Ezekieli 20:1-49

20  M’chaka cha 7, m’mwezi wachisanu, pa tsiku la 10 la mweziwo, akuluakulu a Isiraeli anabwera kwa ine kudzafunsira kwa Yehova,+ ndipo anakhala pamaso panga.+  Ndiyeno Yehova analankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, lankhula ndi akuluakulu a Isiraeliwo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi amuna inu mwabweradi kudzafunsira kwa ine?+ ‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindilola kuti inu mufunsire kwa ine,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’  “Kodi ndiwe wokonzeka kuwaweruza? Kodi uwaweruza, iwe mwana wa munthu?+ Auze zinthu zonyansa zimene makolo awo anachita.+  Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pa tsiku limene ndinasankha Isiraeli,+ ndinakweza mkono wanga+ polumbirira mbewu ya nyumba ya Yakobo+ ndi kuwachititsa kuti andidziwe m’dziko la Iguputo.+ Inde, ndinakweza mkono wanga ndi kuwalumbirira kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’+  Pa tsiku limenelo ndinakweza dzanja langa+ powalumbirira kuti ndidzawatulutsa m’dziko la Iguputo kupita nawo kudziko limene ndinaliyendera kuti iwo akakhalemo, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Linali dziko lokongola kwambiri kuposa mayiko onse.+  Ine ndinawauza kuti, ‘Aliyense wa inu ataye zinthu zake zonyansa zimene amaziyang’anitsitsa pozilambira+ ndipo musadziipitse ndi mafano onyansa a ku Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’+  “‘“Koma iwo anayamba kundipandukira+ ndipo sanafune kundimvera. Aliyense wa iwo sanataye zinthu zonyansa zimene anali kuziyang’anitsitsa pozilambira ndipo sanasiye mafano onyansa a ku Iguputo.+ Choncho ine ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga kuti ukali wanga uthere pa iwo m’dziko la Iguputo.+  Koma ine ndinachita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina amene iwo anali kukhala pakati pawo,+ pakuti ndinawachititsa kuti andidziwe pamaso pa anthu a mitundu inawo powatulutsa m’dziko la Iguputo.+ 10  Chotero ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo ndi kuwalowetsa m’chipululu.+ 11  “‘“Kumeneko ndinawapatsa malamulo+ ndi kuwadziwitsa zigamulo zanga,+ kuti munthu amene akuzitsatira akhalebe ndi moyo.+ 12  Ndinawapatsanso sabata langa+ kuti likhale chizindikiro pakati pa ine ndi iwowo.+ Ndinachita zimenezi n’cholinga choti adziwe kuti ine Yehova, ndiye amene ndikuwapatula. 13  “‘“Koma iwowo, a nyumba ya Isiraeli, anandipandukira m’chipululu.+ Iwo sanayende motsatira malamulo anga+ ndipo anakana zigamulo zanga+ zimene munthu akamazitsatira, amakhala ndi moyo.+ Sabata langa analidetsa kwambiri,+ moti ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga m’chipululu kuti ndiwafafanize.+ 14  Koma ndinachita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa mitundu ya anthu amene anaona ndikutulutsa anthu anga pakati pawo.+ 15  Ine ndinakweza dzanja langa powalumbirira m’chipululu+ kuti sindidzawalowetsa m’dziko limene ndinawapatsa, dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ (dziko lokongola kwambiri kuposa mayiko onse)+ 16  chifukwa anakana zigamulo zanga, sanayende motsatira malamulo anga, anadetsa sabata langa komanso mtima wawo unali pa mafano awo onyansa.+ 17  “‘“Maso anga anayamba kuwamvera chisoni kuti ndisawawononge,+ chotero sindinawafafanize m’chipululu. 18  Choncho ndinauza ana awo m’chipululu kuti,+ ‘Musayende motsatira malamulo a makolo anu,+ ndipo musasunge zigamulo zawo.+ Musadziipitse ndi mafano awo onyansa.+ 19  Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ Yendani motsatira malamulo anga+ ndipo musunge zigamulo zanga+ ndi kuzitsatira.+ 20  Muzisunga sabata langa kuti likhale lopatulika+ ndipo likhale chizindikiro pakati pa ine ndi inu, kuti mudziwe kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’+ 21  “‘“Koma anawo anayamba kundipandukira.+ Sanayende motsatira malamulo anga ndipo sanasunge ndi kutsatira zigamulo zanga, zimene ngati munthu atazitsatira angakhale ndi moyo.+ Iwo anadetsa sabata langa,+ choncho ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga, kuti ukali wanga uthere pa iwo m’chipululu.+ 22  Ine ndinabweza dzanja langa+ ndi kuchita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa mitundu ya anthu amene anaona ndikutulutsa anthu anga pakati pawo.+ 23  Komanso ndinakweza dzanja langa powalumbirira m’chipululu,+ kuti ndidzawabalalitsira ku mitundu ya anthu ndi kuwamwazira m’mayiko osiyanasiyana,+ 24  chifukwa chakuti sanatsatire zigamulo zanga,+ anakana malamulo anga,+ anadetsa sabata langa+ komanso maso awo anali pa mafano onyansa a makolo awo.+ 25  Chifukwa cha zimenezi ine ndinawalola kutsatira malamulo oipa ndi zigamulo zimene sizikanawathandiza kukhala ndi moyo.+ 26  Ndinawalola kudziipitsa ndi mphatso zawo pamene anali kuponya pamoto* mwana aliyense woyamba kubadwa.+ Ndinachita zimenezi kuti ndiwasautse n’cholinga choti adziwe kuti ine ndine Yehova.”’