Ezekieli 17:1-24

17  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, phera nyumba ya Isiraeli mwambi+ ndipo uwauze mawu ophiphiritsa.+  Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ku Lebanoni+ kunabwera chiwombankhanga chachikulu+ chokhala ndi mapiko aakulu+ ndi aatali. Chiwombankhangacho chinali ndi nthenga zambiri zamitundu yosiyanasiyana. Chitafika kumeneko, chinathyola nsonga ya mtengo+ wa mkungudza.+  Chiwombankhangacho chinathyola nsonga yapamwamba penipeni pa nthambi zanthete, n’kupita nayo kudziko la Kanani.+ Kumeneko chinakabzala nsonga ya mkungudzayo mumzinda wa anthu ochita malonda.  Kenako chinatenga zina mwa mbewu za m’dzikomo+ ndi kuzibzala m’munda wolimidwa bwino. Chinabzala nsonga ya mkungudza ija ngati mtengo wa msondodzi umene uli m’mphepete mwa madzi ambiri.+  Nsonga ya mkungudza ija inayamba kuphuka n’kukhala mtengo wa mpesa waufupi+ wamasamba ambiri. Nthambi za mtengowo sizinali kukulira m’mbali ndipo unaphuka mizu pansi pake. Pomalizira pake nsongayo inakhala mtengo wa mpesa ndipo inaphuka ndi kuchita nthambi.+  “‘“Kenako kunabwera chiwombankhanga china chachikulu+ chokhala ndi mapiko aakulu anthenga zikuluzikulu.+ Ndiyeno mwanjala, mtengo wa mpesawo unatambasula mizu yake ndi nthambi zake kuchokera pamene unabzalidwa kukafika pamene panali chiwombankhangacho+ kuti chithirire mtengowo.+  Koma mtengowo anali ataubzala m’munda wabwino, m’mphepete mwa madzi ambiri,+ kuti uchite nthambi ndi kubereka zipatso n’kukhala mtengo waukulu wa mpesa.”’  “Ndiyeno unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi mtengo umenewu zinthu zidzauyendera bwino?+ Kodi munthu wina sadzadula mizu yake+ ndi kuwononga zipatso zake? Kodi mphukira zake zimene zangothyoledwa kumene sizidzauma?+ Mtengowo udzauma ndithu. Sudzachita kufuna dzanja lamphamvu kapena anthu ambiri kuti uzulidwe ndi mizu yomwe. 10  Ngakhale kuti mtengowo anautenga pamalo ena n’kukaubzala pamalo ena, kodi zinthu zidzauyendera bwino? Kodi sudzaumiratu ukadzawombedwa ndi mphepo ya kum’mawa?+ Udzauma ndithu pamalo amene unabzalidwapo.”’”+ 11  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 12  “Chonde, uza nyumba yopandukayi+ kuti, ‘Kodi anthu inu simukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?’ Auze kuti, ‘Mfumu ya Babulo inabwera ku Yerusalemu n’kudzatenga mfumu+ ndi akalonga a mumzindawo ndi kupita nawo ku Babulo.+ 13  Kuwonjezera apo, inatenga mmodzi wa mbewu yachifumu+ n’kuchita naye pangano ndi kumulumbiritsa.+ Mfumuyo inatenga atsogoleri a m’dzikolo n’kupita nawo kwawo,+ 14  kuti ufumuwo ukhale waung’ono, usakule,+ komanso kuti ukhalepobe mwa kusunga pangano limene anachita.+ 15  Koma iye anapandukira+ mfumuyo potumiza amithenga ku Iguputo kuti dziko la Iguputo limupatse mahatchi*+ ndi khamu la anthu. Kodi zinthu zidzamuyendera bwino? Kodi munthu amene akuchita zinthu zimenezi ndiponso amene akuphwanya pangano adzapulumuka? Kodi iye adzapulumukadi?’+ 16  “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, “Pali ine Mulungu wamoyo,+ munthu amene ananyoza lumbiro+ ndi kuphwanya pangano limene anachita ndi mfumu imene inamulonga ufumu, adzafera m’dziko la mfumu yomweyo, dziko la Babulo.+ 17  Farao sadzamutumizira gulu lalikulu la asilikali ndi khamu la anthu kuti amuthandize pankhondo.+ Sadzamuthandiza mwa kumanga chiunda chomenyerapo nkhondo ndiponso mpanda womenyerapo nkhondo n’cholinga chakuti aphe anthu ambiri.+ 18  Ngakhale kuti anatambasula dzanja lake+ povomereza lumbiro, iye wanyoza lumbiro+ limenelo mwa kuphwanya pangano. Iye wachita zinthu zonsezi ndipo sadzapulumuka.”’+ 19  “‘Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndidzamulanga ndithu chifukwa cha lumbiro langa limene walinyoza+ ndiponso pangano langa limene waliphwanya. 20  Ndidzam’ponyera ukonde wanga ndipo adzakodwa mu ukonde wanga wosakira.+ Ndiyeno ndidzamubweretsa ku Babulo ndi kumuweruza chifukwa chondichitira zinthu mosakhulupirika.+ 21  Gulu lonse la asilikali ake amene anathawa, lidzaphedwa ndi lupanga. Amene adzapulumuke adzabalalikira ku mphepo zonse.+ Anthu inu mudzadziwa kuti ine Yehova ndi amene ndanena zimenezi.”’+ 22  “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inenso ndidzathyola nsonga ya pamwamba penipeni pa mtengo wa mkungudza.+ Ndidzabudula nsonga yanthete kunthambi zake+ ndipo ndidzaibzala pamwamba pa phiri lalitali.+ 23  Ndidzaibzala pamwamba pa phiri lalitali la ku Isiraeli+ ndipo idzachita nthambi ndi kubereka zipatso+ n’kukhala mtengo waukulu wa mkungudza.+ Mbalame zamitundu yonse zizidzakhala pansi pa mtengowo ndi mumthunzi wa masamba ake.+ 24  Mitengo yonse yamthengo idzadziwa kuti ine Yehova+ ndatsitsa mtengo waukulu+ ndi kukweza mtengo wonyozeka,+ ndaumitsa mtengo wauwisi+ ndi kuchititsa maluwa mtengo umene unali wouma. Ine Yehova ndanena ndi kuchita zimenezi.”’”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”