Ezekieli 24:1-27

24  Yehova anapitiriza kulankhula nane m’chaka cha 9, m’mwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, kuti:  “Iwe mwana wa munthu, lemba dzina la tsikuli. Ulembe dzina la tsiku lalero. Lero mfumu ya Babulo yazungulira mzinda wa Yerusalemu kuti iuwononge.+  Nena mwambi wokhudza nyumba yopanduka.+ Unene kuti:“‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ika pamoto mphika wakukamwa kwakukulu ndipo uthiremo madzi.+  Uikemo nthuli za nyama,+ nthuli zabwinozabwino. Uikemo mwendo wam’mbuyo ndi wakutsogolo. Udzazemo mafupa abwino kwambiri.  Tenga nkhosa yabwino kwambiri+ ndipo usonkhezere nkhuni kuzungulira mphikawo. Uwiritse nthuli za nyamazo ndi kuphika mafupawo.”’”+  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Tsoka mzinda wokhetsa magazi,+ umene uli ngati mphika wakukamwa kwakukulu. Mphikawo uli ndi dzimbiri ndipo dzimbiri lakelo silikutha. Muchotsemo nthulizo imodziimodzi.+ Musachite maere pamphikawo.+  Pakuti magazi amene mzindawo wakhetsa ali mkati mwake.+ Waika magaziwo pathanthwe losalala, pamalo oonekera. Mzindawo sunathire magaziwo pansi kuti uwakwirire ndi dothi.+  Ine ndathira magazi amene wakhetsawo pathanthwe losalala ndi loonekera kuti asakwiriridwe.+ Ndachita zimenezi kuti mkwiyo wanga uyakire mzindawo ndi kuulanga chifukwa cha zochita zake.’+  “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Tsoka mzinda wokhetsa magazi!+ Ine ndidzaunjika mulu waukulu wa nkhuni.+ 10  Sonkhanitsani zikuni zambiri. Kolezani moto. Wiritsani nyamayo mpaka ipse. Khuthulani msuzi wake ndipo mafupawo atenthe kwambiri. 11  Ikani mphikawo pamakala amoto mulibe chilichonse kuti utenthe kwambiri. Mkuwa wa mphikawo utenthe kuti zonyansa zake zisungunukemo.+ Dzimbiri lake lipse ndi moto.+ 12  Ntchito yakula. Ntchito yoyeretsa mphikawo ndi yotopetsa koma dzimbiri lake, lomwe ndi lambiri, silikuchoka.+ Uponyeni pamoto ndi dzimbiri lakelo.’ 13  “‘Unachita zonyansa chifukwa cha khalidwe lako lotayirira.+ Ine ndinayesetsa kukuyeretsa, koma zonyansa zako sizinachoke.+ Sudzayeranso kufikira nditathetsera mkwiyo wanga pa iwe.+ 14  Tsoka lako lidzabwera ndithu+ ndipo ndidzachitapo kanthu. Sindidzazengereza,+ kumva chisoni+ kapena kusintha maganizo.+ Iwo adzakuweruza mogwirizana ndi njira zako ndi zochita zako.+ Ine Yehova ndanena,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 15  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 16  “Iwe mwana wa munthu, ine ndimenya+ chinthu chako chokongola ndi kuchichotsa kwa iwe.+ Koma iwe usadzigugude pachifuwa, kulira kapena kugwetsa misozi.+ 17  Uuse moyo mosatulutsa mawu. Anthu akufa usawalire maliro.+ Uvale chovala chakumutu+ ndipo uvale nsapato zako.+ Usaphimbe ndevu zako zapamlomo,+ ndipo usadye chakudya chimene anthu angakupatse.”+ 18  M’mawa ndinayamba kulankhula ndi anthu ndipo pofika madzulo, mkazi wanga anamwalira. Ndiyeno m’mawa ndinachita zimene anandilamula. 19  Anthu anayamba kundifunsa kuti: “Kodi sutiuza kuti zimene ukuchitazi zikutikhudza motani?”+ 20  Pamenepo ine ndinawayankha kuti: “Yehova wandiuza kuti, 21  ‘Uza nyumba ya Isiraeli kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndidetsa malo anga opatulika,+ chinthu chimene mumachinyadira kwambiri,+ chinthu chosiririka kwa inu,+ ndiponso chinthu chimene mumachichitira chifundo. Ana anu aamuna ndi aakazi amene munawasiya m’mbuyo adzaphedwa ndi lupanga.+ 22  Inu mudzachita zimene ine ndachita. Simudzaphimba ndevu zanu zapamlomo+ ndipo simudzadya chakudya chimene anthu adzakupatseni.+ 23  Mudzavala chovala chakumutu ndiponso nsapato zanu. Simudzadziguguda pachifuwa kapena kulira.+ Mudzawonda chifukwa cha zolakwa zanu+ ndipo mudzabuula pakati panu.+ 24  Ezekieli wakhala chizindikiro cholosera zam’tsogolo.+ Mudzachita zonse zimene iye wachita. Mudzachita zimenezo tsoka lanu likadzafika,+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”’”+ 25  “Koma iwe mwana wa munthu, ine ndidzawachotsera mpanda wawo wolimba, chinthu chokongola chimene amachinyadira. Ndidzawachotsera chinthu chosiririka m’maso mwawo+ ndi chokhumba cha moyo wawo, ndiponso ana awo aamuna ndi aakazi.+ 26  Kodi pa tsiku limenelo wothawa sadzabwera kwa iwe kuti adzanene zimene zachitika?+ 27  Pa tsiku limenelo udzatsegula pakamwa pako n’kulankhula ndi wothawayo+ ndipo sudzakhalanso chete.+ Choncho iwe udzakhala chizindikiro kwa iwo cholosera zam’tsogolo,+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+

Mawu a M'munsi