Ezekieli 16:1-63

16  Yehova analankhula nanenso kuti:  “Iwe mwana wa munthu, uza+ Yerusalemu za zinthu zake zonyansa.+  Umuuze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akunena kwa iwe Yerusalemu kuti: “Iwe unachokera kudziko la Akanani ndipo unabadwira komweko.+ Bambo ako anali Muamori,+ mayi ako anali Mhiti.+  Pa tsiku limene unabadwa,+ chingwe chako cha pamchombo sichinadulidwe. Sanakusambitse kuti uyere, sanakupake mchere ndiponso sanakukulunge munsalu.  Palibe diso limene linakumvera chisoni kuti likuchitire chimodzi mwa zinthu zimenezi chifukwa chochita nawe chifundo.+ Koma tsiku limene unabadwa, unaponyedwa pansi chifukwa anthu ananyansidwa nawe.  “‘“Kenako ine ndinadutsa pafupi nawe ndipo ndinakuona ukuponyaponya timiyendo tako m’mwamba uli m’magazi ako. Ndiyeno ndinakuuza uli m’magazi akowo kuti, ‘Khalabe ndi moyo!’+ Ndithu ndinakuuza uli m’magazi akowo kuti, ‘Khalabe ndi moyo!’  Ndinakusandutsa khamu lalikulu ngati udzu wophuka m’munda kuti ukule ndi kutalika,+ ndiponso kuti uvale zodzikongoletsera zabwino kwambiri.+ Mabere ako awiri anakula bwino ndipo tsitsi lako linakula kwambiri udakali wosavala ndiponso wamaliseche.”’  “‘Ndinadutsa pafupi nawe n’kukuona, ndipo ndinaona kuti inali nthawi yako yoti uchite zachikondi.+ Chotero ndinakuphimba ndi chovala changa+ ndipo ndinabisa maliseche ako. Ndinakulumbirira n’kuchita nawe pangano+ ndipo unakhala wanga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.  ‘Komanso ndinakusambitsa.+ Ndinatsuka magazi ako n’kukudzoza mafuta.+ 10  Kenako ndinakuveka chovala cha nsalu yopeta+ ndi nsapato za chikopa cha katumbu.*+ Ndinakukulunga munsalu zabwino kwambiri+ n’kukufunditsa nsalu zamtengo wapatali. 11  Ndinakuvekanso zokongoletsera ndi zibangili+ m’manja mwako ndipo ndinakuveka mkanda+ m’khosi mwako. 12  Ndinakuveka ndolo ya pamphuno+ ndi ndolo za m’makutu*+ ndiponso chisoti chokongola pamutu pako.+ 13  Unali kuvala zinthu zagolide ndi zasiliva ndiponso nsalu zabwino kwambiri. Unali kuvala nsalu zamtengo wapatali ndi chovala cha nsalu yopeta.+ Unkadya ufa wosalala, uchi, ndi mafuta+ ndipo unakhala chiphadzuwa. Patapita nthawi unakhala woyenera ufumu.’”+ 14  “‘Dzina lako linatchuka pakati pa mitundu ya anthu chifukwa cha kukongola kwako, pakuti linali labwino kwambiri chifukwa cha ulemerero wanga umene ndinaika pa iwe,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 15  “‘Koma unayamba kudalira kukongola kwako+ ndipo unakhala hule chifukwa cha kutchuka kwa dzina lako.+ Unayamba kuchita uhule mosadziletsa ndi munthu aliyense wodutsa m’njira.+ Kukongola kwako unakupereka kwa anthu odutsawo. 16  Unatenga zovala zako zina n’kupangira malo okwezeka+ okhala ndi mitundu yosiyanasiyana ndipo unayamba kuchitirapo uhule.+ Zoterezi siziyenera kuchitika. Zisamachitike ayi. 17  Unali kutenga zinthu zako zokongola zochokera pagolide ndi siliva wanga amene ndinakupatsa+ n’kupangira zifaniziro za munthu wamwamuna+ n’kumachita nazo uhule.+ 18  Unali kutenganso zovala zako za nsalu yopeta n’kuphimbira zifanizirozo. Komanso unkaika mafuta anga ndi zonunkhiritsa zanga+ pamaso pa zifanizirozo. 19  Ndinakupatsa chakudya choti uzidya. Ndinakupatsa ufa wosalala, mafuta, ndi uchi.+ Koma zinthu zimenezi, iwe unaziika pamaso pa zifanizirozo kuti zikhale fungo lokhazika mtima pansi,+ ndipo unapitiriza kuchita zimenezi,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 20  “‘Unali kutenga ana ako aamuna ndi aakazi amene unandiberekera+ n’kumawapereka nsembe kwa mafano.+ Kodi zochita zako zauhulezo sizinakukwanire? 21  Iwe unali kupha ana anga,+ ndipo unali kuwapereka nsembe kwa mafano mwa kuwaponya pamoto.+ 22  M’zonyansa zako zonse ndi m’zochita zako zauhule sunakumbukire masiku a ubwana wako pamene unali wosavala ndi wamaliseche, pamene unali kuponyaponya timiyendo tako m’mwamba uli m’magazi ako.