Ezekieli 3:1-27
3 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya chimene chili pamaso pakochi. Idya mpukutuwu,+ kenako upite kukalankhula ndi nyumba ya Isiraeli.”
2 Pamenepo ndinatsegula pakamwa panga, ndipo iye anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye.+
3 Kenako anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsawu, kuti mimba yako ikhute ndiponso kuti mpukutuwo udzaze m’matumbo mwako.” Choncho ndinayamba kudya mpukutuwo, ndipo unali wotsekemera* ngati uchi m’kamwa mwanga.+
4 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, pita pakati pa nyumba+ ya Isiraeli ndipo ukawauze mawu anga.
5 Pakuti sindikukutuma kwa anthu olankhula chinenero chovuta kumva+ ndiponso a lilime lolemera.+ Koma ndikukutuma kunyumba ya Isiraeli,
6 osati kwa mitundu yambiri ya anthu olankhula chinenero chovuta kumva kapena a lilime lolemera, amene sungathe kumvetsetsa mawu awo.+ Ndikanakhala kuti ndinakutuma kwa anthu amenewo, akanakumvera.+
7 Koma a nyumba ya Isiraeli sakafuna kukumvera, chifukwa iwo safuna kundimvera.+ Pakuti anthu onse a nyumba ya Isiraeli ndi amakani ndi osamva.+
8 Koma ndachititsa nkhope yako kuti ikhale yolimba mofanana ndi nkhope zawo,+ ndiponso chipumi chako kuti chikhale cholimba mofanana ndi zipumi zawo.+
9 Ndachititsa chipumi chako kukhala ngati mwala wa dayamondi, cholimba kuposa mwala wa nsangalabwi.+ Usawaope,+ ndipo usachite mantha ndi nkhope zawo,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.”+
10 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, usunge mumtima mwako mawu anga onse amene ndikukuuza,+ ndipo umve ndi makutu ako.
11 Pita pakati pa anthu otengedwa ukapolo,+ pakati pa ana a anthu a mtundu wako, ndipo ukawauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena,’ kaya akamve kapena ayi.”+
12 Kenako mzimu unanditenga+ ndipo kumbuyo kwanga ndinayamba kumva mawu amphamvu ngati chimkokomo chachikulu,+ akuti: “Utamandike ulemerero wa Yehova kumalo ake.”+
13 Kenako ndinamva phokoso la mapiko a zamoyo amene anali kukhulana pafupipafupi.+ Ndinamvanso phokoso la mawilo amene anali pambali pawo,+ ndi chimkokomo chachikulu.
14 Mzimu unandinyamula+ moti ndinapita ndili wachisoni ndi wokwiya kwambiri mumtima mwanga, ndipo dzanja la Yehova linandigwira mwamphamvu.+
15 Chotero ndinapita kwa anthu otengedwa ukapolo amene anali ku Tele-abibu, amene anali kukhala+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara.+ Ndinayamba kukhala pamalo pamene anthuwo anali kukhala ndipo ndinakhala pamenepo masiku 7. Ndinangokhala phee pakati pawo, ndili m’maganizo.+
16 Pamapeto pa masiku 7, Yehova analankhula nane, kuti:
17 “Iwe mwana wa munthu, ine ndakuika kuti ukhale mlonda wa nyumba ya Isiraeli.+ Umve mawu ochokera pakamwa panga ndipo undichenjezere anthuwo.+
18 Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’+ iwe osamulankhula munthu woipayo ndi kumuchenjeza kuti asiye njira yake yoipa n’cholinga choti akhalebe ndi moyo,+ iyeyo poti ndi woipa adzafa chifukwa cha zolakwa zake,+ koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera m’manja mwako.+
19 Koma iweyo ukachenjeza munthu woipa,+ koma iye osasiya zoipa zakezo ndi njira zake zoipa, munthuyo adzafa chifukwa cha zoipa zake.+ Koma iweyo udzakhala utapulumutsa moyo wako.+
20 Munthu wolungama akasiya chilungamo chake+ n’kumachita zinthu zopanda chilungamo, ine n’kumuikira chopunthwitsa pamaso pake,+ iyeyo adzafa chifukwa chakuti sunamuchenjeze. Adzafa chifukwa cha tchimo lake+ ndipo zinthu zolungama zimene anachita sizidzakumbukiridwa,+ koma magazi ake ndidzawafuna kwa iweyo.+
21 Koma ngati iweyo unachenjeza munthu wolungama kuti asachimwe,+ iye osachimwadi, munthuyo adzakhalabe ndi moyo chifukwa anachenjezedwa,+ ndipo iweyo udzakhala utapulumutsa moyo wako.”+
22 Kenako dzanja la Yehova linafika pa ine kumeneko ndipo iye anandiuza kuti: “Nyamuka, pita kuchigwa+ ndipo ndikalankhula nawe kumeneko.”
23 Chotero ndinanyamuka n’kupita kuchigwako. Kumeneko ndinangoona kuti ulemerero wa Yehova waimirira,+ ngati ulemerero umene ndinauona pafupi ndi mtsinje wa Kebara.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+
24 Kenako mzimu unalowa mwa ine+ n’kundiimiritsa,+ ndipo Mulungu anayamba kulankhula nane, kuti:
“Pita ukadzitsekere m’nyumba mwako.
25 Tsopano iwe mwana wa munthu, dziwa kuti adzakumanga ndi zingwe kuti usapite pakati pawo.+
26 Ndidzachititsa lilime lako kumatirira kumwamba m’kamwa mwako,+ ndipo sudzathanso kulankhula.+ Sudzakhalanso munthu wowadzudzula,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.+
27 Ndikamalankhula nawe ndizikutsegula pakamwa. Ndiyeno iweyo uzikawauza kuti,+ ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’ Wakumva amve,+ ndipo wosamva asamve, pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “wonzuna.”