Ezekieli 12:1-28

12  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu opanduka+ omwe ali ndi maso koma saona,+ omwe ali ndi makutu koma samva,+ chifukwa ndi anthu opanduka.+  Tsopano iweyo mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo ndipo upite ku ukapolo masana, anthu akuona. Upite ku ukapolo iwo akuona. Uchoke kwanu kupita kumalo ena. Mwina azindikira tanthauzo lake ngakhale kuti iwo ndi anthu opanduka.+  Utulutse katundu wako monga katundu wopita naye ku ukapolo. Umutulutse masana iwo akuona. Madzulo, iweyo unyamuke iwo akuona. Unyamuke ngati mmene amachitira anthu otengedwa kupita ku ukapolo.+  “Uboole khoma iwo akuona n’kutulutsirapo katundu wako.+  Unyamule katunduyo paphewa iwo akuona, ndipo utulutse katunduyo kuli mdima. Uphimbe nkhope yako kuti usaone dziko chifukwa ndakuika kuti ukhale chizindikiro+ kwa nyumba ya Isiraeli.”+  Chotero ine ndinachita zonse monga mmene anandilamulira.+ Ndinatulutsa katundu wanga masana ngati mmene amachitira anthu opita ku ukapolo. Madzulo ndinaboola khoma ndi manja. Kutagwa mdima, ndinatulutsa katundu wanga, ndipo ndinanyamula katunduyo paphewa iwo akuona.  M’mawa Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, kodi anthu opanduka a nyumba ya Isiraeli+ sanakufunse kuti, ‘Kodi ukuchita chiyani?’ 10  Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali uthenga uwu wotsutsana ndi mtsogoleri,+ uthenga wokhudza Yerusalemu ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli amene ali kumeneko.”’ 11  “Uwauze kuti iweyo ndiwe chizindikiro cholosera zam’tsogolo+ kwa iwo. Zidzachitika kwa iwo monga mmene iwe wachitira. Iwo adzapita ku ukapolo, kudziko lina.+ 12  Mtsogoleri amene ali pakati pawo adzanyamula katundu wake paphewa n’kumapita mu mdima. Adzaboola khoma n’kutulukirapo.+ Iye adzaphimba kumaso kuti asaone dziko. 13  Ine ndidzamutambasulira ukonde wanga. Chotero iye adzakodwa mu ukonde wanga wosakira+ ndipo ndidzamupititsa ku Babulo, kudziko la Akasidi.+ Koma iye sadzaliona ndipo adzafera komweko.+ 14  Anthu onse omuzungulira amene amamuthandiza, ndiponso magulu ake onse ankhondo, ndidzawabalalitsira ku mphepo zonse zinayi,+ ndipo ndidzawatsatira nditasolola lupanga.+ 15  Ndikadzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndi kumayiko ena, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 16  Pakati pawo ndidzapulumutsapo amuna ochepa kuti asaphedwe ndi lupanga,+ njala, kapena miliri, n’cholinga chakuti akafotokoze za zinthu zawo zonse zonyansa+ pakati pa mitundu imene akakhaleko,+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.” 17  Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti: 18  “Iwe mwana wa munthu, idya chakudya ukunjenjemera, ndipo umwe madzi ndi mantha ndiponso nkhawa.+ 19  Anthu a m’dzikoli uwauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kwa anthu okhala mu Yerusalemu, okhala m’dziko la Isiraeli:+ “Adzadya chakudya ndi nkhawa ndipo adzamwa madzi ndi mantha, pakuti dzikolo lidzakhala bwinja.+ Zinthu zonse za mmenemo zidzachotsedwa chifukwa cha zinthu zachiwawa zimene anthu onse okhala mmenemo akuchita.+ 20  Mizinda ya anthu idzawonongedwa.+ Dzikolo lidzangokhala bwinja lokhalokha,+ ndipo inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+ 21  Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti: 22  “Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene anthu inu okhala m’dziko la Isiraeli mukunena+ wakuti, ‘Masiku akupita+ koma palibe masomphenya amene akwaniritsidwa,’+ umatanthauza chiyani? 23  Chotero uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndithu Ine ndidzathetsa mwambi umenewu ndipo sadzaunenanso ngati mwambi mu Isiraeli.”’+ Koma uwauze kuti, ‘Masiku ayandikira+ ndipo zonse zotchulidwa m’masomphenya zichitikadi.’ 24  Pakati pa nyumba ya Isiraeli sipadzakhalanso masomphenya opanda pake+ kapena kulosera kwachiphamaso.+ 25  ‘“Pakuti ine Yehova ndidzalankhula, ndipo mawu amene ndidzalankhulewo adzakwaniritsidwadi.+ Sindidzazengerezanso+ chifukwa ine ndidzalankhula mawu m’masiku anu,+ inu a m’nyumba yopanduka, ndipo mawuwo ndidzawakwaniritsa,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’” 26  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 27  “Iwe mwana wa munthu, a nyumba ya Isiraeli akunena kuti, ‘Masomphenya amene akuona adzachitika m’tsogolo, ndipo akulosera zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo kwambiri.’+ 28  Chotero iwe uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘Sindidzazengerezanso pa zimene ndalankhula.+ Mawu alionse amene ndalankhula adzakwaniritsidwadi,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’”+

Mawu a M'munsi