Ezekieli 29:1-21
29 M’chaka cha 10, m’mwezi wa 10, pa tsiku la 12 la mweziwo, Yehova analankhula nane kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana kwa Farao mfumu ya Iguputo+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzachitikire iyeyo ndi dziko lonse la Iguputo.+
3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndilanga iwe Farao mfumu ya Iguputo.+ Ndiwe chilombo chachikulu cha m’nyanja+ chimene chagona m’ngalande zake zotuluka mumtsinje wa Nailo.+ Ndiwe chilombo chimene chanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga, ndipo ineyo ndinaupanga ndekha.’+
4 Ndidzakukola ndi ngowe munsagwada zako+ ndi kuchititsa nsomba za m’ngalande za mtsinje wa Nailo kukakamira kumamba ako. Ndidzakutulutsa m’ngalande za Nailo pamodzi ndi nsomba zonse za m’ngalandezo zimene zakakamira kumamba ako.
5 Iwe ndidzakutaya m’chipululu pamodzi ndi nsomba zonse za m’ngalande za Nailo.+ Udzagwera panthaka+ ndipo palibe amene adzakutenge kukakuika m’manda. Ndidzakupereka kwa zilombo zakutchire ndi zolengedwa zouluka kuti ukhale chakudya chawo.+
6 Anthu onse okhala ku Iguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova+ chifukwa chakuti iwo anali ngati bango loyendera la nyumba ya Isiraeli.+
7 Atakugwira dzanja ndi kukutsamira ngati ndodo yoyendera, unaphwanyika+ ndipo unachititsa kuti miyendo* yawo ikhale yagwedegwede,+ zimene zinawachititsa kuti athyole+ phewa lawo.”
8 “‘Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndibweretsa lupanga+ m’dziko lako ndipo ndidzapha anthu ndi ziweto.+
9 Dziko la Iguputo lidzakhala bwinja ndi malo owonongeka.+ Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova chifukwa chakuti iwe Farao wanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga, ndipo ineyo ndinaupanga ndekha.’+
10 Choncho, iwe ndikulanga ndi kuwononga ngalande zako zotuluka mu Nailo.+ Dziko la Iguputo ndiliwononga. Ndilisandutsa malo ouma komanso bwinja,+ kuchokera ku Migidoli+ mpaka ku Seyene+ kukafika kumalire a dziko la Itiyopiya.
11 M’dziko lako simudzaponda phazi la munthu+ kapena la chiweto,+ ndipo simudzakhala munthu aliyense kwa zaka 40.+
12 Dziko la Iguputo ndidzalisandutsa bwinja pakati pa mayiko omwe simukukhalanso anthu.+ Kwa zaka 40, mizinda yake idzakhala mabwinja pakati pa mizinda yopanda anthu.+ Ndidzamwaza Aiguputo pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsira m’mayiko ena.”+
13 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Zaka 40 zikadzatha,+ ndidzasonkhanitsa pamodzi Aiguputowo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina kumene adzabalalikire.+
14 Ndidzabwezeretsa gulu la Aiguputo amene anagwidwa n’kupita nawo kudziko lina. Ndidzawabwezeretsa kudera la Patirosi,+ m’dziko limene anachokera. Kumeneko adzakhazikitsa ufumu wonyozeka.
15 Ufumu wawo udzakhala wotsika kusiyana ndi maufumu ena ndipo sudzadzikwezanso pamaso pa mitundu ina ya anthu.+ Ndidzawachepetsa kwambiri moti sadzakhalanso ndi mphamvu zolamulira mitundu ina ya anthu.+
16 Nyumba ya Isiraeli sidzawadaliranso.+ Aisiraeli sadzachititsa kuti zolakwa zawo zikumbukiridwe mwa kutembenukira kwa Iguputo,+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’”
17 Tsopano m’chaka cha 27, m’mwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova analankhula nane kuti:
18 “Iwe mwana wa munthu, Nebukadirezara+ mfumu ya Babulo anatuma gulu lake lankhondo kukachita utumiki wofunika kwambiri pomenyana ndi Turo.+ Mutu wa msilikali aliyense unameteka ndipo mapewa awo ananyuka.+ Koma mfumuyo ndi gulu lake lankhondo sanalandire cholowa+ chilichonse pa utumiki umene anachita pomenyana ndi Turo.
19 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndipereka dziko la Iguputo kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo.+ Adzatenga chuma chake chochuluka ndi kulanda zinthu zake zambiri.+ Zimenezi zidzakhala malipiro a gulu lake lankhondo.’
20 “‘Ndamupatsa dziko la Iguputo monga chipukutamisozi pa utumiki wake umene anachita pomenyana ndi Turo, chifukwa iwo anachita zimene ine ndinali kufuna,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
21 “Pa tsikulo, ndidzaphukitsira nyumba ya Isiraeli nyanga.*+ Iwe ndidzakupatsa mpata kuti utsegule pakamwa pako pakati pawo,+ ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”