Ezara 2:1-70

2  Awa ndiwo anali anthu a m’chigawo*+ amene anatuluka mu ukapolo+ wa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera+ ku Babulo. Anthuwa anabwerera+ ku Yerusalemu ndi ku Yuda,+ aliyense kumzinda wakwawo.  Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,*+ Nehemiya, Seraya,+ Reelaya, Moredekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, ndi Bana. Chiwerengero cha amuna a Isiraeli chinali ichi:  Ana a Parosi,+ 2,172.  Ana a Sefatiya,+ 372.  Ana a Ara,+ 775.  Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu,+ 2,812.  Ana a Elamu,+ 1,254.  Ana a Zatu,+ 945.  Ana a Zakai,+ 760. 10  Ana a Bani,+ 642. 11  Ana a Bebai,+ 623. 12  Ana a Azigadi,+ 1,222. 13  Ana a Adonikamu,+ 666. 14  Ana a Bigivai,+ 2,056. 15  Ana a Adini,+ 454. 16  Ana a Ateri,+ a m’nyumba ya Hezekiya, 98. 17  Ana a Bezai,+ 323. 18  Ana a Yora, 112. 19  Ana a Hasumu,+ 223. 20  Ana a Gibara,+ 95. 21  Ana a Betelehemu,+ 123. 22  Amuna a ku Netofa,+ 56. 23  Amuna a ku Anatoti,+ 128. 24  Ana a Azimaveti,+ 42. 25  Ana a Kiriyati-yearimu,+ Kefira ndi Beeroti, 743. 26  Ana a Rama+ ndi Geba,+ 621. 27  Amuna a ku Mikemasi,+ 122. 28  Amuna a ku Beteli+ ndi a ku Ai,+ 223. 29  Ana a Nebo,+ 52. 30  Ana a Magabisi, 156. 31  Ana a Elamu+ wina, 1,254. 32  Ana a Harimu,+ 320. 33  Ana a Lodi,+ Hadidi+ ndi Ono,+ 725. 34  Ana a Yeriko,+ 345. 35  Ana a Senaya,+ 3,630. 36  Ansembe:+ Ana a Yedaya,+ a m’nyumba ya Yesuwa,+ 973. 37  Ana a Imeri,+ 1,052. 38  Ana a Pasuri,+ 1,247. 39  Ana a Harimu,+ 1,017. 40  Alevi:+ Ana a Yesuwa,+ a m’nyumba ya Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodaviya,+ 74. 41  Oimba, ana a Asafu,+ 128. 42  Ana a alonda a pachipata, omwe anali ana a Salumu,+ ana a Ateri,+ ana a Talimoni,+ ana a Akubu,+ ana a Hatita,+ ndi ana a Sobai, onse analipo 139. 43  Anetini:+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,+ 44  ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni,+ 45  ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu, 46  ana a Hagabu, ana a Salimai,+ ana a Hanani, 47  ana a Gideli, ana a Gahara,+ ana a Reyaya, 48  ana a Rezini,+ ana a Nekoda, ana a Gazamu, 49  ana a Uziza, ana a Paseya,+ ana a Besai, 50  ana a Asena, ana a Meyuni, ana a Nefusimu,+ 51  ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,+ 52  ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa,+ 53  ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,+ 54  ana a Neziya, ana a Hatifa.+ 55  Ana a atumiki a Solomo:+ Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,+ 56  ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli,+ 57  ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu, ana a Ami.+ 58  Anetini+ onse pamodzi ndi ana a atumiki a Solomo analipo 392.+ 59  Ndiyeno amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ndipo sanathe kupereka umboni wotsimikizira kumene anachokera komanso kuti makolo awo+ anali Aisiraeli, ndi awa: 60  ana a Delaya, ana a Tobia, ndi ana a Nekoda,+ 652. 61  Ana a ansembe+ anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi,+ ana a Barizilai+ amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ Mgiliyadi n’kuyamba kutchedwa ndi dzina lawo. 62  Amenewa ndiwo anayang’ana mayina awo m’kaundula kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira koma sanapezekemo. Zitatero anawaletsa kuti asatumikire monga ansembe chifukwa anali oipitsidwa.+ 63  Pa chifukwa chimenechi, Tirisata*+ anawauza kuti sayenera kudya+ zinthu zopatulika koposa, kufikira patakhala wansembe wokhala ndi Urimu+ ndi Tumimu. 64  Mpingo wonsewo monga gulu limodzi+ unali ndi anthu 42,360,+ 65  kupatulapo akapolo awo aamuna ndi akapolo awo aakazi amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna+ ndi aakazi 200. 66  Anali ndi mahatchi* 736 ndi nyulu* 245.+ 67  Ngamila zawo zinalipo 435. Abulu awo analipo 6,720.+ 68  Atsogoleri ena+ a nyumba za makolo awo+ atafika kunyumba ya Yehova+ imene inali ku Yerusalemu,+ anapereka zopereka zaufulu+ kunyumba ya Mulungu woona kuti imangidwe pamalo ake.+ 69  Mogwirizana ndi chuma chawo, anapereka golide+ kuti athandize pa ntchitoyo wokwana madalakima* 61,000, siliva+ wokwana ma mina* 5,000 ndi mikanjo 100+ ya ansembe. 70  Ndiyeno ansembe, Alevi, anthu ena,+ oimba, alonda a pazipata, Anetini ndi Aisiraeli onse anayamba kukhala m’mizinda yawo.+

Mawu a M'munsi

N’kutheka kuti chimenechi chinali chigawo cha Babulo.
Akutchedwa “Yoswa” pa Hag 1:1 ndi Zek 3:1.
Dzina lakuti “Tirisata” ndi dzina laulemu lachiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.
Nthawi zambiri “dalakima” anali kuifanizira ndi ndalama yagolide ya ku Perisiya yotchedwa dariki, yomwe inali yolemera magalamu 8.4. Imeneyi si dalakima ya ku Malemba Achigiriki.
Onani Zakumapeto 12.