Ezekieli 1:1-28

1  M’chaka cha 30, m’mwezi wachinayi, pa tsiku lachisanu la mweziwo, pamene ndinali pakati pa anthu amene anali ku ukapolo+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara,+ kumwamba kunatseguka+ ndipo ndinayamba kuona masomphenya a Mulungu.+  Pa tsiku lachisanu la mweziwo, m’chaka chachisanu kuchokera pamene Mfumu Yehoyakini anatengedwa ukapolo,+  Yehova analankhula+ ndi Ezekieli,+ mwana wa wansembe Buzi, pamene anali m’dziko la Akasidi+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Dzanja la Yehova linafika pa iye kumeneko.+  Ndinayamba kuona masomphenya, ndipo ndinaona mphepo yamkuntho+ ikuchokera kumpoto. Ndinaonanso mtambo waukulu+ ndi moto walawilawi.+ Mtambowo unali wowala ndipo unali kuwalitsa malo onse ozungulira pamenepo. Pakati pa motowo panali powala ngati siliva wosakanikirana ndi golide, wooneka ngati akuchokera pakati pa motowo.+  Pakati pa motowo panali zinazake zooneka ngati zamoyo zinayi,+ ndipo zamoyozo zinali zooneka ngati anthu.  Chamoyo chilichonse chinali ndi nkhope zinayi+ ndi mapiko anayi.+  Mapazi awo anali owongoka, ndipo kupansi kwa mapazi awo kunali ngati kupansi kwa mapazi a mwana wa ng’ombe.+ Mapaziwo anali kuwala ngati mkuwa wopukutidwa bwino.+  Kunsi kwa mapiko anayi a zamoyozo kunali manja a munthu.+ Zamoyozo zinali ndi nkhope ndiponso mapiko.+  Mapiko a chamoyo china anali kukhudzana ndi a chamoyo china. Zamoyozo sizinali kutembenuka zikamayenda. Chilichonse chinkangopita kutsogolo basi.+ 10  Ponena za maonekedwe a nkhope zawo, zamoyo zinayi zimenezi zinali ndi nkhope ya munthu,+ nkhope ya mkango+ mbali ya kumanja,+ nkhope ya ng’ombe yamphongo+ mbali ya kumanzere,+ ndiponso nkhope ya chiwombankhanga.+ 11  Umu ndi mmene nkhope zawo zinalili. Mapiko awo+ anali otambasukira m’mwamba. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko awiri ogundana, ndipo mapiko ena awiri anali kuphimba matupi awo.+ 12  Chamoyo chilichonse chinkapita kutsogolo basi.+ Zamoyozo zinali kupita kulikonse kumene mzimu wafuna kuti zipite.+ Zikamayenda sizinali kutembenuka.+ 13  Zamoyozo zinali zooneka ngati makala oyaka moto.+ Pakati pa zamoyozo panali zinazake zooneka ngati miyuni ya moto+ zimene zinali kuyenda uku ndi uku. Motowo unali wowala, ndipo m’motowo munali kutuluka mphezi.+ 14  Zamoyozo zinali kuyenda uku ndi uku, ndipo zikamayenda zinali kuoneka ngati mphezi.+ 15  Pamene ndinali kuyang’ana zamoyozo, ndinangoona kuti pansi panali wilo limodzi pafupi ndi zamoyozo,+ pambali pa nkhope zinayi za chamoyo chilichonse.+ 16  Maonekedwe a mawilowo+ anali ngati kuwala kwa mwala wa kulusolito,+ ndipo mawilo anayiwo anali ofanana. Kapangidwe kake kanali ngati kuti wilo lina lili pakati pa wilo linzake.*+ 17  Mawilowo akamayenda, anali kulowera kumbali zonse zinayi+ ndipo sanali kukhotera kwina.+ 18  Malimu a mawilowo anali aatali kwambiri moti anali ochititsa mantha. Malimu anayi onsewo anali odzaza ndi maso.+ 19  Zamoyo zija zikamayenda, mawilowo anali kuyenda pambali pawo. Zamoyozo zikanyamuka kuchoka pansi, mawilowonso anali kunyamuka.+ 20  Kulikonse kumene mzimu ukufuna kupita, zamoyozo zinali kupita kumeneko, chifukwa mzimuwo wafuna kuti upite kumeneko. Mawilowo anali kukwera m’mwamba ali pambali pa zamoyozo, pakuti mzimu wa zamoyozo unali m’mawilowo. 21  Zamoyozo zikamayenda, mawilowo analinso kuyenda. Zikaima chilili, mawilowonso anali kuima chilili. Zamoyozo zikakwera m’mwamba kuchoka pansi, mawilowonso anali kukwera m’mwamba ali pambali pa zamoyozo, pakuti mzimu wa zamoyozo unali m’mawilowo.+ 22  Pamwamba pa mitu ya zamoyozo, panali chinachake chooneka ngati thambo,+ chonyezimira ngati madzi oundana ochititsa chidwi, choyalidwa pamwamba pa mitu yawo.+ 23  Pansi pa thambolo, mapiko awo anali otambasuka. Phiko lililonse linagundana ndi phiko la chamoyo chinzake. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko awiri ochiphimba mbali imodzi, ndi mapiko ena awiri ochiphimba mbali ina ya thupi lake. 24  Ndinamva phokoso la mapiko awo, lokhala ngati phokoso la madzi ambiri,+ ndiponso ngati phokoso la Wamphamvuyonse. Zikamayenda, zinali kuchita phokoso ngati la chipwirikiti cha anthu,+ ngati phokoso la pamsasa.+ Zikaima chilili, zinali kutsitsa mapiko awo. 25  Pamwamba pa thambo limene linali pamwamba pa mitu yawo, panamveka mawu. (Zikaima chilili, zinali kutsitsa mapiko awo.) 26  Pamwamba pa thambo limene linali pamwamba pa mitu yawo, panali chinachake chooneka ngati mwala wa safiro,+ chooneka ngati mpando wachifumu.+ Pachinthu chooneka ngati mpando wachifumucho, panali winawake wooneka ngati munthu,+ atakhala pamwamba pake. 27  Ndinaona chinachake chowala ngati siliva wosakanikirana ndi golide,+ chooneka ngati kuti mkati mwake monse mukuyaka moto.+ Kuchokera pa chimene chinali kuoneka ngati chiuno chake kupita m’mwamba ndiponso kutsika m’munsi, munthuyo anali kuoneka ngati moto, ndipo pamalo onse omuzungulira panali powala. 28  Panali chinachake chooneka ngati utawaleza+ umene umaoneka mumtambo pa tsiku la mvula yamphamvu. Umu ndi mmene kuwala kozungulira pamalopo kunali kuonekera. Zinali kuoneka ngati ulemerero wa Yehova.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ Kenako ndinayamba kumva mawu a winawake akulankhula.

Mawu a M'munsi

Mwina wilo limodzi linali kulowa pakati pa wilo linzake mopingasana nalo. Chotero mawilowo anali ndi mbali zinayi.