Ezekieli 13:1-23

13  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, losera zokhudza aneneri a mu Isiraeli.+ Uuze amene akulosera zam’mutu mwawo+ kuti, ‘Mvetserani mawu a Yehova.+  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka kwa aneneri opusa,+ amene akungolosera zamumtima mwawo+ pamene sanaone chilichonse.+  Iwe Isiraeli, aneneri ako akhala ngati nkhandwe za m’mabwinja.+  Amuna inu, simudzapita kukakhala m’mipata ya mpanda+ kuti mukamenye nkhondo, kapena kuti mukamangire nyumba ya Isiraeli mpanda wamiyala+ n’cholinga chakuti mudzadziteteze pa nkhondo ya m’tsiku la Yehova.”+  “Iwo aona masomphenya abodza ndipo alosera zonama.+ Akunena kuti, ‘Yehova wanena kuti,’ pamene Yehova sanawatume, ndipo akuyembekeza kuti zimene anenazo zichitika.+  Amuna inu, kodi masomphenya mwaonawa si abodza? Kodi zimene mwaloserazi si zonama? Inu mwati, ‘Yehova wanena kuti,’ pamene ine sindinalankhule kalikonse.”’+  “‘Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘Pakuti amuna inu mwalankhula zabodza ndipo mwaona masomphenya onama, ine ndithana nanu,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”  Dzanja langa lalimbana ndi aneneri amene akuona masomphenya abodza ndiponso amene akulosera zonama.+ Iwo sadzapitiriza kukhala m’gulu la anthu anga apamtima,+ komanso sadzalembedwa m’buku la mayina a anthu a nyumba ya Isiraeli.+ Sadzabwera kudziko la Isiraeli+ ndipo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa,+ 10  chifukwa chakuti iwo asocheretsa anthu anga ponena kuti, “Tili pa mtendere!” Koma palibe mtendere.+ Palinso munthu amene akumanga khoma lachipinda, ndipo anthu ena akulipaka laimu pachabe.’+ 11  “Uza anthu amene akupaka laimuwo kuti khomalo lidzagwa. Kudzagwa mvula yambiri imene madzi ake adzasefukira. Kudzagwa matalala ndipo mphepo yamkuntho idzang’amba khomalo.+ 12  Ndithu khomalo lidzagwa. Amuna inu, kodi anthu sadzakufunsani kuti, ‘Ali kuti laimu amene munapaka uja?’+ 13  “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzatumiza mphepo yamkuntho, mvula yambiri ndi matalala, kusonyeza mkwiyo wanga kuti ndikuwonongeni.+ 14  Khoma limene amuna inu mwalipaka laimulo, ndidzaligwetsa lonse mpaka pansi moti maziko ake adzaonekera.+ Mzindawo udzawonongedwa ndithu, ndipo inuyo mudzathera pakati pake. Choncho mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+ 15  “‘Mkwiyo wanga ndidzauthetsera pakhomalo ndiponso pa anthu amene analipaka laimu. Anthu inu ndidzakuuzani kuti: “Khoma lija kulibe, komanso anthu amene analipaka laimu aja kulibe,+ 16  kutanthauza aneneri a mu Isiraeli amene akulosera zokhudza Yerusalemu, amene akuona masomphenya onena za mzindawo kuti mudzakhala mtendere+ pamene simudzakhala mtendere,”’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 17  “Koma iwe mwana wa munthu, yang’ana+ kwa ana aakazi a anthu a mtundu wako, amene akulosera+ zam’mutu mwawo+ monga aneneri aakazi, ndipo ulosere zoipa zimene zidzawachitikire. 18  Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka kwa akazi amene akusoka pamodzi zinthu zovala m’zigongono, amenenso akupanga zophimba kumutu za mitu ya anthu otalika mosiyanasiyana n’cholinga chakuti awakole mumsampha anthuwo.+ Kodi mukusaka miyoyo ya anthu anga? Kodi pochita zimenezi, mukuganiza kuti mupulumutsa miyoyo yanu? 19  Kodi zoona mukundinyozetsa pamaso pa anthu anga chifukwa cha balere wongodzaza m’manja ndi nyenyeswa za mkate?+ Kodi mukuphadi anthu osayenera kufa,+ ndipo mukusiya anthu osayenera kukhala ndi moyo, ponamiza anthu anga amene akumva bodza lanulo?”’+ 20  “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndithana ndi zovala za m’mikono za akazi inu, zimene mukukolera miyoyo ya anthu ngati kuti ndi mbalame. Ine ndizichotsa m’mikono mwanu ndi kumasula miyoyo ya anthu imene mukuikola ngati mbalame.+ 21  Nding’amba zovala zanu zakumutu ndi kulanditsa anthu anga m’manja mwanu, ndipo iwo sadzakhalanso m’manja mwanu ngati zinthu zogwidwa posaka. Chotero inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 22  Chifukwa chakuti mwakhumudwitsa mtima wa munthu wolungama mwa chinyengo chanu,+ pamene ineyo sindinamukhumudwitse, ndiponso chifukwa chakuti mwalimbitsa manja a munthu woipa+ kuti asasiye njira zake zoipa, n’kukhala ndi moyo,+ 23  akazi inu simupitiriza kuona masomphenya abodza+ ndipo simudzaloseranso zam’tsogolo.+ Ineyo ndidzapulumutsa anthu anga m’manja mwanu+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+

Mawu a M'munsi