Ezara 10:1-44

10  Tsopano Ezara atangomaliza kupemphera+ ndi kuvomereza machimo,+ komwe ankachita akulira ndiponso ali chogona+ patsogolo pa nyumba+ ya Mulungu woona, Aisiraeli anasonkhana kwa iye. Iwo anali mpingo waukulu kwambiri, amuna, akazi ndi ana, ndipo anali atalira kwambiri.  Kenako Sekaniya mwana wa Yehiela+ wochokera mwa ana a Elamu+ anauza Ezara kuti: “Ifeyo tachita zosakhulupirika kwa Mulungu wathu, chifukwa tinatenga akazi achilendo kuchokera kwa anthu a mitundu ina.+ Koma tsopano Aisiraeli ali ndi chiyembekezo+ pa nkhani imeneyi.  Tsopano tiyeni tichite pangano+ ndi Mulungu wathu, lakuti tisiya+ akazi onse amenewa ndi ana awo mogwirizana ndi lamulo la Yehova ndi la anthu amene akunjenjemera+ chifukwa cha lamulo+ la Mulungu wathu, kuti zinthu zichitike mogwirizana ndi lamulo.+  Choncho iweyo nyamuka, chifukwa nkhaniyi ili m’manja mwako ndipo ife tili nawe. Limba mtima ndi kuchitapo kanthu.”  Pamenepo Ezara ananyamuka ndipo anauza atsogoleri a ansembe, a Alevi ndi a Aisiraeli onse kuti alumbire+ kuti achita mogwirizana ndi mawu amenewa. Choncho iwo analumbira.  Tsopano Ezara anachoka panyumba ya Mulungu woona n’kupita kuchipinda chodyera+ cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu. Ngakhale kuti anapita kumeneko, sanadye mkate+ kapena kumwa madzi, chifukwa anali kumva chisoni+ ndi kusakhulupirika kwa anthu ochokera ku ukapolo aja.  Kenako anauza anthu kuti alengeze mu Yuda ndi Yerusalemu yense kwa anthu onse amene anachokera ku ukapolo+ kuti asonkhane ku Yerusalemu,  ndi kuti aliyense amene sabwera+ potha masiku atatu mogwirizana ndi lamulo la akalonga+ ndi akulu, katundu wake yense alandidwa+ ndipo iyeyo achotsedwa+ pa khamu la anthu amene anachokera ku ukapolo.  Choncho amuna onse a fuko la Yuda ndi la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu m’masiku atatu, ndipo umu munali m’mwezi wa 9,+ pa tsiku la 20 la mweziwo. Anthu onsewo anakhala pabwalo la nyumba ya Mulungu woona, akunjenjemera poganizira nkhaniyo komanso chifukwa kunali kugwa mvula yamvumbi.+ 10  Patapita nthawi wansembe Ezara anaimirira n’kuuza anthuwo kuti: “Inuyo mwachita zosakhulupirika chifukwa mwatenga akazi achilendo+ n’kuwonjezera pa machimo a Isiraeli.+ 11  Tsopano vomerezani+ machimo anu kwa Yehova Mulungu wa makolo anu, ndipo chitani zomusangalatsa+ ndi kudzipatula kwa anthu a mitundu ina ndiponso kwa akazi achilendo.”+ 12  Pamenepo mpingo wonsewo unayankha ndi mawu okweza kuti: “Tichita ndendende mogwirizana ndi mawu anuwo.+ 13  Komabe, tilipo anthu ambiri ndipo ino ndi nyengo ya mvula yamvumbi, choncho n’zosatheka kuima panja. Komanso nkhani imeneyi sitenga tsiku limodzi kapena masiku awiri chifukwa tachimwa kwambiri pa nkhani imeneyi. 14  Choncho aloleni akalonga+ athu kuti aimire mpingo wonse ndipo anthu onse a m’mizinda yathu amene atenga akazi achilendo, abwere pa nthawi zimene zikhazikitsidwe. Abwere limodzi ndi akulu a mzinda uliwonse ndi oweruza ake, mpaka titathetsa mkwiyo wa Mulungu wathu umene watiyakira pa nkhani imeneyi.” 15  (Koma Yonatani mwana wa Asaheli ndi Yahazeya mwana wa Tikiva anatsutsa+ zimenezi, ndipo Mesulamu ndi Sabetai,+ omwe anali Alevi, anawathandiza.) 16  Anthu amene anachokera ku ukapolowo+ anatsatira dongosolo limenelo, ndipo wansembe Ezara ndi amuna onse amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ omwe anachita kuwatchula mayina awo, anachoka pakati pa anthuwo n’kukakhala pansi kuti afufuze nkhaniyo,+ kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wa 10.+ 17  Pomalizira pake, pofika pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, anamaliza kufufuza amuna onse amene anatenga akazi achilendo.+ 18  Iwo anapeza kuti ana ena a ansembe+ anatenga akazi achilendo. Kuchokera pa ana a Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki+ ndi abale ake, panali Maaseya, Eliezere, Yaribi ndi Gedaliya. 19  Koma iwo analonjeza mwa kugwirana chanza kuti asiya akazi awo ndi kuti popeza anali atachimwa,+ nkhosa yamphongo iperekedwa+ chifukwa cha tchimo lawolo. 20  Pa ana a Imeri+ panali Haneni ndi Zebadiya. 21  Pa ana a Harimu+ panali Maaseya, Eliya, Semaya, Yehiela ndi Uziya. 22  Pa ana a Pasuri+ panali Elioenai, Maaseya, Isimaeli, Netaneli, Yozabadi ndi Eleasa. 23  Pa Alevi panali Yozabadi, Simeyi, Kelaya (kapena kuti Kelita), Petahiya, Yuda ndi Eliezere. 24  Pa oimba panali Eliyasibu. Pa alonda a pachipata panali Salumu, Telemu ndi Uri. 25  Kuchokera pa Aisiraeli, pa ana a Parosi+ panali Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eleazara, Malikiya ndi Benaya. 26  Pa ana a Elamu+ panali Mataniya, Zekariya, Yehiela,+ Abidi, Yeremoti ndi Eliya. 27  Pa ana a Zatu+ panali Elioenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi ndi Aziza. 28  Pa ana a Bebai+ panali Yehohanani, Hananiya, Zabai ndi Atilai. 29  Pa ana a Bani panali Mesulamu, Maluki, Adaya, Yasubi, Seali ndi Yeremoti. 30  Pa ana a Pahati-mowabu+ panali Adena, Kelali, Benaya, Maaseya, Mataniya, Bezaleli, Binui ndi Manase. 31  Pa ana a Harimu+ panali Eliezere, Isihiya, Malikiya,+ Semaya, Simeoni, 32  Benjamini, Maluki ndi Semariya. 33  Pa ana a Hasumu+ panali Matenai, Mateta, Zabadi, Elifeleti, Yeremai, Manase ndi Simeyi. 34  Pa ana a Bani panali Maadai, Amuramu, Ueli, 35  Benaya, Bedeya, Kelui, 36  Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, 37  Mataniya, Matenai ndi Yaasu. 38  Pa ana a Binui panali Simeyi, 39  Selemiya, Natani, Adaya, 40  Makinadebai, Sasai, Sarayi, 41  Azareli, Selemiya, Semariya, 42  Salumu, Amariya ndi Yosefe. 43  Pa ana a Nebo panali Yeyeli, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yoweli ndi Benaya. 44  Onsewa anali atatenga akazi achilendo,+ ndipo akaziwo ndi ana awo anawatumiza kwawo.

Mawu a M'munsi