Ezekieli 30:1-26
30 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, losera kuti,+ ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Fuulani anthu inu kuti, ‘Kalanga ine! Tsiku lija layandikira.’+
3 Tsikulo lili pafupi. Inde tsiku la Yehova lili pafupi.+ Limeneli lidzakhala tsiku la mitambo,+ ndiponso nthawi yoikidwiratu yoti mitundu ya anthu iweruzidwe.+
4 Lupanga lidzafikadi mu Iguputo,+ ndipo ku Itiyopiya anthu adzamva ululu waukulu. Izi zidzachitika anthu akadzaphedwa mu Iguputo, chuma cha dzikolo chikadzalandidwa komanso maziko ake akadzagwetsedwa.+
5 Itiyopiya,+ Puti,+ Ludi, anthu onse ochokera ku mitundu ina,+ Kubi ndi anthu ochokera m’dziko la Isiraeli amene ali m’pangano, onsewa adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Aiguputo.”’+
6 “Yehova wanena kuti, ‘Nawonso othandiza Iguputo adzaphedwa, ndipo mphamvu zimene amazinyadira zidzatha.’+
“‘Kuchokera ku Migidoli+ mpaka ku Seyene,+ anthu adzaphedwa ndi lupanga m’dzikolo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
7 ‘Onsewo adzakhala mabwinja pakati pa mayiko omwe simukukhalanso anthu ndipo mizinda yake idzakhala pakati pa mizinda yowonongedwa.+
8 Ndikadzayatsa moto mu Iguputo, ndipo onse omuthandiza akadzawonongedwa, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+
9 Pa tsikulo, amithenga ochokera kwa ine adzakwera zombo kuti akaopseze Itiyopiya yemwe ndi wodzidalira.+ Itiyopiya adzamva ululu woopsa pa tsiku limene Iguputo adzawonongedwe, pakuti tsikulo lidzafika ndithu.’+
10 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzawononga khamu la ku Iguputo pogwiritsa ntchito dzanja la Nebukadirezara, mfumu ya Babulo.+
11 Mfumuyo ndi anthu ake, olamulira ankhanza a mitundu ina ya anthu,+ akubwera kudzawononga dzikolo kuti likhale bwinja. Iwo adzasolola malupanga awo kumenyana ndi Iguputo ndipo adzadzaza dzikolo ndi anthu ophedwa.+
12 Ndidzaumitsa ngalande zotuluka mumtsinje wa Nailo+ ndi kugulitsa dzikolo kwa anthu oipa.+ Ndidzachititsa kuti dzikolo ndi zonse zimene zili mmenemo ziwonongedwe ndi anthu achilendo.+ Ine Yehova, ndanena zimenezi.’+
13 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzawononganso mafano onyansa+ ndi kuthetsa milungu yopanda pake ku Nofi.+ Sipadzapezekanso mtsogoleri wochokera m’dziko la Iguputo, ndipo ndidzachititsa anthu a m’dzikolo kukhala mwamantha.+
14 Mzinda wa Patirosi+ ndidzausandutsa bwinja. Mzinda wa Zowani+ ndidzautentha ndi moto ndipo ndidzapereka ziweruzo mumzinda wa No.+
15 Ndidzatsanulira mkwiyo wanga+ pa Sini, malo otetezedwa kwambiri a Iguputo, ndipo ndidzapha khamu la anthu a ku No.+
16 Ndidzayatsa moto mu Iguputo. Sini adzamva ululu waukulu, No adzalandidwa ndi adani amene adzagumule mpanda wake. Adani adzalowa mumzinda wa Nofi masanasana.
17 Anyamata a ku Oni+ ndi ku Pibeseti adzaphedwa ndi lupanga. Anthu a m’mizinda imeneyi adzatengedwa kupita ku ukapolo.
18 Mumzinda wa Tahapanesi+ mudzagwa mdima masana ndikadzathyola magoli a Iguputo kumeneko.+ Mphamvu zimene amazinyadira zidzathetsedwa.+ Iye adzakutidwa ndi mitambo+ ndipo anthu a m’mizinda yake yozungulira adzatengedwa kupita ku ukapolo.+
19 Ndidzapereka ziweruzo mu Iguputo+ ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”
20 Ndiyeno m’chaka cha 11, m’mwezi woyamba, pa tsiku la 7 la mweziwo, Yehova analankhulanso ndi ine kuti:
21 “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzathyola dzanja la Farao mfumu ya Iguputo.+ Dzanjalo silidzamangidwa ndi nsalu zomangira pachilonda+ kuti lichire n’kukhalanso lamphamvu kuti lizidzatha kugwira lupanga.”
22 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndithana ndi Farao mfumu ya Iguputo.+ Ndidzathyola manja ake onse,+ dzanja lamphamvu ndi lothyoka lija,+ ndipo ndidzachititsa kuti lupanga ligwe m’dzanja lake.+
23 Ine ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu ndi kuwamwazira kumayiko ena.+
24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya Babulo+ ndipo ndidzaipatsa lupanga langa.+ Ndidzathyola manja a Farao ndipo adzabuula kwambiri pamaso pa mfumu ya Babulo monga wovulazidwa koopsa.+
25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya Babulo ndipo Farao adzagwetsa manja ake. Ndikadzapereka lupanga langa m’manja mwa mfumu ya Babulo, iye n’kuligwiritsa ntchito pomenyana ndi dziko la Iguputo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+
26 Ine ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu+ ndi kuwamwazira kumayiko ena, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”