Ezekieli 15:1-8
15 Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:
2 “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wa mpesa+ umasiyana bwanji ndi mitengo ina yonse? Kodi kamtengo kophuka pambali pa mtengowo pakati pa mitengo ya m’nkhalango kamasiyana bwanji ndi mitengo ina?
3 Kodi anthu amadula nthambi yake kuti ikhale mtengo wogwiritsira ntchito inayake? Kapena kodi amatengapo kamtengo koti akhome pakhoma kuti azikolowekapo ziwiya zosiyanasiyana?
4 Mtengowotu umangoikidwa pamoto basi kuti ukhale nkhuni.+ Motowo umanyeketsa kutsinde ndi kunsonga kwake. Pakati pa mtengowo pamapsanso.+ Choncho kodi mtengowo ungagwire ntchito ina iliyonse?
5 Mtengowo ukakhala wathunthu saugwiritsa ntchito iliyonse. Ndiye kuli bwanji ukapsa ndi moto n’kunyeka? Kodi ungagwirenso ntchito iliyonse?”+
6 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Mofanana ndi mtengo wa mpesa umene uli pakati pa nkhalango, umene ndaupereka kuti uzikhala nkhuni pamoto, ndaperekanso anthu okhala mu Yerusalemu.+
7 Anthuwo ndawayang’ana mokwiya.+ Iwo achoka pamoto, koma motowo uwanyeketsa.+ Anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, ndikadzawayang’ana mokwiya.’”+
8 “‘Dziko lawo ndidzalisandutsa bwinja lokhalokha+ chifukwa chakuti iwo achita zosakhulupirika,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”