ndi khamu lake lonse adzaikidwa m’manda pakati pa anthu osadulidwa. Iye adzaikidwa m’manda pamodzi ndi anthu ophedwa ndi lupanga,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi