Ezekieli 25:1-17
25 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, yang’ana kwa ana a Amoni ndipo ulosere zoipa zimene zidzawachitikire.+
3 Uuze ana a Amoniwo kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Chifukwa chakuti malo anga opatulika adetsedwa, inu mwanena kuti: Eyaa! Zakhala bwino! Mwaneneranso zimenezi dziko la Isiraeli chifukwa chakuti lakhala bwinja, komanso nyumba ya Yuda chifukwa chakuti anthu ake atengedwa ukapolo.+
4 Pa chifukwa chimenechi, ndikuperekani kwa anthu a Kum’mawa kuti mukhale chuma chawo.+ Iwo adzamanga misasa yokhala ndi mipanda ndiponso mahema awo m’dziko lanu. Adzadya zokolola zanu ndi kumwa mkaka wanu.+
5 Mzinda wa Raba+ ndidzausandutsa malo odyetserako ngamila, ndipo dziko la ana a Amoni ndidzalisandutsa malo opumulirako gulu la nkhosa.+ Anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+
6 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti munawomba m’manja+ ndi kuponda pansi mwamphamvu, komanso munasangalala ndi mtima wonyoza poona zimene zinachitikira dziko la Isiraeli,+
7 ine ndakutambasulirani dzanja langa,+ ndipo ndidzakuperekani kwa mitundu ina ya anthu monga zofunkha. Ndidzakuphani ndi kukuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndi kukuwonongani kuti musapezekenso m’dziko.+ Ndidzakufafanizani,+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’
8 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Popeza kuti Mowabu+ ndi Seiri+ anena kuti: “Taonani! Nyumba ya Yuda ili ngati mitundu ina yonse ya anthu,”+
9 ine ndidzaonetsa adani awo malo otsetsereka a ku Mowabu. Kumalo amenewa ndi kumene kuli mizinda ya m’malire a dzikolo. Mizinda yake ndi Beti-yesimoti,+ Baala-meoni+ ndi Kiriyataimu.+ Mizinda imeneyi imakongoletsa dzikolo.
10 Ndidzapereka Mowabu limodzi ndi ana a Amoni+ kwa anthu a Kum’mawa+ kuti akhale chuma chawo. Ndidzachita izi kuti ana a Amoni asadzakumbukiridwenso+ pakati pa mitundu ya anthu.
11 Ndidzapereka chiweruzo m’dziko la Mowabu,+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+
12 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu walanga nyumba ya Yuda ndipo akupitiriza kuilanga ndi kuichitira zinthu zoipa kwambiri,+
13 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzatambasulira Edomu+ dzanja langa ndi kupha anthu ndi ziweto m’dzikolo.+ Ndidzalisandutsa bwinja kuyambira ku Temani+ mpaka ku Dedani.+ Iwo adzaphedwa ndi lupanga.
14 ‘Ine ndidzalanga Edomu kudzera mwa anthu anga Aisiraeli.+ Aisiraeliwo adzachitira Edomu mogwirizana ndi mkwiyo komanso ukali wanga, ndipo Aedomuwo adzadziwa mmene ndimalangira,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’
15 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Afilisiti achitira zoipa+ Aisiraeli ndipo akupitiriza kuwachitira zoipazo. Mumtima mwawo akusangalala ndiponso kuwanyoza. Akuchita zimenezi kuti awawononge+ chifukwa cha chidani chawo chomwe chidzakhalepo mpaka kalekale.+
16 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikutambasula dzanja langa kuti ndilange Afilisiti,+ ndipo ndidzapha Akereti+ ndi kuwononga anthu onse okhala m’mbali mwa nyanja.+
17 Anthu amenewa ndidzawalanga kwambiri ndi kuwadzudzula mwaukali,+ ndipo ndikadzawalanga adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+