Ezara 1:1-11

1  M’chaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya, Yehova analimbikitsa+ mtima wa Koresi mfumu ya Perisiya kuti mawu a Yehova kudzera mwa Yeremiya+ akwaniritsidwe. Pamenepo Koresiyo anatumiza mawu amene analengezedwa+ mu ufumu wake wonse. Mawuwo analembedwanso m’makalata,+ kuti:  “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti,+ ‘Yehova Mulungu wakumwamba+ wandipatsa+ maufumu onse a padziko lapansi. Iye wandituma kuti ndim’mangire nyumba ku Yerusalemu+ m’dziko la Yuda.  Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite ku Yerusalemu m’dziko la Yuda n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, yomwe inali ku Yerusalemu.+ Iye ndiye Mulungu woona.+  Aliyense amene akukhala monga mlendo+ kumalo alionse, anthu akwawo amuthandize ndi siliva, golide, katundu, ziweto, limodzi ndi nsembe yaufulu+ ya nyumba ya Mulungu woona, yomwe inali ku Yerusalemu.’”  Ndiyeno atsogoleri+ a mabanja a fuko la Yuda, la Benjamini, ansembe, ndi Alevi, aliyense amene Mulungu woona analimbikitsa mtima wake,+ ananyamuka kuti apite kukamanganso nyumba ya Yehova,+ yomwe inali ku Yerusalemu.  Anthu onse okhala nawo pafupi anawathandiza*+ powapatsa ziwiya zasiliva, golide, katundu, ziweto, ndi zinthu zabwinozabwino, kuwonjezera pa zonse zimene zinaperekedwa mwaufulu.+  Komanso, Mfumu Koresi inabweretsa ziwiya za nyumba ya Yehova.+ Ziwiyazo n’zimene Nebukadinezara anatenga ku Yerusalemu+ n’kukaziika m’kachisi wa mulungu wake.+  Koresi mfumu ya Perisiya anatuma msungichuma Mitiredati yemwe anabweretsa ziwiyazo n’kuziwerenga. Atatero anazipereka kwa Sezibazara*+ mtsogoleri wa Yuda.+  Ziwiyazo zinali zochuluka chonchi: ziwiya 30 zagolide zooneka ngati mabasiketi, ziwiya 1,000 zasiliva zooneka ngati mabasiketi, ndi ziwiya 29 zowonjezera. 10  Panalinso mbale 30 zing’onozing’ono zolowa+ zagolide, mbale 410 zing’onozing’ono zolowa zasiliva zogwiritsira ntchito zina, ndi ziwiya zina 1,000. 11  Ziwiya zonse zagolide ndi zasiliva zinalipo 5,400 ndipo Sezibazara+ anabweretsa zonsezi ku Yerusalemu. Anatenganso anthu amene anagwidwa ukapolo+ kuchoka nawo ku Babulo n’kupita nawo ku Yerusalemu.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “anawalimbitsa manja.”
Akutchedwa “Zerubabele” pa Eza 2:2 ndi 3:8.