Ezara 9:1-15

9  Zinthu zimenezi zitangotha, akalonga+ anabwera kwa ine n’kundiuza kuti: “Aisiraeli, ansembe ndiponso Alevi sanadzipatule+ kwa anthu a mitundu ina pa nkhani ya zinthu zonyansa+ za anthu a mitundu inawo. Anthu ake ndi Akanani,+ Ahiti,+ Aperezi,+ Ayebusi,+ Aamoni,+ Amowabu,+ Aiguputo+ ndi Aamori.+  Iwo alola ena mwa ana aakazi a mitundu inayo kuti akhale akazi awo ndi akazi a ana awo aamuna,+ ndipo iwo omwe ndi mtundu wopatulika,+ asakanikirana+ ndi anthu a mitundu ina. Akalonga ndi atsogoleri ndiwo ali patsogolo+ pa kusakhulupirika kumeneku.”  Nditangomva nkhani imeneyi, ndinang’amba zovala zanga+ n’kuyamba kuzula tsitsi la m’mutu mwanga+ ndi ndevu zanga, ndipo ndinakhala pansi ndili wokhumudwa ndi wachisoni kwambiri.+  Iwo anayamba kusonkhana kwa ine, aliyense akunjenjemera+ chifukwa cha mawu a Mulungu wa Isiraeli otsutsa kusakhulupirika kwa anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo. Pa nthawiyi n’kuti ine nditakhala pansi ndili wokhumudwa ndi wachisoni kwambiri, ndipo ndinakhala choncho mpaka nthawi yopereka nsembe yambewu yamadzulo.+  Pa nthawi yopereka nsembe yambewu+ yamadzulo, pambuyo podzichepetsa mwanjira imeneyi, ndinaimirira, zovala zanga zitang’ambika, ndipo ndinagwada+ n’kutambasulira manja anga kwa Yehova Mulungu wanga.+  Kenako ndinayamba kunena kuti:+ “Inu Mulungu wanga, ndikuchita manyazi+ kuti ndikweze nkhope yanga kwa inuyo Mulungu wanga, chifukwa zolakwa zathu+ zachuluka pamutu pathu ndipo machimo athu achuluka kwambiri mpaka kufika kumwamba.+  Kuyambira masiku a makolo athu+ mpaka lero, takhala m’machimo aakulu kwambiri,+ ndipo chifukwa cha zolakwa zathu, ifeyo, mafumu athu,+ ndi ansembe athu,+ taperekedwa m’manja mwa mafumu a mayiko ena ndi lupanga,+ mwa kutengedwa ukapolo,+ kulandidwa katundu,+ komanso kukhala ndi nkhope zamanyazi+ ngati mmene tilili lero.  Tsopano kwa nthawi yochepa, Yehova Mulungu wathu watikomera mtima+ mwa kutisiyira anthu opulumuka,+ ndiponso mwa kutipatsa malo otetezeka* m’malo ake oyera kuti maso athu awale,+ inu Mulungu wathu, ndi kutitsitsimutsa pang’ono mu ukapolo wathu.+  Ngakhale kuti ndife akapolo,+ Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathuwo,+ koma watisonyeza kukoma mtima kosatha pamaso pa mafumu a ku Perisiya.+ Wachita zimenezi kuti atitsitsimutse n’cholinga choti tikamange nyumba ya Mulungu wathu+ komanso tikakonze malo ozungulira nyumbayo amene anali bwinja,+ ndi kuti tikhale mu Yuda ndi mu Yerusalemu ngati kuti tili mumpanda wamiyala.+ 10  “Ndiye tinganene chiyani inu Mulungu wathu pambuyo pa zimene zachitikazi? Popeza tasiya malamulo anu+ 11  amene munatilamula kudzera mwa atumiki anu aneneri, akuti, ‘Dziko limene anthu inu mukukalitenga kukhala lanu ndi lodetsedwa chifukwa cha kudetsedwa kwa anthu a mitundu ina,+ ndiponso chifukwa cha zonyansa zawo+ zimene adzaza nazo dzikolo. Iwo adzaza dzikolo ndi zodetsa kuyambira koyambirira mpaka kumapeto.+ 12  Choncho musakapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna,+ kapena kutenga ana awo aakazi n’kuwapereka kwa ana anu aamuna. Ndipo mpaka kalekale, musakawathandize kukhala ndi mtendere+ ndiponso kutukuka. Mukachite zimenezi kuti mukakhale amphamvu+ ndiponso kuti mukadyedi zabwino za dzikolo ndi kulitengadi kuti likhale la ana anu mpaka kalekale.’+ 13  Tsopano pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha zochita zathu zoipa+ ndi machimo athu ochuluka, ngakhale kuti inuyo Mulungu wathu simunatilange monga mmene tinafunika kulangidwira+ ndipo mwalola kuti anthu onsewa apulumuke,+ 14  kodi zoona tiphwanyenso malamulo anu kachiwiri ndi kupanga mapangano a ukwati+ ndi anthu a mitundu ina ochita zonyansawa?+ Kodi tikatero simutikwiyira koopsa+ mwakuti sipakhalanso wotsala+ ndi wopulumuka? 15  Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli ndinu wolungama+ chifukwa ife tatsala monga anthu opulumuka lero. Taima pamaso panu m’machimo athu,+ ngakhale kuti n’zosatheka kuima pamaso panu chifukwa cha machimo athuwo.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chikhomo.”