Ezekieli 18:1-32

18  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Kodi mukutanthauza chiyani mukamanena mwambi m’dziko la Isiraeli wakuti, ‘Bambo ndi amene amadya mphesa zosapsa koma mano a ana awo ndiwo amayayamira’?+  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, simudzanenanso mwambi umenewu mu Isiraeli.  Tamverani! Miyoyo yonse ndi yanga.+ Moyo+ wa bambo komanso moyo wa mwana, yonse ndi yanga.+ Moyo umene ukuchimwawo+ ndi umene udzafe.+  “‘Munthu akakhala wolungama n’kumachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo,+  ngati sadya+ zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano m’mapiri,+ ngati sakweza maso ake kuyang’ana mafano onyansa a nyumba ya Isiraeli,+ ngati saipitsa mkazi wa mnzake,+ ngati sayandikira mkazi amene wadetsedwa,+  ngati sazunza munthu aliyense,+ ngati amabweza chikole kwa munthu amene anakongola zinthu zake,+ ngati salanda zinthu za ena mwauchifwamba,+ ngati amapatsa munthu wanjala chakudya+ ndi kuphimba munthu wamaliseche ndi chovala,+  ngati salandira chiwongoladzanja akabwereketsa zinthu,+ ndiponso sakongoza zinthu mwa katapira,*+ ngati sachita zopanda chilungamo,+ ngati amachita chilungamo chenicheni poweruza munthu ndi mnzake,+  ngati akuyendabe m’malamulo anga+ ndi kusunga zigamulo zanga kuti azichita mogwirizana ndi choonadi,+ ndiye kuti munthu wotero ndi wolungama.+ Ndithu adzakhalabe ndi moyo,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 10  “‘Munthu akabereka mwana wamwamuna, mwanayo n’kukhala wakuba,+ wokhetsa magazi,+ ndipo amachita chilichonse cha zinthu zimenezi, 11  (koma bamboyo sanachitepo chilichonse mwa zinthu zimenezi), ngati mwanayo amadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano m’mapiri+ ndipo amaipitsa mkazi wa mnzake,+ 12  ngati amazunza munthu wosautsika ndi wosauka,+ ngati amalanda zinthu za ena mwauchifwamba,+ ngati sabweza chikole,+ ngati amakweza maso ake kuyang’ana mafano onyansa,+ ndiye kuti wachita chinthu chonyansa.+ 13  Iye amakongoza zinthu zake mwa katapira+ ndipo amalandira chiwongoladzanja.+ Ndithudi iye sadzakhala ndi moyo chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi.+ Adzaphedwa ndithu, ndipo magazi ake adzakhala pamutu pake.+ 14  “‘Ndiyeno munthu wina wabereka mwana wamwamuna amene amaona machimo onse amene bambo ake amachita. Mwanayo amaona machimowo koma sawachita.+ 15  Iye sadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano m’mapiri. Sakweza maso ake kuyang’ana mafano onyansa a nyumba ya Isiraeli+ ndipo sanaipitsepo mkazi wa mnzake.+ 16  Sanazunzepo munthu aliyense.+ Sanatengepo chikole+ ndipo sanalandepo chilichonse mwauchifwamba.+ Munthu wanjala amam’patsa chakudya+ ndipo munthu wamaliseche amam’phimba ndi chovala.+ 17  Iye sapondereza munthu wosautsika. Sakongoza zinthu mwa katapira+ ndipo salandira chiwongoladzanja.+ Amatsatira zigamulo zanga+ ndi kuyenda motsatira malamulo anga.+ Munthu wotere sadzafa chifukwa cha zolakwa za bambo ake.+ Adzakhalabe ndi moyo.+ 18  Koma bambo akewo, adzafa chifukwa cha zolakwa zawo,+ popeza anabera anthu mwachinyengo,+ anabera m’bale wawo zinthu mwauchifwamba+ ndipo anachita choipa chilichonse pakati pa anthu a mtundu wawo.+ 19  “‘Anthu inu mudzanena kuti: “N’chifukwa chiyani mwanayo alibe mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo ake?”+ Mwanayo anachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo.+ Iye anasunga malamulo anga ndipo akupitiriza kuwatsatira.+ Ndithudi adzakhalabe ndi moyo.+ 20  Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.+ Mwana sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo ake. Bambo sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za mwana wake.+ Chilungamo cha munthu wolungama chidzakhala pa iye,+ ndipo zoipa za munthu woipa zidzakhala pamutu pa woipayo.+ 21  “‘Munthu woipa akabwerera, kusiya machimo ake onse amene anali kuchita+ ndipo akasunga malamulo anga onse n’kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo,+ adzakhalabe ndi moyo. Sadzafa ayi.+ 22  Zolakwa zonse zimene anachita sizidzakumbukiridwa ndipo sadzalangidwa nazo.+ Adzakhalabe ndi moyo chifukwa cha zinthu zolungama zimene anachita.’+ 23  “‘Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu aliyense wochimwa?+ Kodi sindisangalala kuti munthu wochimwayo abwerere kusiya njira zakezo ndi kukhalabe ndi moyo?’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 24  “‘Munthu wolungama akasiya chilungamo chake n’kumachita zinthu zopanda chilungamo,+ akamachita zopanda chilungamo+ n’kumakhalabe ndi moyo, zinthu zolungama zonse zimene anachita sizidzakumbukiridwa.+ Iye adzafa chifukwa chochita zinthu mosakhulupirika ndiponso chifukwa cha machimo ake amene anachita.+ 25  “‘Anthu inu mudzanena kuti: “Njira za Yehova n’zopanda chilungamo.”+ Tamverani inu a nyumba ya Isiraeli. Kodi njira zanga ndiye zopanda chilungamo?+ Kodi njira za anthu inu sindizo zopanda chilungamo?+ 26  “‘Munthu wolungama akasiya chilungamo chake n’kumachita zinthu zopanda chilungamo+ n’kufa chifukwa cha zochita zakezo, wafa chifukwa cha zochita zake zopanda chilungamo.+ 27  “‘Munthu woipa akasiya zinthu zoipa zimene anali kuchita n’kumachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo,+ iyeyu adzapulumutsa moyo wake.+ 28  Munthu woipayo akaona+ zoipa zimene anali kuchita n’kuzisiya,+ adzakhalabe ndi moyo. Sadzafa ayi.+ 29  “‘Ndithu nyumba ya Isiraeli idzanena kuti: “Njira za Yehova n’zopanda chilungamo.”+ Kodi njira zanga ndiye zopanda chilungamo, inu a nyumba ya Isiraeli?+ Kodi njira za anthu inu sindizo zopanda chilungamo?’+ 30  “‘Chotero ine ndidzaweruza aliyense wa inu malinga ndi njira zake,+ inu a nyumba ya Isiraeli,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ ‘Lapani ndi kusiya zolakwa zanu zonse+ ndipo musalole kuti chilichonse chizikupunthwitsani ndi kukulakwitsani.+ 31  Tayani zolakwa zanu zonse zimene munachita+ ndipo muyesetse kukhala ndi mtima watsopano+ ndiponso mzimu watsopano.+ Kodi muferenji+ inu a nyumba ya Isiraeli?’ 32  “‘Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Choncho tembenukani anthu inu, kuti mukhale ndi moyo.’”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 22:25.