Ezara 7:1-28

7  Pambuyo pa zimenezi, mu ulamuliro wa mfumu Aritasasita+ ya ku Perisiya, panali mwamuna wina dzina lake Ezara.+ Iye anali mwana wa Seraya.+ Seraya anali mwana wa Azariya, Azariya anali mwana wa Hilikiya,+  Hilikiya anali mwana wa Salumu,+ Salumu anali mwana wa Zadoki, Zadoki anali mwana wa Ahitubu,+  Ahitubu anali mwana wa Amariya,+ Amariya anali mwana wa Azariya,+ Azariya anali mwana wa Merayoti,+  Merayoti anali mwana wa Zerahiya,+ Zerahiya anali mwana wa Uzi,+ Uzi anali mwana wa Buki,+  Buki anali mwana wa Abisuwa,+ Abisuwa anali mwana wa Pinihasi,+ Pinihasi anali mwana wa Eleazara,+ ndipo Eleazara anali mwana wa Aroni+ wansembe wamkulu.+  Ezara ameneyu ananyamuka n’kuchoka ku Babulo. Iye anali katswiri wodziwa kukopera+ chilamulo cha Mose,+ chimene Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka. Chotero mfumu inamupatsa zopempha zake zonse chifukwa dzanja la Yehova Mulungu wake linali pa iye.+  Choncho ena mwa ana a Isiraeli, ansembe,+ Alevi,+ oimba,+ alonda a pazipata,+ ndi Anetini+ anapita ku Yerusalemu m’chaka cha 7 cha mfumu Aritasasita.+  Patapita nthawi, Ezara anafika ku Yerusalemu m’mwezi wachisanu, m’chaka cha 7 cha mfumuyo.  Zinatero chifukwa pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, iye analamula anthu kuti anyamuke ku Babulo, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, iye anafika ku Yerusalemu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linali pa iye,+ 10  popeza Ezara anakonza+ mtima wake kuti aphunzire chilamulo cha Yehova+ ndi kuchichita+ ndiponso kuti aphunzitse+ mu Isiraeli malamulo+ ndi chilungamo.+ 11  Izi n’zimene zinali m’kalata imene Mfumu Aritasasita inapatsa wansembe Ezara wokopera zinthu, wokopera+ mawu a malamulo a Yehova ndi malangizo ake kwa Aisiraeli: 12  “Kuchokera kwa Aritasasita,+ mfumu ya mafumu,+ kupita kwa wansembe Ezara, wokopera chilamulo cha Mulungu wakumwamba:+ Ukhale ndi mtendere wochuluka.+ Tsopano 13  ine ndaika lamulo+ lakuti aliyense mu ufumu wanga+ pakati pa anthu a Isiraeli, ansembe awo, ndi Alevi amene akufuna kupita nawe ku Yerusalemu apite.+ 14  Popeza kuchokera kwa mfumu ndi aphungu ake 7+ lamulo linaperekedwa kuti afufuze+ zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, m’chilamulo+ cha Mulungu+ wako chimene chili m’manja mwako, 15  ndi kutinso munyamule siliva ndi golide zimene mfumu ndi aphungu ake apereka mwaufulu+ kwa Mulungu wa Isiraeli, amene amakhala ku Yerusalemu.+ 16  Munyamulenso siliva ndi golide yense amene mum’peze m’chigawo chonse cha Babulo, limodzi ndi mphatso za anthu+ ndi za ansembe omwe akupereka mwaufulu kunyumba ya Mulungu wawo,+ yomwe ili ku Yerusalemu. 17  Ndi ndalama zimenezi, ukagule mwamsangamsanga ng’ombe zamphongo,+ nkhosa zamphongo,+ ana a nkhosa amphongo,+ limodzi ndi nsembe zake zambewu+ ndiponso nsembe zake zachakumwa.+ Zimenezi ukazipereke paguwa lansembe la panyumba ya Mulungu wako,+ yomwe ili ku Yerusalemu.+ 18  “Zilizonse zimene iweyo ndi abale ako mudzaone kuti n’zabwino kuchita ndi siliva ndi golide wotsalayo,+ mogwirizana ndi chifuniro+ cha Mulungu wanu, mudzachite zimenezo.+ 19  Ziwiya+ zimene ukupatsidwa kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wa panyumba ya Mulungu wako, ukazipereke zonse ku Yerusalemu n’kukaziika pamaso pa Mulungu.+ 20  Zinthu zina zonse zofunika panyumba ya Mulungu wako zimene ukuyenera kupereka, udzazitenge kunyumba ya mfumu yosungiramo chuma.+ 21  “Ineyo mfumu Aritasasita ndalamula+ asungichuma onse+ amene ali kutsidya lina la Mtsinje,*+ kuti chilichonse chimene wansembe Ezara,+ wokopera chilamulo cha Mulungu wakumwamba, angapemphe kwa inu chichitidwe mwamsanga. 22  Mum’patse ngakhale matalente* 100+ a siliva, tirigu wokwana miyezo 100 ya kori,*+ vinyo+ wokwana mitsuko*+ 100, mafuta okwana mitsuko 100,+ ndi mchere+ wochuluka. 23  Zonse zimene Mulungu wakumwamba+ walamula+ zokhudza nyumba yake, zichitike modzipereka kwambiri+ kuti mkwiyo usayakire dziko la mfumu ndiponso usayakire ana ake.+ 24  Amuna inu mudziwe kuti ansembe,+ Alevi,+ oimba,+ alonda a pakhomo,+ Anetini,+ ndi anthu ogwira ntchito panyumba ya Mulunguyi, musawakhometse msonkho umene munthu aliyense amakhoma, msonkho wakatundu,+ kapena msonkho wapanjira.+ 25  “Iweyo Ezara, pogwiritsa ntchito nzeru+ zimene Mulungu wako wakupatsa, uike anthu osungitsa malamulo ndi oweruza kuti nthawi zonse aziweruza+ anthu onse a kutsidya lina la Mtsinje, ngakhalenso onse odziwa malamulo a Mulungu wako. Aliyense wosadziwa malamulowo, amuna inu mum’phunzitse.+ 26  Aliyense wosatsatira chilamulo cha Mulungu wako+ ndi chilamulo cha mfumu, azipatsidwa chiweruzo msangamsanga, kaya choti aphedwe,+ athamangitsidwe,+ alipitsidwe ndalama,+ kapena aikidwe m’ndende.” 27  Atamandike Yehova Mulungu wa makolo athu,+ amene waika maganizo amenewa mumtima+ mwa mfumu, kuti nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu ikongoletsedwe.+ 28  Iye wandisonyeza kukoma mtima kosatha+ pamaso pa mfumu, pamaso pa aphungu ake,+ ndi pamaso pa akalonga onse amphamvu a mfumu. Ineyo ndinadzilimbitsa chifukwa dzanja+ la Yehova Mulungu wanga linali pa ine, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri a Aisiraeli kuti apite nane limodzi.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.