Ezekieli 19:1-14

19  “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira+ yokhudza atsogoleri a Isiraeli.+  Unene kuti, ‘Kodi mayi anu anali ndani? Anali mkango waukazi pakati pa mikango ina.+ Mkango waukaziwo unali kugona pakati pa mikango yamphamvu yamphongo, ndipo unalera ana ake.  “‘Patapita nthawi, mkangowo unalera mwana wake mmodzi mpaka kukula.+ Mwanayo anakhala mkango wamphamvu wamphongo. Anaphunzira kupha nyama+ ndipo anayamba kudya ngakhale anthu.  Mitundu ya anthu inali kumva za mkangowo. Kenako unagwera m’mbuna zawo ndipo anaukola ndi ngowe n’kupita nawo ku Iguputo.+  “‘Mkango waukazi uja utaona kuti wadikira popanda chilichonse chochitika, ndipo palibenso chiyembekezo chilichonse, unatenganso mwana wake wina.+ Unalera mwanayo mpaka kukhala mkango wamphamvu.  Mkangowo unayamba kuyendayenda pakati pa mikango ina. Unakhaladi mkango wamphamvu wamphongo. Pang’onopang’ono unaphunzira kupha nyama+ ndipo unayamba kudya ngakhale anthu.+  Mkango wamphongowo unadziwa nsanja zokhalamo anthu ndipo unawononga mizinda yawo.+ Chotero dzikolo linakhala bwinja moti munkangomveka kubangula kwa mkangowo.+  Mitundu ya anthu a m’zigawo zonse zozungulira anabwera kudzauukira.+ Anauponyera ukonde+ wawo ndipo mkangowo unagwera m’mbuna zawo.+  Kenako anaukola ndi ngowe n’kuuika m’kakhola ndi kupita nawo kwa mfumu ya Babulo.+ Anapita nawo ataukulunga ndi ukonde wosakira kuti mawu ake asamvekenso m’mapiri a ku Isiraeli.+ 10  “‘Mayi anu+ anali ngati mtengo wa mpesa*+ wobzalidwa m’mphepete mwa madzi. Mtengowo unali kubereka zipatso ndipo unali ndi nthambi zambiri chifukwa unali pamadzi ambiri.+ 11  Nthambi za mtengowo zinakhala zolimba zoyenera kupangira ndodo zachifumu za olamulira.+ Patapita nthawi, mtengowo unatalika kwambiri kuposa mitengo ina, ndipo unali kuonekera patali chifukwa cha kutalika kwake ndi kuchuluka kwa masamba ake.+ 12  Koma pamapeto pake, mtengowo unazulidwa ndi manja aukali+ n’kuponyedwa pansi. Kenako kunabwera mphepo ya kum’mawa n’kuumitsa zipatso zake.+ Ndodo yake yolimba inathyoledwa n’kuuma+ ndipo inanyeka ndi moto.+ 13  Tsopano mtengo wa mpesawo wabzalidwa m’chipululu,+ m’dziko lopanda madzi ndi louma.+ 14  Kenako moto unatuluka m’ndodo yake+ n’kunyeketsa nthambi zake ndi zipatso zake, ndipo mtengowo unalibenso ndodo yolimba yachifumu.+ “‘Imeneyi ndi nyimbo yoimba polira ndipo idzakhala nyimbo yotchuka.’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni m’Chiheberi ndi, “mtengo wa mpesa umene uli m’magazi anu.”