Ezekieli 23:1-49
23 Yehova anapitiriza kulankhula nane+ kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, panali akazi awiri, ana aakazi obadwa kwa mayi mmodzi.+
3 Akazi amenewa anayamba kuchita uhule m’dziko la Iguputo.+ Anayamba uhule umenewu ali atsikana ang’onoang’ono.+ Kumeneko amuna anafinya mabere awo+ ndi kutsamira chifuwa chawo ali anamwali.
4 Wamkulu dzina lake anali Ohola, wamng’ono anali Oholiba. Akazi amenewa anakhala anga+ ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.+ Ohola akuimira Samariya+ ndipo Oholiba akuimira Yerusalemu.+
5 “Ohola anayamba kuchita uhule+ ngakhale kuti anali mkazi wanga. Anali kulakalaka kwambiri amuna amene ankakhumba kugona naye.+ Anali kulakalaka Asuri+ amene anali kukhala moyandikana naye.
6 Anali kulakalaka abwanamkubwa ovala zovala zabuluu ndiponso ankalakalaka atsogoleri. Onsewa anali anyamata osiririka, asilikali okwera pamahatchi.
7 Iye anapitiriza kuchita zauhule zakezo ndi amuna onse osankhidwa a ku Asuri. Anadziipitsa ndi amuna onse amene anawakhumba ndiponso ndi mafano awo onyansa.+
8 Iye sanasiye zauhule zake zimene anachokera nazo ku Iguputo. Aiguputowo anagona naye kuyambira ali kamtsikana. Iwo ndiwo anatsamira chifuwa chake ali namwali ndipo anali kuchita naye zachiwerewere.+
9 Choncho ndinam’pereka m’manja mwa amuna amene anali kukhumba kugona naye.+ Ndinam’pereka m’manja mwa ana aamuna a ku Asuri amene iye anali kuwakhumba.+
10 Amuna amenewa ndiwo amene anamuvula.+ Iwo anatenga ana ake aamuna ndi aakazi+ ndipo iyeyo anamupha ndi lupanga. Iye anatchuka ndi khalidwe loipa pakati pa akazi ena ndipo iwo anamuweruza.
11 “Mng’ono wake Oholiba ataona zimenezi,+ anayamba kukonda chiwerewere chodziwononga nacho kuposa mkulu wake. Anayamba kuchita uhule kuposa dama la mkulu wake.+
12 Iye anali kulakalaka kwambiri ana aamuna a ku Asuri.+ Anali kulakalaka abwanamkubwa ndi atsogoleri amene anali kukhala moyandikana naye. Amuna onsewa anali ovala mwaulemerero, asilikali okwera pamahatchi komanso anyamata osiririka.+
13 Oholiba atadziipitsa, ine ndinaona kuti akazi onsewa anali ndi khalidwe lofanana.+
14 Iye anawonjezera zochita zake zauhule ataona zithunzi za amuna zogoba pakhoma,+ zithunzi+ za Akasidi zopaka utoto wofiira,+
15 zithunzi za amuna ovala malamba m’chiuno,+ ndiponso ovala nduwira zazitali zolendewera kumutu kwawo. Amuna onsewo anali kuoneka ngati ankhondo, komanso ngati ana aamuna a ku Babulo, obadwira m’dziko la Kasidi.
16 Ataona zithunzizo, anayamba kukhumba kwambiri amunawo+ ndipo anatumiza anthu ku Kasidi kuti akawaitane.+
17 Ana aamuna a ku Babulowo anali kubwera kwa iye. Anali kupita kubedi lake lochitirapo zachikondi ndi kumuipitsa ndi chiwerewere chawo.+ Iye anapitiriza kuipitsidwa ndi amunawo kenako ananyansidwa nawo n’kuwasiya.
18 “Oholiba anayamba kuchita uhule modzionetsera ndipo anali kudzivula,+ moti ine ndinasiya kukhala naye chifukwa chonyansidwa naye, monga mmene ndinasiyira mkulu wake chifukwa chonyansidwa naye.+
19 Oholiba anapitiriza kuwonjezera zochita zake zauhule+ mpaka kufika pokumbukira masiku amene anali kamtsikana,+ pamene anali kuchita uhule m’dziko la Iguputo.+
20 Iye anali ndi chilakolako champhamvu ngati cha adzakazi* amene amuna awo ali ndi ziwalo ngati za abulu amphongo, amuna amene mpheto zawo zili ngati mpheto za mahatchi amphongo.+
21 Iwe Oholiba, unapitiriza kulakalaka khalidwe lotayirira la pa utsikana wako mwa kufunafuna njira zoti amuna atsamire pachifuwa chako, kuyambira pamene unali ku Iguputo+ mpaka m’tsogolo. Unachita izi kuti ukhutiritse chilakolako cha mabere a utsikana wako.+
22 “Choncho iwe Oholiba, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndichititsa kuti amuna amene anali zibwenzi zako akuukire.+ Amenewa ndi amuna amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo. Ine ndidzawabweretsa kuti akuukire kuchokera kumbali zonse.+
23 Ndidzabweretsa ana aamuna a ku Babulo,+ Akasidi onse,+ amuna a ku Pekodi,+ a ku Sowa, a ku Kowa, pamodzi ndi ana aamuna a ku Asuri. Onsewa ndiwo anyamata osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri, amuna ankhondo, amuna ochita kusankhidwa ndi okwera pamahatchi.
