Ezekieli 10:1-22

10  Ndinapitiriza kuona masomphenya, ndipo ndinaona kuti pamwamba pa thambo+ limene linali pamwamba pa mitu ya akerubi, panali chinachake chooneka ngati mwala wa safiro.+ Chinthucho chinalinso chooneka ngati mpando wachifumu,+ ndipo chinali kuonekera pamwamba pa mitu yawo.  Kenako Mulungu anauza munthu amene anavala zovala zansalu+ uja, kuti: “Pita pakati pa mawilo,+ pansi pa akerubi. Ukatengepo makala+ amoto odzaza manja ako onse awiri kuchokera pakati pa akerubiwo, ndipo ukawaponye pamzindawo.”+ Chotero iye anapitadi ine ndikuona.  Akerubiwo anali ataimirira mbali ya kumanja kwa nyumbayo pamene munthuyo anapita pakati pawo, ndipo mtambo unali utadzaza bwalo lonse lamkati.+  Tsopano ulemerero wa Yehova+ unachoka pa akerubi n’kupita pakhomo la nyumba yopatulika, ndipo mtambo+ unadzaza nyumbayo pang’onopang’ono. Komanso ulemerero wowala wa Yehova unadzaza m’bwalo lonse la nyumbayo.  Phokoso la mapiko a akerubiwo+ linali kumveka mpaka kubwalo lakunja. Phokosolo linali kumveka ngati kulankhula kwa Mulungu Wamphamvuyonse.+  Kenako Mulungu analamula munthu wovala zovala zansalu uja kuti: “Tenga moto pakati pa mawilo, pakati pa akerubi.” Atatero munthuyo anapita n’kukaima pambali pa wilo.  Ndiyeno kerubi wina anatambasula dzanja lake kuchokera pakati pa akerubiwo n’kutapa moto+ umene unali pakati pawo.+ Iye anatenga motowo n’kuuika m’manja mwa munthu wovala zovala zansalu+ uja, ndipo munthuyo anatenga motowo n’kuchoka.  Kupansi kwa mapiko a akerubiwo,+ kunaoneka chinachake chokhala ngati dzanja la munthu.  Ndinapitiriza kuona masomphenya, ndipo ndinaona kuti pambali pa akerubi panali mawilo anayi. Pambali pa kerubi aliyense panali wilo limodzi.+ Maonekedwe a mawilowo anali ngati kuwala kwa mwala wa kulusolito. 10  Mawilo anayiwo anali ofanana. Anali kuoneka ngati kuti wilo lina lili pakati pa wilo linzake.*+ 11  Mawilowo anali kulowera kumbali zawo zonse zinayi. Akamayenda, sanali kukhota chifukwa chakuti anali kulowera kumene mitu ya akerubiwo* yayang’ana. Akamayenda sanali kukhota.+ 12  Zamoyozo zinali ndi maso paliponse. Zinali ndi maso pamatupi awo, kumbuyo kwawo, m’manja awo, m’mapiko awo, ndiponso kuzungulira mawilo onse.+ Pambali pa kerubi aliyense mwa akerubi anayi amenewo, panali wilo. 13  Kenako ndinamva mawu akuitana mawilowo kuti, “Mawilo inu!” 14  Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi.+ Nkhope yoyamba inali ya kerubi. Nkhope yachiwiri inali ya munthu.+ Nkhope yachitatu inali ya mkango, ndipo nkhope yachinayi inali ya chiwombankhanga.+ 15  Akerubiwo anali zamoyo zomwe zija zimene ndinaziona kumtsinje wa Kebara.+ Akerubiwo akanyamuka kukwera m’mwamba,+ 16  kapena akamapita, mawilo aja anali kupita nawo limodzi ali pambali pawo.+ Akerubiwo akatambasula mapiko awo kuti akhale pamwamba pa dziko lapansi, mawilo sanali kutembenukira kwina, anali kungokhala pambali pa zamoyozo.+ 17  Akerubi akaima chilili, mawilonso anali kuima chilili. Akerubiwo akakwera m’mwamba,+ mawilonso anali kukwera m’mwamba, pakuti mzimu wa zamoyozo unali m’mawilowo.+ 18  Kenako ulemerero+ wa Yehova unanyamuka kuchoka pakhomo la nyumba yopatulika n’kukakhala pamwamba pa akerubi.+ 19  Tsopano akerubi aja anatambasula mapiko awo n’kunyamuka kuchoka pansi+ ine ndikuona. Atanyamuka, mawilo aja anali pambali pawo. Kenako iwo anakaima pakhomo la kum’mawa la chipata cha nyumba ya Yehova, ndipo ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli unali pamwamba pawo. 20  Zimenezi zinali zamoyo+ zimene ndinaziona pansi pa mpando wachifumu wa Mulungu wa Isiraeli kumtsinje wa Kebara,+ choncho ndinadziwa kuti anali akerubi. 21  Pa zamoyo zinayizo, chamoyo chilichonse chinali ndi nkhope zinayi+ ndi mapiko anayi, ndipo kupansi kwa mapiko awo kunali zinthu zooneka ngati manja a munthu. 22  Nkhope zawo zinali zofanana ndi zimene ndinaziona m’mphepete mwa mtsinje wa Kebara. Zinali zofanana ndendende.+ Chamoyo chilichonse chinali kupita kutsogolo basi.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eze 1:16.
Mawu ake enieni, “mutu.”