Ezekieli 2:1-10

2  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu,+ imirira kuti ndikulankhule.”+  Atayamba kulankhula nane, mzimu unalowa mwa ine+ ndipo unandiimiritsa kuti ndimvetsere yemwe anali kulankhula ndi ineyo.+  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ndikukutumiza kwa ana a Isiraeli,+ kwa mitundu yopanduka imene yandipandukira.+ Iwo ndi makolo awo akhala akuphwanya malamulo anga mpaka lero.+  Ndikukutumiza kwa ana a nkhope zamwano+ ndi amakani,*+ ndipo ukawauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’  Kaya iwowo akamvetsera+ kapena ayi,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka,+ adzadziwabe kuti pakati pawo panali mneneri.+  “Iwe mwana wa munthu, usawaope.+ Usaope mawu awo ngakhale kuti iwo ndi anthu osamva+ ndipo ali ngati zinthu zokulasa.+ Usaope, ngakhale kuti ukukhala pakati pa zinkhanira.+ Usaope mawu awo+ ndipo usachite mantha ndi nkhope zawo,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.+  Ukawauze mawu anga, kaya akamva kapena ayi, pakuti iwo ndi anthu opanduka.+  “Iwe mwana wa munthu, imva zimene ndikukuuza. Usapanduke ngati nyumba yopandukayi.+ Tsegula pakamwa pako kuti udye zimene ndikukupatsa.”+  Ndili mkati moyang’ana, ndinangoona dzanja litatambasukira kwa ine.+ M’dzanjalo munali mpukutu wolembedwa.+ 10  Iye anautambasula pamaso panga, ndipo unalembedwa kuseri n’kuseri.+ Mumpukutumo munalembedwa nyimbo zoimba polira, mawu odandaula ndi mawu olira.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “anthota.”