Ezara 6:1-22

6  Panali pa nthawi imeneyi pamene mfumu Dariyo inaika lamulo loti afufuze ndipo anafufuza m’nyumba yosungiramo mabuku ofotokoza mbiri yakale,+ momwe analinso kusungiramo zinthu zamtengo wapatali zimene zinaikidwa ku Babuloko.  Ku malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri a ku Ekibatana, m’chigawo cha dziko la Amedi,+ anapezako mpukutu. Mumpukutuwo munalembedwa uthenga wakuti:  “M’chaka choyamba cha Mfumu Koresi,+ mfumuyo inaika lamulo lokhudza nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu lakuti: Ayuda amangenso nyumbayo kuti azikapereka nsembe+ kumeneko, ndipo amange maziko olimba. Nyumbayo kutalika kwake kuchokera pansi kufika pamwamba ikhale mikono* 60, ndiponso m’lifupi mwake ikhale mikono 60.+  Ikhale ndi mizere itatu ya miyala yochita kuigubuduzira+ pamalopo ndi mzere umodzi wa matabwa.+ Ndalama zake zichokere kunyumba ya mfumu.+  Komanso ziwiya zagolide ndi zasiliva+ za m’nyumba ya Mulungu, zimene Nebukadinezara+ anazichotsa m’kachisi yemwe anali ku Yerusalemu n’kuzipititsa ku Babulo, zibwezedwe kuti zipite kumalo ake, kukachisi amene ali ku Yerusalemu ndipo zikaikidwe m’nyumba ya Mulungu.+  “Tsopano inu Tatenai+ bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,*+ Setara-bozenai+ ndi anzanu ndiponso abwanamkubwa aang’ono+ amene ali kutsidya lina la Mtsinje, musakasokoneze kumeneko.+  Musakalowerere ntchito yomanga nyumba ya Mulunguyo.+ Bwanamkubwa wa Ayuda ndi akulu a Ayuda amanganso nyumba ya Mulunguyo pamalo ake.  Ineyo ndaika lamulo+ lokhudza zimene muyenera kuchita ndi akulu a Ayuda amenewa pa ntchito yomanganso nyumba ya Mulungu. Amuna amenewa muziwapatsa+ ndalama mosalekeza+ zochokera pa chuma cha mfumu+ zomwe anthu a kutsidya la Mtsinje amapereka pokhoma msonkho.  Komanso muziwapatsa zinthu zofunika monga ng’ombe zing’onozing’ono zamphongo,+ nkhosa zamphongo,+ ndi ana a nkhosa+ kuti azipereka nsembe yopsereza kwa Mulungu wakumwamba. Muziwapatsanso tirigu,+ mchere,+ vinyo+ ndi mafuta+ monga mmene anganenere ansembe amene ali ku Yerusalemu. Musalephere kuwapatsa zinthu zimenezi tsiku ndi tsiku mosalekeza. 10  Muziwapatsa zimenezi kuti nthawi zonse+ azipereka nsembe zoziziritsa mtima+ kwa Mulungu wakumwamba, ndiponso kuti azipempherera moyo wa mfumu ndi ana ake.+ 11  Ndaikanso lamulo lakuti aliyense wophwanya+ lamulo limeneli, thabwa+ lidzazulidwa panyumba yake ndipo iye adzapachikidwa+ pathabwalo. Komanso nyumba yake idzasandutsidwa chimbudzi cha aliyense chifukwa cha zimenezi.+ 12  Mulungu amene anaika dzina lake+ kumeneko, achotse mfumu iliyonse ndi anthu alionse ophwanya lamulo limeneli ndiponso owononga+ nyumba ya Mulungu imene ili ku Yerusalemu. Ine Dariyo ndaika lamulo limeneli, ndipo zichitike mwamsanga.” 13  Kenako Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,+ Setara-bozenai+ ndi anzawo anachita mogwirizana ndi mawu amene mfumu Dariyo inatumiza. Anachita zimenezi mwamsanga. 14  Tsopano akulu+ a Ayuda anali kupita patsogolo pa ntchito yomanga+ nyumbayo atalimbikitsidwa ndi ulosi wa mneneri Hagai+ ndi Zekariya+ mdzukulu wa Ido.+ Iwo anamanga nyumbayo ndi kuimaliza potsatira lamulo la Mulungu wa Isiraeli,+ ndi lamulo la Koresi,+ Dariyo,+ ndi Aritasasita+ mfumu ya Perisiya. 15  Iwo anali atamaliza kumanga nyumbayo pofika tsiku lachitatu la mwezi wa Adara,+ m’chaka cha 6 cha ulamuliro wa mfumu Dariyo. 16  Ndiyeno ana a Isiraeli, ansembe, Alevi+ ndi anthu ena onse amene anachokera ku ukapolo,+ anatsegulira+ nyumba ya Mulunguyo mosangalala. 17  Pamwambo wotsegulira nyumba ya Mulunguyo, anapereka nsembe ng’ombe zamphongo 100, nkhosa zamphongo 200, ndi ana a nkhosa amphongo 400. Anaperekanso mbuzi zamphongo 12 za nsembe ya machimo ya ana onse a Isiraeli mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a Isiraeli.+ 18  Kenako anaika ansembe ndi Alevi m’magulu awo+ kuti azichita utumiki wa Mulungu ku Yerusalemu, mogwirizana ndi malangizo a m’buku la Mose.+ 19  Anthu amene anachokera ku ukapolowo anachita pasika+ pa tsiku la 14 la mwezi woyamba.+ 20  Chifukwa chakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa+ monga gulu limodzi, onse anali oyera. Choncho Aleviwo anapha nyama ya pasika+ ya anthu onse amene anachokera ku ukapolo, ya abale awo ansembe, ndiponso yawo. 21  Ndiyeno ana a Isiraeli amene anabwera kuchokera ku ukapolo anadya+ nyamayo. Komanso aliyense amene anadzilekanitsa ku zonyansa+ za anthu a mitundu ina ya m’dzikolo n’kubwera kwa iwo ndi kufunafuna Yehova Mulungu wa Isiraeli, anadya nawo.+ 22  Kwa masiku 7, iwo anachita mosangalala chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ pakuti Yehova anawachititsa kusangalala. Iye anatembenuzira+ kwa iwo mtima wa mfumu ya Asuri kuti ilimbitse manja awo pa ntchito yomanga nyumba ya Mulungu woona, Mulungu wa Isiraeli.

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.