24 Onsewa adzabwera kudzakuukira. Anthuwo pofika, padzamveka phokoso la magaleta* ankhondo ndi la mawilo.+ Iwo adzabwera ndi khamu la anthu, atatenga zishango zazikulu, zishango zazing’ono ndi zisoti. Iwo adzakuzungulira kuti akuukire. Ndidzawapatsa mphamvu zoweruza, ndipo adzakuweruza motsatira malamulo awo.+
25 Ndidzasonyeza ukali wanga pa iwe+ ndipo iwo adzakulanga mwaukali.+ Adzakuchotsa mphuno ndi makutu ndipo ziwalo zako zotsala adzazidula ndi lupanga. Iwo adzatenga+ ana ako aamuna ndi aakazi+ ndipo zinthu zako zotsala adzazitentha ndi moto.+
26 Adzakuvula zovala zako+ ndi kutenga zinthu zako zokongola.+
27 Ndithu, ine ndidzathetsa khalidwe lotayirira mwa iwe+ ndiponso uhule wako umene unachoka nawo kudziko la Iguputo.+ Sudzakwezanso maso ako kuyang’ana amuna a ku Iguputo ndipo dziko la Iguputo sudzalikumbukiranso.’
28 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Iwe ndikupereka m’manja mwa amuna amene wadana nawo, amuna amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo.+
29 Iwo adzakulanga mwaukali ndi kukutengera zinthu zonse zimene unazipeza movutikira ndipo adzakusiya wosavala ndi wamaliseche.+ Umaliseche umene unauonetsa pochita dama, khalidwe lako lotayirira, ndi zochita zako zauhule zidzaonekera poyera.+
30 Adzakuchitira zimenezi chifukwa chakuti wachita uhule ndi mitundu ina ya anthu+ komanso chifukwa chakuti wadziipitsa ndi mafano awo onyansa.+
31 Iwe wayenda m’njira ya mkulu wako+ ndipo ndidzakupatsa kapu yake.’+
32 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Udzamwa za m’kapu ya mkulu wako, kapu yaitali ndi yaikulu.+ Udzakhala chinthu choseketsa ndi chotonzedwa chifukwa m’kapumo muli zambiri.+
33 Udzaledzera kwambiri ndi kudzazidwa ndi chisoni. Udzaledzera ndi zinthu za m’kapu ya mkulu wako Samariya, zinthu zodabwitsa kwambiri ndi zowononga.
34 Iwe udzamwa ndi kugugudiza za m’kapuyo,+ ndipo udzatafuna zidutswa za kapuyo ndi kukhadzula mabere ako.+ “Ine ndanena,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’
35 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Popeza kuti wandiiwala+ ndi kundiponya kumbuyo,+ udzalangidwa chifukwa cha khalidwe lako lotayirira ndi zochita zako zauhule.’”
36 Yehova anandiuzanso kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi uweruza+ Ohola ndi Oholiba+ ndi kuwauza zinthu zonyansa zimene achita?+
37 Iwo achita chigololo+ ndipo m’manja mwawo muli magazi.+ Achita chigololo ndi mafano awo onyansa.+ Kuwonjezera apo, ana anga aamuna amene anandiberekera anawaponya pamoto kuti akhale chakudya cha mafanowo.+
38 Komanso anandichitira zinthu izi: Pa tsikulo anaipitsa+ malo anga opatulika+ ndiponso sabata langa.+
39 Atapha ana awo aamuna ndi kuwapereka kwa mafano onyansa,+ pa tsiku lomwelo anabwera kumalo anga opatulika ndi kuwadetsa.+ Izi ndi zimene achita m’nyumba yanga.+
40 Kuwonjezera apo, akaziwo atatumiza uthenga kwa amuna ochokera kutali, amuna amene anawatumizira uthengawo+ anabweradi.+ Iwe unasamba,+ n’kupaka zodzikongoletsera m’maso,+ ndi kuvala zodzikongoletsera kuti amuna amenewa akuone.+
41 Kenako unakhala pabedi pako,+ patsogolo pa tebulo loyalidwa bwino.+ Patebulopo unaikapo zofukiza zanga zonunkhira+ ndi mafuta anga.+
42 Kumeneko kunamveka phokoso la anthu amene akucheza mosaopa kanthu.+ Kuwonjezera pa amuna ambiri amene anali kubwera, panalinso zidakwa+ zochokera m’chipululu. Amuna amenewa anaveka akaziwo zibangili ndi zisoti zokongola zachifumu kumutu kwawo.+
43 “Kenako ndinalankhula zokhudza mkazi amene anatopa chifukwa cha chigololo+ kuti, ‘Komatu apitiriza kuchita uhulewo.’+
44 Amuna aja anapitiriza kubwera kwa iye monga mmene amuna amapitira kwa hule. Anapita kwa Ohola ndi Oholiba monga akazi akhalidwe lotayirira.+
45 Koma amuna olungama+ ndi amene adzam’patse chiweruzo chimene amapereka kwa akazi achigololo+ komanso chimene amapereka kwa akazi okhetsa magazi.+ Pakuti iwowa ndi akazi achigololo ndipo m’manja mwawo muli magazi.+
46 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Kudzabwera khamu la anthu kudzawaukira+ ndi kuwasandutsa chinthu chochititsa mantha komanso chinthu choyenera kutengedwa ndi adani.+
47 Khamu la anthulo lidzawaponya miyala+ ndi kuwapha ndi malupanga. Adzaphanso ana awo aamuna ndi aakazi+ ndi kutentha nyumba zawo.+
48 Ndithu ine ndidzathetsa khalidwe lotayirira+ m’dzikoli+ ndipo akazi onse adzatengerapo phunziro, moti sadzachita khalidwe lotayirira ngati lanu.+
49 Anthu amenewo adzakulangani chifukwa cha khalidwe lanu lotayirira+ komanso mudzalangidwa chifukwa cha machimo amene munachita ndi mafano anu onyansa. Anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”+