+ 23  (“Tsoka, tsoka kwa iwe,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.) Ndiyeno pambuyo pa zoipa zako zonse, 24  unadziunjikira mulu wa dothi ndipo unadzikonzera malo okwera m’bwalo lililonse la mzinda.+ 25  Unamanga malo ako okwerawo pamphambano iliyonse ya msewu+ ndipo unaipitsa kukongola kwako.+ Unayamba kukhanyulira munthu aliyense wodutsa+ n’kumachulukitsa zochita zako zauhule.+ 26  Unayamba kuchita uhule ndi ana aamuna a Iguputo,+ anthu a ziwalo zikuluzikulu amene ukukhala nawo pafupi.+ Unapitiriza kuwonjezera uhule wako kuti undikwiyitse. 27  Tsopano ine ndidzakutambasulira dzanja langa+ ndipo ndidzakuchepetsera gawo lako.+ Ndidzakupereka ku zilakolako+ za akazi odana nawe,+ ana aakazi a Afilisiti,+ akazi amene akuchita manyazi ndi khalidwe lako lotayirira.+ 28  “‘Unachitanso uhule ndi ana aamuna a Asuri chifukwa chakuti sunali kukhutira.+ Unapitiriza kuchita nawo uhule koma sunakhutirebe. 29  Unawonjezera kuchita zauhule ndi dziko la Kanani+ ndiponso Akasidi.+ Ngakhale amenewanso sunakhutiritsidwe nawo. 30  Tsopano iweyo wandikwiyitsa koopsa+ chifukwa cha zonse zimene wakhala ukuchitazi. Wakhala ukuchita ntchito za hule+ lopanda m’manyazi omwe,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 31  ‘Ngakhale kuti unaunjika mulu wako wadothi pamphambano m’misewu, komanso unapanga malo okwera m’bwalo lililonse la mzinda, unakhala wosiyana ndi hule chifukwa sunkafuna kulipidwa. 32  Mkazi amene amachita chigololo amatenga amuna achilendo m’malo mwa mwamuna wake.+ 33  Nthawi zambiri anthu amapatsa mahule mphatso,+ koma iweyo umapereka mphatso kwa zibwenzi zako zonse.+ Umawapatsa chiphuphu kuti abwere kwa iwe kuchokera kumalo onse ozungulira kuti adzachite nawe zauhule.+ 34  Iweyo umachita zosiyana ndi akazi ena pa uhule wako, ndipo palibenso amene amachita uhule wofanana ndi wako, womapereka malipiro pamene iweyo sunalipidwe. Choncho iwe ukuchita zosiyana ndi anzako.’ 35  “Chotero hule iwe,+ imva mawu a Yehova.+ 36  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Popeza wasonyeza chilakolako chako chonyansa mopitirira muyezo+ ndipo maliseche ako+ aonekera pamtunda pamene unali kuchita zauhule ndi zibwenzi zako+ ndi mafano ako onse onyansa,+ ndiponso chifukwa cha magazi a ana ako amene unawapereka kwa mafanowo,+ 37  ine ndisonkhanitsa pamodzi zibwenzi zako zonse zimene unali kuzisangalatsa. Ndisonkhanitsanso anthu onse ochokera kumalo onse okuzungulira amene unali kuwakonda limodzi ndi onse amene unali kudana nawo kuti akuukire. Ndidzakuvula pamaso pawo ndipo iwo adzaona maliseche ako onse.+ 38  “‘Ndidzakupatsa chiweruzo chimene chimaperekedwa kwa akazi achigololo+ ndi kwa akazi okhetsa magazi,+ ndipo ndidzakupatsa magazi a mkwiyo ndi nsanje.+ 39  Ndidzakupereka m’manja mwa anthu okuukira ndipo iwo adzafafaniza mulu wako wadothi+ ndi malo ako okwera.+ Iwo adzakuvula zovala+ ndipo adzatenga zinthu zako zokongola+ n’kukusiya wosavala ndi wamaliseche. 40  Adzakubweretsera chigulu cha anthu+ n’kukuponya miyala+ ndipo adzakupha ndi malupanga awo.+ 41  Iwo adzatentha nyumba zako ndi moto+ ndipo adzakulanga pamaso pa akazi ambiri.+ Ine ndidzakusiyitsa uhule+ moti sudzaperekanso malipiro. 42  Mkwiyo wanga ndidzauthetsera pa iwe,+ moti sindidzakuchitiranso nsanje.+ Ndidzangokhala osachita kalikonse ndipo sindidzakhalanso wokwiya.’ 43  “‘Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako+ ndipo unandikwiyitsa ndi zinthu zonsezi,+ ineyo ndidzakubwezera malinga ndi zochita zako.+ Sudzachitanso khalidwe lako lotayirira komanso zinthu zako zonse zonyansa,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 44  “‘Aliyense wokunenera mwambi+ adzanena mwambi wakuti, “Make mbuu, mwana mbuu!”+ 45  Iwe ndiwe mwana wamkazi wa mayi ako,+ omwe amanyansidwa ndi mwamuna wawo+ ndi ana awo aamuna. Ndiwe m’bale wawo wa abale ako, amene amanyansidwa ndi amuna awo ndi ana awo aamuna. Akazi inu, mayi wanu anali Mhiti,+ ndipo bambo wanu anali Muamori.’”