Ezara 4:1-24

4  Adani+ a Yuda ndi Benjamini atamva kuti anthu amene anabwera kuchokera ku ukapolo+ akumangira kachisi Yehova Mulungu wa Isiraeli,  nthawi yomweyo anapita kwa Zerubabele+ ndi kwa atsogoleri+ a nyumba za makolo n’kukawauza kuti: “Bwanji timangire nanu limodzi,+ popeza ifeyo mofanana ndi inuyo, timapembedza Mulungu wanu+ ndipo timapereka nsembe kwa iye, kuyambira m’masiku a Esari-hadoni+ mfumu ya Asuri, yemwe anatibweretsa kuno.”+  Koma Zerubabele, Yesuwa,+ ndi atsogoleri ena onse+ a nyumba za makolo za Isiraeli anawayankha kuti: “Mulibe ufulu womanga nafe limodzi nyumba ya Mulungu wathu,+ pakuti ifeyo patokha timangira limodzi nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, monga momwe Mfumu Koresi+ ya Perisiya yatilamulira.”  Kuyambira pamenepo, anthu a m’dzikolo anakhala akufooketsa+ manja a anthu a ku Yuda ndi kuwagwetsa ulesi pa ntchito yomanga.+  Komanso, anali kulemba ntchito+ aphungu kuti alepheretse zolinga zawo masiku onse a Koresi mfumu ya Perisiya, mpaka ulamuliro wa Dariyo+ mfumu ya Perisiya.  Mu ulamuliro wa Ahasiwero, kumayambiriro kwa ulamuliro wake, iwo analemba kalata yoneneza+ anthu okhala ku Yuda ndi ku Yerusalemu.  Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli, ndi anzake ena onse analemba kalata kwa Aritasasita mfumu ya Perisiya m’masiku a mfumuyo. Kalatayo anaimasulira m’Chiaramu n’kuilemba m’zilembo za Chiaramu.+  Rehumu mtsogoleri wa akulu a boma ndi Simusai mlembi, analemba kalata kwa mfumu Aritasasita yotsutsana ndi Yerusalemu, kuti:  Kuchokera kwa Rehumu+ mtsogoleri wa akulu a boma, Simusai mlembi, anzawo ena onse monga oweruza ndi abwanamkubwa aang’ono a kutsidya lina la Mtsinje,*+ alembi+ ena, anthu a ku Ereke,+ Ababulo,+ anthu okhala ku Susa,+ kapena kuti Aelamu,+ 10  mitundu ina yonse+ imene Asinapera+ wamkulu ndi wolemekezeka anaitenga ukapolo n’kukaiika m’mizinda ya ku Samariya,+ ndi ena onse a kutsidya lina la Mtsinje . . . Tsopano 11  izi n’zimene analemba m’kalata imene anatumizayo: “Kwa mfumu Aritasasita,+ kuchokera kwa ife akapolo anu, amuna a kutsidya lina la Mtsinje: Tsopano 12  inu mfumu dziwani kuti Ayuda amene anachokera kwa inu n’kudzatipeza kuno, ali ku Yerusalemu. Iwo akumanga mzinda woukira ndi woipa uja, ndipo akumanga mpanda+ ndi kukonzanso maziko ake. 13  Ndiyeno inu mfumu dziwani kuti, mzinda umenewu ukamangidwanso, mpanda wake n’kumalizidwa, anthu amenewa asiya kupereka msonkho umene munthu aliyense amapereka,+ msonkho wakatundu,+ ndi msonkho wapanjira ndipo zimenezi zidzachititsa kuti chuma+ cha mafumu chiwonongeke. 14  Tsopano popeza ife timalandira malipiro ochokera kunyumba yachifumu,* si bwino kuti tingolekerera kuti inu mfumu chuma chanu chiwonongeke. Pa chifukwa chimenechi, tatumiza kalatayi kuti tikudziwitseni zimenezi inu mfumu 15  n’cholinga choti mufufuze m’buku la mbiri+ ya makolo anu. Mukafufuza m’bukulo mupeza kuti mzinda umenewu ndi mzinda woukira ndi wowonongetsa chuma cha mafumu ndi zigawo za mayiko. Mupezanso kuti mumzinda umenewu mwakhala muli anthu oyambitsa kupanduka kuyambira kalekale. N’chifukwa chake mzindawu uli bwinja.+ 16  Tikukudziwitsani mfumu kuti mzinda umenewu ukamangidwanso, mpanda wake n’kumalizidwa, ndithu simudzakhala ndi gawo kutsidya lino la Mtsinje.”+ 17  Ndiyeno mfumuyo inatumiza mawu kwa Rehumu+ mtsogoleri wa akulu a boma, Simusai mlembi, anzawo ena onse+ amene anali kukhala ku Samariya, ndi kwa ena onse okhala kutsidya lina la Mtsinje. Mawuwo anali akuti: “Moni!+ 18  Kalata imene mwatitumizira aiwerenga momveka bwino pamaso panga. 19  Choncho ine ndinalamula kuti afufuze, ndipo atafufuza+ apeza kuti mzinda umenewo kuyambira kale wakhala ukuukira mafumu, ndiponso anthu a mumzindawo akhala akupanduka ndi kugalukira.+ 20  Panali mafumu amphamvu+ olamulira Yerusalemu ndi dera lonse la kutsidya lina la Mtsinje+ ndipo anali kupatsidwa msonkho umene munthu aliyense amapereka, msonkho wakatundu, ndi msonkho wapanjira.+ 21  Tsopano ikani lamulo loti amuna amenewa asiye ntchitoyo, ndi kuti mzinda umenewo usamangidwenso kufikira ine ndikadzalamula. 22  Muonetsetse kuti musanyalanyaze kuchita zimenezi kuti vuto limeneli lingakule, zomwe zingapweteketse mafumu.”+ 23  Mawu amene analembedwa m’kalata ya mfumu Aritasasita atawerengedwa pamaso pa Rehumu,+ Simusai+ mlembi, ndi anzawo,+ iwo anapita msangamsanga kwa Ayuda ku Yerusalemu n’kukawaletsa ntchitoyo mwankhondo.+ 24  Panali pa nthawi imeneyi pamene ntchito yomanga nyumba ya Mulungu, imene inali ku Yerusalemu, inaima ndipo inakhala chiimire mpaka chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo+ mfumu ya Perisiya.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Mawu ake enieni, “timadya mchere wa kunyumba yachifumu.”