+ 27  “Choncho iwe mwana wa munthu, lankhula ndi nyumba ya Isiraeli ndipo uwauze kuti,+ ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Makolo anu anandilankhulira mawu onyoza pamene anali kundichitira zinthu mosakhulupirika.+ 28  Komabe ine ndinawalowetsa m’dziko+ limene ndinawalumbirira nditakweza dzanja langa kuti ndidzawapatsa.+ Koma ataona phiri lililonse lalitali+ ndi mtengo uliwonse wanthambi zambiri, anayamba kupereka nsembe zawo pamenepo+ ndi zopereka zawo zochititsa mseru. Analinso kufukiza nsembe zafungo lokhazika mtima pansi+ ndi kuthira nsembe zawo zachakumwa pamalo amenewo.+ 29  Choncho ndinawafunsa kuti, ‘Kodi malo okwezekawa ndi a chiyani? Kodi mumachitako chiyani kumeneko kuti malowo azitchedwa kuti Malo Okwezeka mpaka lero?’”’+ 30  “Tsopano uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi anthu inu mukudziipitsa potsatira njira za makolo anu?+ Kodi mukutsatira zinthu zawo zonyansa ndi kuchita zachiwerewere ndi mafano amenewo?+ 31  Kodi mukudziipitsa polemekeza mafano anu onse onyansa mpaka lero,+ popereka mphatso zanu mwa kuponya pamoto ana anu aamuna?+ Kodi pa nthawi imodzimodziyo ndilole kuti mufunsire kwa ine, inu anthu a nyumba ya Isiraeli?”’+ “‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindilola kuti mufunsire kwa ine,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 32  ‘Ndithu zimene mukuganiza+ sizichitika.+ Inu mukunena kuti: “Tiyeni tikhale ngati anthu a mitundu ina. Tikhale ngati mabanja a m’mayiko ena+ potumikira mitengo ndi miyala.”’”+ 33  “‘Pali ine Mulungu wamoyo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘ndidzakhala mfumu yanu ndipo ndidzakulamulirani ndi dzanja lamphamvu, mkono wotambasula+ ndi mkwiyo wosefukira.+ 34  Ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ya anthu ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kumayiko amene munabalalikirako. Ndidzakusonkhanitsani ndi dzanja lamphamvu, mkono wotambasula ndi mkwiyo wosefukira.+ 35  Ndidzakulowetsani m’chipululu cha mitundu ya anthu+ ndipo kumeneko ndidzatsutsana nanu pamasom’pamaso.+ 36  “‘Monga mmene ndinatsutsirana ndi makolo anu m’chipululu cha dziko la Iguputo,+ ndidzatsutsananso ndi inu,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 37  ‘Ndidzakudutsitsani pansi pa ndodo ya m’busa+ ndi kuchita nanu pangano lolimba.+ 38  Ndidzachotsa pakati panu anthu ondipandukira ndi ondichimwira.+ Pakuti ndidzawatulutsa m’dziko limene akukhalamo monga alendo, koma sadzalowa m’dziko la Isiraeli,+ ndipo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+ 39  “Inu a nyumba ya Isiraeli, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pitani, aliyense wa inu akatumikire mafano ake onyansawo.+ Pambuyo pake, ngati simundimvera ndidzakusiyani ndipo simudzadetsanso dzina langa loyera ndi mphatso zanu ndiponso mafano anu onyansa.’+ 40  “‘Nyumba yonse ya Isiraeli idzanditumikira m’phiri langa loyera,+ phiri lalitali la m’dziko la Isiraeli,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Kumeneko ndidzasangalala nawo ndipo ndidzafuna zopereka zanu ndi nsembe zanu za zinthu zoyambirira kucha pa zinthu zanu zonse zopatulika.+ 41  Ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukusonkhanitsani pamodzi kuchokera m’mayiko osiyanasiyana kumene munabalalikira,+ ndidzasangalala nanu chifukwa cha nsembe zanu zafungo lokhazika mtima pansi,+ ndipo ndidzakhala woyera chifukwa cha inu pamaso pa anthu a mitundu ina.’+ 42  “‘Ndikadzakulowetsani m’dziko la Isiraeli,+ dziko limene ndinalumbira nditakweza dzanja kuti ndidzalipereka kwa makolo anu, anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 43  Ndithu kumeneko mudzakumbukira njira zanu+ ndi zochita zanu zonse zimene munali kudziipitsa nazo.+ Mukadzakumbukira zimenezi, mudzachita manyazi ochita kuonekera pankhope zanu chifukwa cha zoipa zonse zimene munachita.+ 44  Ndikadzachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa,+ inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ Inu a nyumba ya Isiraeli, ine sindidzachitapo kanthu mogwirizana ndi njira zanu zoipa kapena zochita zanu zosayenera,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 45  Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 46  “Iwe mwana wa munthu, yang’ana+ ku mbali ya kum’mwera ndipo ulankhule+ mawu onena za kumeneko. Ulosere kunkhalango ya dziko la kum’mwera. 47  Uuze nkhalango ya kum’mwerayo kuti, ‘Imva mawu a Yehova. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikukuyatsa moto.+ Motowo unyeketsa mtengo uliwonse wauwisi ndi mtengo uliwonse wouma.+ Malawi a motowo sadzatheka kuwazimitsa,+ ndipo nkhope zonse,* kuchokera kum’mwera mpaka kumpoto zidzapsa ndi moto.+ 48  Anthu onse adzaona kuti ine Yehova ndaiyatsa moto nkhalangoyo ndipo sudzatheka kuuzimitsa.”’”+ 49  Ine ndinanena kuti: “Kalanga ine, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Iwo akundinena kuti, ‘Kodi si miyambi imene akunenayi?’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “anadutsitsa pamoto.”
Kapena kuti “nthaka yonse ya dziko lapansi.”