+ 46  “‘Mkulu wako amene akukhala kumanzere kwako ndiye Samariya+ ndi midzi yake yozungulira.+ Mng’ono wako, amene akukhala mbali ya kudzanja lako lamanja ndi Sodomu+ ndi midzi yake yozungulira.+ 47  Iwe sikuti unangoyenda chabe m’njira zawo ndiponso sikuti unangochita zinthu motsatira zinthu zawo zonyansa,+ koma m’nthawi yochepa unayamba kuchita zinthu zoipa kwambiri kuposa iwowo m’njira zako zonse.+ 48  Pali ine Mulungu wamoyo, m’bale wako Sodomu ndi midzi yake yozungulira, sanachite mofanana ndi zimene iwe ndi midzi yako yozungulira munachita,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 49  ‘Tamvera! Cholakwa cha m’bale wako Sodomu chinali, kunyada,+ kukhala ndi chakudya chokwanira+ ndiponso kukhala ndi moyo wabata+ ndi wosatekeseka. Izi n’zimene iye ndi midzi yake yozungulira anali nazo.+ Sanalimbitse dzanja la munthu wosautsika+ ndi wosauka.+ 50  Iwo anapitiriza kudzikweza+ ndi kuchita chinthu chonyansa pamaso panga+ ndipo pamapeto pake ndinawachotsa nditaona kuti n’koyenera kutero.+ 51  “‘Komanso, Samariya+ sanachite machimo ofika ngakhale hafu ya machimo ako. Koma iwe unapitiriza kuchulukitsa zinthu zako zonyansa kuposa abale ako, moti unachititsa kuti iwo aoneke ngati olungama chifukwa cha zinthu zako zonse zonyansa zimene unali kuchita.+ 52  Iweyo udzachita manyazi kwambiri ukamadzaikira kumbuyo abale ako. Iwowo ndi olungama kuposa iweyo chifukwa machimo amene unachita ndi onyansa kwambiri kuposa amene iwowo anachita.+ Chotero iweyo uchite manyazi ndi kunyozeka chifukwa chakuti wachititsa kuti abale ako aoneke ngati olungama.’ 53  “‘Ine ndidzasonkhanitsa anthu awo amene anawagwira ndi kupita nawo kudziko lina.+ Ndidzasonkhanitsa anthu ogwidwa a ku Sodomu ndi midzi yake yozungulira, ndi ogwidwa a ku Samariya ndi midzi yake yozungulira. Ndidzasonkhanitsanso anthu ako amene anagwidwa omwe ali pakati pawo,+ 54  kuti udzachite manyazi.+ Iwe udzachita manyazi chifukwa cha zonse zimene unachita pakuti unawatonthoza.+ 55  Abale akowo, Sodomu ndi midzi yake yozungulira, Samariya ndi midzi yake yozungulira, adzakhalanso monga mmene analili kale, komanso iweyo ndi midzi yako yozungulira mudzakhalanso ngati mmene munalili kale.+ 56  M’bale wako Sodomu sanali woti n’kumveka ukumutchula ndi pakamwa pako m’masiku amene iwe unali kunyada.+ 57  Zoipa zako zisanaonekere,+ Sodomu sanali woti n’kumveka ukumutchula ngati mmene zinalili pa nthawi imene ana aakazi a Siriya+ ndi onse omuzungulira, komanso ana aakazi a Afilisiti,+ anali kukunyoza kuchokera kumbali zonse.+ 58  Chotero iweyo udzakumana ndi zotsatira za khalidwe lako lotayirira+ ndiponso zotsatira za zinthu zako zonyansa,’+ watero Yehova.” 59  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Inenso ndidzakubwezera mogwirizana ndi zochita zako,+ chifukwa unanyoza lumbiro pophwanya pangano langa.+ 60  Ndithu ine ndidzakumbukira pangano limene ndinapangana ndi iwe m’masiku a ubwana wako,+ ndipo ndidzakukhazikitsira pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale.*+ 61  Ndithu udzakumbukira njira zako+ ndipo udzachita manyazi ukadzalandira akulu ako ndi ang’ono ako. Ndidzawapereka kwa iwe ngati ana ako aakazi,+ koma osati chifukwa cha pangano limene ndinapangana nawe.’+ 62  “‘Ineyo ndidzapangana nawe pangano+ ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova. 63  Ndidzachita izi kuti ndikadzakuperekera nsembe yophimba machimo+ chifukwa cha zonse zimene wachita, udzakumbukire ndi kuchita manyazi+ ndiponso kuti usadzakhale ndi chifukwa chilichonse chotsegulira pakamwa pako+ chifukwa cha manyazi ako,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi

Katumbu ndi nyama yaubweya yam’madzi ndipo katumbu amene akutchulidwa pano ndi mtundu waukulu wa akatumbu amene amapezeka m’nyanja zikuluzikulu.
Ena amati, “masikiyo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.