Ezekieli 31:1-18

31  Ndiyeno m’chaka cha 11, m’mwezi wachitatu, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova anandiuzanso kuti:  “Iwe mwana wa munthu, uza Farao mfumu ya Iguputo ndi khamu lake kuti,+“‘Kodi wakula kufanana ndi ndani?  Wafanana ndi Msuri. Wafanana ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,+ wanthambi zikuluzikulu zokongola,+ wanthambi za masamba ambiri zopereka mthunzi, mtengo wautali kwambiri+ umene nsonga yake inafika m’mitambo.+  Mtengowo unakula kwambiri chifukwa cha madzi.+ Unatalika chifukwa cha madzi akuya. Madziwo anali kuyenda m’mitsinje kuzungulira pamalo pamene mtengowo unabzalidwa. Ngalande za madziwo zinakafika kumitengo yonse ya kumeneko.  N’chifukwa chake mtengowo unatalika kwambiri kuposa mitengo yonse yakumaloko.+ “‘Nthambi zake zikuluzikulu zinali kuchuluka, ndipo nthambi zina zinapitiriza kutalika chifukwa cha kuchuluka kwa madzi m’ngalande zake.+  Zolengedwa zonse zouluka m’mlengalenga zinali kumanga zisa zawo m’nthambi zake zikuluzikuluzo.+ Nyama zonse zakutchire zinkaberekera pansi pa nthambi zake.+ Mitundu yonse ya anthu ambiri inali kukhala mumthunzi wake.  Mtengowo unakongola kwambiri+ chifukwa cha kukula kwake ndi kutalika kwa nthambi zake zamasamba ambiri. Izi zinachitika chifukwa chakuti mizu yake inali pamadzi ambiri.  Mitengo ina ya mkungudza sinafanane ndi mtengo umenewu m’munda wa Mulungu.+ Nthambi zikuluzikulu za mitengo ina yooneka ngati mkungudza, sizinafanane ndi za mtengo umenewu. Nthambi za mitengo ya katungulume sizinafanane ndi nthambi za mtengo umenewu. Panalibenso mtengo wina m’munda wa Mulungu umene unali wokongola ngati mtengo umenewu.+  Mtengo umenewu ndinaukongoletsa pouchulukitsira nthambi zamasamba ambiri.+ Mitengo ina yonse ya mu Edeni, imene inali m’munda wa Mulungu woona, inali kuuchitira nsanje.’+ 10  “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti mtengowu unatalika kwambiri moti nsonga yake inakafika m’mitambo,+ ndipo mtima wake unayamba kudzikuza chifukwa cha kutalika kwake,+ 11  ndidzaupereka m’manja mwa wolamulira wamphamvu wa mitundu ina.+ Iye adzaukhaulitsa, ndipo chifukwa cha kuipa kwake ine ndidzauthamangitsa.+ 12  Anthu achilendo, olamulira ankhanza a mitundu ina, adzadula mtengowo ndipo anthu adzausiya m’mapiri. Masamba ake adzagwera m’zigwa zonse ndipo nthambi zake zidzathyoka ndi kugwera m’mitsinje ya padziko lapansi.+ Mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi idzachoka mumthunzi wake n’kuusiya.+ 13  Zolengedwa zonse zouluka m’mlengalenga zidzakhala pathunthu lake logwetsedwalo, ndipo nyama zonse zakutchire zidzakhala m’nthambi zake.+ 14  Choncho sipadzakhalanso mtengo uliwonse wothiriridwa bwino umene udzakhale wautali kwambiri kapena umene nsonga zake zidzafike m’mitambo. Sipadzakhala mtengo uliwonse umene uli pamadzi ambiri umene udzatalike kukafika m’mitambo, pakuti mitengo yonse idzakhala itadulidwa.+ Yonse idzakhala itatsikira pansi pa nthaka+ pamodzi ndi ana a anthu amene akutsikira kudzenje.’ 15  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsiku limene mtengo wamkungudza udzatsikire ku Manda* ndidzachititsa anthu kulira.+ Ndidzaphimba madzi akuya chifukwa cha mtengowo. Ndidzachita izi kuti ndiimitse madzi m’mitsinje yake ndi kutseka madzi ambiri. Ndidzachititsa mdima mu Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse yakutchire idzafota. 16  Mitundu ya anthu ikadzamva phokoso la kugwa kwake idzanjenjemera. Zimenezi zidzachitika ndikadzatsitsira mtengowo ku Manda pamodzi ndi amene akutsikira kudzenje.+ Mitengo yonse ya mu Edeni+ imene ili pansi pa nthaka, mitengo yabwino kwambiri ya ku Lebanoni ndi mitengo yonse imene inali pamadzi ambiri, idzatonthozedwa.+ 17  Mitengo imeneyi yatsikira ku Manda pamodzi ndi mtengo wa mkungudzawo.+ Yatsikira kwa ophedwa ndi lupanga ndi kwa amene ankakhala mumthunzi wake pakati pa mitundu ina ya anthu monga mbewu yake.’+ 18  “‘Kodi iwe ukufanana ndi ndani pa nkhani ya ulemerero+ ndi kukula pakati pa mitengo ya mu Edeni?+ Koma ndithu udzatsikira pansi pa nthaka limodzi ndi mitengo ya mu Edeni.+ Udzagona pakati pa anthu osadulidwa limodzi ndi ophedwa ndi lupanga. Mtengo umenewu ukuimira Farao ndi khamu lake lonse,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 5.