Ezara 3:1-13

3  Pofika mwezi wa 7,+ ana a Isiraeli anali akukhala m’mizinda yawo. Ndiyeno anthuwo anayamba kusonkhana ku Yerusalemu+ monga munthu mmodzi.+  Kenako Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ndi abale ake ansembe, ndiponso Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi abale ake, ananyamuka n’kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Isiraeli kuti aziperekerapo nsembe zopsereza, mogwirizana ndi zimene zinalembedwa+ m’chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu woona.  Chotero iwo anamanga guwa lansembe lolimba pamalo ake+ akale, chifukwa anali kuopa anthu a mitundu ina.+ Atatero anayamba kuperekerapo nsembe zopsereza kwa Yehova, zam’mawa ndi zamadzulo.+  Kenako iwo anachita chikondwerero cha misasa+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.+ Pachikondwererochi, anthuwo anali kubweretsa nsembe zopsereza paguwa lansembe tsiku ndi tsiku, mogwirizana ndi lamulo la nsembe zimene zinayenera kuperekedwa tsiku lililonse.+  Ndiyeno anayamba kupereka nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku,+ nsembe ya masiku okhala mwezi,+ ndi nsembe za panyengo zonse zochita zikondwerero zopatulika+ za Yehova. Analinso kupereka nsembe za aliyense amene anapereka chopereka chaufulu+ kwa Yehova ndi mtima wonse.  Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wa 7+ kupita m’tsogolo, anthuwo anayamba kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Pa nthawiyi n’kuti maziko a kachisi wa Yehova asanamangidwe.  Kenako anthuwo anapereka ndalama+ kwa anthu osema miyala+ ndi kwa amisiri,+ ndiponso anapereka chakudya,+ zakumwa ndi mafuta+ kwa Asidoni+ ndi kwa anthu a ku Turo,+ kuti abweretse matabwa a mkungudza kuchokera ku Lebanoni+ n’kudzawasiya m’mphepete mwa nyanja ku Yopa.+ Anachita zimenezi malinga ndi chilolezo chimene Koresi+ mfumu ya ku Perisiya anawapatsa.  M’chaka chachiwiri kuchokera pamene anabwera kunyumba ya Mulungu woona ku Yerusalemu, m’mwezi wachiwiri,+ Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli,+ Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki, abale awo onse, ansembe ndi Alevi, ndiponso anthu ena onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo,+ anayamba kugwira ntchitoyo. Kenako anaika Alevi+ m’malo awo kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo kuti akhale oyang’anira ntchito ya panyumba ya Yehova.+  Chotero Yesuwa,+ ana ake ndi abale ake, Kadimiyeli ndi ana ake, ndi ana a Yuda,* ananyamuka monga gulu limodzi kukayang’anira anthu ogwira ntchito m’nyumba ya Mulungu woona. Komanso panali ana a Henadadi,+ ana awo ndi abale awo, omwe anali Alevi. 10  Tsopano anthu amene anali kugwira ntchito yomanga nyumbayo anamaliza kumanga maziko+ a kachisi wa Yehova. Atatero, ansembe ovala zovala zaunsembe+ omwe ananyamula malipenga,+ ndiponso Alevi ana a Asafu+ omwe ananyamula zinganga,+ anaimirira kuti atamande Yehova motsatira dongosolo+ limene Davide mfumu ya Isiraeli anakhazikitsa. 11  Iwo anayamba kuimba molandizana potamanda+ ndi kuthokoza Yehova kuti, “iye ndi wabwino,+ pakuti kukoma mtima kosatha kumene amakusonyeza kwa Isiraeli kudzakhala mpaka kalekale.”*+ Ndipo anthu onse anafuula mokweza kwambiri+ potamanda Yehova chifukwa cha kumangidwa kwa maziko a nyumba ya Yehova. 12  Ansembe+ ndi Alevi ambiri, omwe anali atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ amuna okalamba amene anaona nyumba yoyambirira,+ anali kulira+ mokweza chifukwa cha kumangidwa kwa maziko+ a nyumbayo pamaso pawo, ndipo enanso ambiri anali kufuula mosangalala.+ 13  Chotero anthu sanathe kusiyanitsa phokoso lawo losonyeza kusangalala+ ndi losonyeza kulira, chifukwa anthuwo anali kufuula kwambiri, ndipo phokoso lawo linali kumveka kutali kwambiri.

Mawu a M'munsi

Akutchedwa Hodaviya pa Eza 2:40, ndipo pa Ne 7:43 akutchedwa Hodeva.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.