Ezekieli 14:1-23

14  Tsopano akuluakulu a Isiraeli anabwera kwa ine n’kudzakhala pamaso panga.+  Kenako Yehova analankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, amuna awa aika mitima yawo pamafano onyansa, ndipo aika pamaso pawo chinthu chopunthwitsa chimene chimawalakwitsa.+ Kodi ndiwayankhe iwo akamandifunsa?+  Chotero lankhula nawo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli amene waika mtima wake pamafano ake onyansa+ ndiponso amene waika pamaso pake chinthu chopunthwitsa chimene chimamulakwitsa n’kupita kwa mneneri, ine Yehova ndidzamuyankha malinga ndi kuchuluka kwa mafano ake onyansa.+  Ndidzatero kuti ndichititse mantha mitima ya anthu a nyumba ya Isiraeli,+ pakuti onsewo achoka kwa ine chifukwa cha mafano awo onyansa.”’+  “Choncho uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Bwererani, siyani mafano anu onyansa.+ Tembenuzani nkhope zanu kuti musayang’anenso zinthu zanu zonse zonyansa.+  Pakuti munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli kapena mlendo amene akukhala mu Isiraeli, amene wasiya kunditsatira+ n’kuika mtima wake pamafano ake onyansa, ndiponso amene waika pamaso pake chinthu chopunthwitsa chimene chimamulakwitsa n’kupita kwa mneneri kuti akafunsire kwa ine,+ ine Yehova ndidzamuyankha ndekha.  Ine ndidzamuyang’ana mokwiya+ n’kumuika kuti akhale chenjezo+ ndi mwambi.+ Ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu anga,+ ndipo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’+  “‘Ngati mneneri wapusitsidwa n’kulankhula mawu, ineyo Yehova ndi amene ndamupusitsa mneneriyo.+ Ndidzamutambasulira dzanja langa n’kumuwononga pakati pa anthu anga, Aisiraeli.+ 10  Iwo adzakumana ndi zotsatira za zolakwa zawo.+ Zolakwa za wofunsira zidzakhala chimodzimodzi ndi zolakwa za mneneri,+ 11  kuti a nyumba ya Isiraeli asadzasiyenso kunditsatira n’kumangoyenda uku ndi uku,+ ndiponso kuti asadzadziipitsenso ndi zochimwa zawo zonse. Chotero iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+ 12  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 13  “Iwe mwana wa munthu, ngati dziko landichimwira pochita zosakhulupirika,+ ndidzalitambasulira dzanja langa n’kuthyola ndodo zake zimene amakolowekapo mikate yoboola pakati.+ Komanso ndidzalitumizira njala+ ndipo ndidzapha anthu ndi ziweto m’dzikolo.”+ 14  “‘Amuna atatu awa: Nowa,+ Danieli+ ndi Yobu,+ akanakhala m’dzikolo, iwo okhawo akanapulumutsa miyoyo yawo chifukwa chokhala olungama,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+ 15  “‘Nditati ndichititse zilombo zolusa zakutchire kudutsa m’dzikolo,+ zilombozo n’kuliphera ana dzikolo,+ moti dzikolo n’kukhala bwinja lokhalokha popanda munthu aliyense wodutsamo chifukwa cha zilombo zolusazo,+ 16  ngakhale zikanakhala kuti amuna atatu amenewa anali kukhala m’dzikolo, pali ine Mulungu wamoyo, iwo sakanapulumutsa ana awo aamuna kapena aakazi. Iwo okhawo ndiwo akanapulumutsidwa, koma dzikolo likanakhala bwinja lokhalokha,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 17  “‘Kapena nditati ndibweretse lupanga m’dzikolo,+ n’kunena kuti: “M’dzikolo mudutse lupanga,” ine n’kuphamo anthu ndi ziweto,+ 18  ngakhale amuna atatu amenewa akanakhalamo,+ pali ine Mulungu wamoyo, sakanapulumutsa ana awo aamuna kapena ana awo aakazi, koma iwo okhawo ndiwo akanapulumutsidwa,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 19  “‘Kapenanso nditati nditumize mliri m’dzikolo,+ n’kukhuthulira mkwiyo wanga padzikolo, n’kukhetsa magazi+ ambiri popha anthu ndi ziweto m’dzikolo, 20  ngakhale Nowa,+ Danieli+ ndi Yobu+ akanakhala m’dzikolo,+ pali ine Mulungu wamoyo, sakanapulumutsamo mwana wawo wamwamuna kapena wamkazi. Iwo okhawo akanapulumutsa miyoyo yawo chifukwa chokhala olungama,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+ 21  “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Zidzateronso ndikadzabweretsa ziweruzo zanga zinayi izi zowononga:+ lupanga, njala, zilombo zolusa zakutchire ndi mliri.+ Ndidzatumiza zimenezi mu Yerusalemu kuti zikaphemo anthu ndi ziweto.+ 22  Koma ndithu m’dzikolo mudzatsala kagulu ka anthu amene adzapulumuke ndipo adzatulutsidwamo.+ Taonani ana aamuna ndi aakazi! Iwo akubwera kwa inu, ndipo mudzaona njira yawo ndi zochita zawo.+ Inu mudzatonthozedwa pambuyo pa tsoka limene ndidzabweretse pa Yerusalemu, ngakhalenso pambuyo pa zonse zimene ndidzabweretsere mzindawo.’” 23  “‘Ndithu iwo adzakutonthozani mukadzaona njira zawo ndi zochita zawo. Chotero mudzadziwa kuti zonse zimene ndidzachitire mzindawo, sindinazichite popanda chifukwa,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+

Mawu a M'munsi