Ezekieli 28:1-26

28  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, uza mtsogoleri wa Turo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘“Chifukwa chakuti wadzikuza mumtima mwako,+ ndipo ukunena kuti, ‘Ndine mulungu.+ Ndakhala pampando wa mulungu+ pakatikati pa nyanja,’+ ngakhale kuti ndiwe munthu wochokera kufumbi+ osati mulungu,+ ndipo umadziona ngati mulungu . . .  iwe umaganiza kuti ndiwe wanzeru kuposa Danieli.+ Umaganiza kuti palibe chinsinsi chimene sukuchidziwa.+  Chifukwa chakuti ndiwe wanzeru ndiponso wozindikira, wapanga chuma ndipo ukupitiriza kusonkhanitsa golide ndi siliva m’nyumba zako zosungiramo zinthu.+  Wachulukitsa chuma chako+ chifukwa chakuti uli ndi nzeru zochuluka+ komanso umachita malonda.+ Chotero mtima wako wayamba kudzikuza chifukwa cha chuma chakocho.”’+  “‘Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Chifukwa chakuti umadziona ngati mulungu,+  ine ndikubweretsera alendo,+ anthu ankhanza a mitundu ina.+ Iwo adzasolola lupanga n’kuwononga chilichonse chokongola chimene unapeza chifukwa cha nzeru zako, ndipo adzaipitsa ulemerero wako wonyezimira.+  Adzakutsitsira kudzenje.+ Udzafa ngati munthu wophedwa ndi lupanga pakatikati pa nyanja.+  Kodi amene adzakuphe udzamuuza kuti, ‘Ine ndine mulungu,’+ pamene ndiwe munthu wamba wochokera kufumbi osati mulungu?+ Kodi udzanena zimenezi m’manja mwa okuipitsawo?”’ 10  “‘Udzafa ngati anthu osadulidwa ndipo alendo ndi amene adzakuphe,+ ine ndanena,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 11  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 12  “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza mfumu ya Turo.+ Uuze mfumuyo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘“Ndiwe chitsanzo changwiro. Uli ndi nzeru zochuluka+ ndipo ndiwe wokongola kwambiri.+ 13  Iwe unali mu Edeni, munda wa Mulungu.+ Unali kuvala chovala chokongoletsedwa ndi miyala yamtengo wapatali yamitundu yonse monga rube, topazi, yasipi, kulusolito, onekisi,+ yade, safiro, nofeki+ ndi emarodi. Zoikamo miyala imeneyi zinali zagolide. Anakukonzera zimenezi pa tsiku limene unalengedwa. 14  Iwe ndiwe kerubi wodzozedwa amene umagwira ntchito yoteteza, ndipo ine ndakuika pa udindo. Unali kukhala paphiri loyera la Mulungu.+ Unali kuyendayenda pamiyala yamoto. 15  Unali wopanda cholakwa m’njira zako kuchokera pa tsiku limene unalengedwa,+ kufikira pamene unachita zinthu zosalungama.+ 16  “‘“Chifukwa cha kuchuluka kwa malonda ako,+ mwa iwe munadzaza zachiwawa ndipo unayamba kuchita machimo.+ Iwe kerubi amene umagwira ntchito yoteteza, ine ndidzakutulutsa m’phiri la Mulungu monga wodetsedwa ndipo ndidzakuwononga pakati pa miyala yamoto.+ 17  “‘“Mtima wako unadzikweza chifukwa cha kukongola kwako.+ Unawononga nzeru zako chifukwa cha ulemerero wako wonyezimira.+ Ndidzakuponyera kudziko lapansi+ ndipo mafumu azidzakuyang’ana.+ 18  “‘“Chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako,+ chifukwa cha malonda ako opanda chilungamo,+ waipitsa malo ako opatulika. Ndidzabweretsa moto kuchokera pakati pako, ndipo udzakunyeketsa.+ Ndidzakusandutsa phulusa padziko lapansi pamaso pa anthu onse okuona.+ 19  Onse okudziwa pakati pa mitundu ya anthu adzakuyang’anitsitsa modabwa.+ Zoopsa zodzidzimutsa zidzakugwera ndipo sudzakhalaponso mpaka kalekale.”’”+ 20  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 21  “Iwe mwana wa munthu, yang’ana ku Sidoni+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzamuchitikire. 22  Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe Sidoni, ine ndithana nawe+ ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako.+ Ndikadzapereka ziweruzo mwa iwe ndi kuyeretsedwa kudzera mwa iwe,+ anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 23  Ndidzakutumizira miliri ndipo magazi adzayenderera m’misewu yako.+ Anthu ophedwa adzapezeka paliponse mwa iwe. Iwo adzaphedwa ndi lupanga lochokera kumbali zonse,+ moti anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 24  Nyumba ya Isiraeli sidzalasidwanso ndi cholasa chopweteka+ kapena minga zaululu zochokera kwa onse owazungulira, amene akuwatonza, ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’ 25  “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa pamodzi nyumba ya Isiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anabalalikira,+ ndidzayeretsedwa pakati pawo pamaso pa mitundu ina ya anthu.+ Ndithu, iwo adzakhala m’dziko lawo+ limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo.+ 26  Adzakhala m’dzikolo popanda chowaopseza,+ adzamanga nyumba+ ndi kulima minda ya mpesa.+ Iwo adzakhala mwabata+ ndikadzapereka chiweruzo kwa onse owazungulira amene akuwatonza.+ Ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo.”’”

Mawu a M'munsi