Deuteronomo 9:1-29

9  “Tamverani Aisiraeli inu, lero mukuwoloka Yorodano+ kulowa m’dziko limene mukukalilanda kwa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inuyo.+ Mukukalanda mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.+  yokhalanso ndi anthu amphamvu ndi aatali, ana a Anaki,+ amene inu mukuwadziwa ndipo munamva anthu akunena za iwo kuti, ‘Ndani angaime pamaso pa ana a Anaki?’  Ndipo inu mukudziwa bwino lero kuti Yehova Mulungu wanu akuwoloka patsogolo panu+ kuti akutsogolereni. Iye ndi moto wowononga.+ Adzawawononga+ ndipo iye ndi amene adzawagonjetsa inu mukuona. Pamenepo mudzawalande dziko lawo ndi kuwawononga mofulumira monga mmene Yehova wakuuzirani.+  “Yehova Mulungu wanu akadzawakankhira kutali ndi inu musadzanene mumtima mwanu kuti, ‘Yehova watilowetsa m’dziko lino kuti tilitenge kukhala lathu, chifukwa cha kulungama kwathu,’+ pamene kwenikweni Yehova akukankhira mitundu iyi kutali ndi inu chifukwa cha kuipa kwawo.+  Sikuti mukulowa m’dziko ili kukalitenga kukhala lanu chifukwa cha kulungama kwanu+ kapena chifukwa cha kuwongoka mtima kwanu.+ Yehova Mulungu wanu akukankhira mitundu iyi kutali ndi inu, kwenikweni chifukwa cha kuipa kwawo,+ ndiponso kuti Yehova akwaniritse mawu onse amene analumbirira makolo anu Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+  Muyenera kudziwa kuti Yehova Mulungu wanu akukupatsani dziko labwinoli osati chifukwa cha kulungama kwanu, pakuti ndinu anthu ouma khosi.+  “Kumbukirani izi: Simuyenera kuiwala mmene munaputira Yehova Mulungu wanu m’chipululu.+ Anthu inu mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova kuyambira tsiku limene munatuluka m’dziko la Iguputo mpaka kudzafika malo ano.+  Ngakhale ku Horebe, inu munaputa mkwiyo wa Yehova moti Yehova anakukwiyirani kwambiri mpaka kufika pofuna kukufafanizani.+  Nditakwera m’phiri kukalandira miyala iwiri yosema,+ miyala ya pangano limene Yehova anachita nanu,+ ndinakhala m’phirimo masiku 40, usana ndi usiku,+ (sindinadye mkate kapena kumwa madzi,) 10  ndipo Yehova anandipatsa miyala iwiri yosema imene chala cha Mulungu chinalembapo.+ Pamiyala iwiri imeneyi panali mawu onse amene Yehova analankhula nanu m’phiri, kuchokera pakati pa moto, tsiku limene munasonkhana kumeneko.+ 11  Ndipo atakwana masiku 40, usana ndi usiku, Yehova anandipatsa miyala iwiriyo, miyala ya pangano.+ 12  Pamenepo Yehova anandiuza kuti, ‘Nyamuka, tsika mofulumira m’phiri muno, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa ku Iguputo achita zinthu zowawonongetsa.+ Apatuka mofulumira panjira imene ndinawalamula kuyendamo. Adzipangira chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.’+ 13  Yehova anandiuza kuti, ‘Ndawaona anthu awa. Haa! Ndi anthu ouma khosi.+ 14  Ndileke ndiwawononge+ ndi kufafaniza dzina lawo pansi pa thambo,+ ndipo ndikupange mtundu wamphamvu ndi waukulu kwambiri kuposa iwo.’+ 15  “Kenako ndinatembenuka ndi kutsika m’phirimo pamene phirilo linali kuyaka moto,+ ndipo miyala iwiri ya pangano inali m’manja mwanga.+ 16  Nditayang’ana, ndinaona kuti mwachimwira Yehova Mulungu wanu. Munali mutadzipangira mwana wa ng’ombe wachitsulo chosungunula.+ Munali mutapatuka mofulumira panjira imene Yehova anakulamulani kuyendamo.+ 17  Pamenepo ndinatenga miyala iwiriyo ndi kuiponya pansi mwamphamvu ndi manja anga, ndi kuiswa inu mukuona.+ 18  Zitatero ndinadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova masiku 40, usana ndi usiku, ngati mmene ndinachitira poyamba. Sindinadye mkate kapena kumwa madzi+ chifukwa cha machimo anu onse amene munachita ndi kukhumudwitsa Yehova, mwa kuchita zinthu zoipa pamaso pake.+ 19  Pakuti ndinachita mantha chifukwa cha mkwiyo waukulu wa Yehova umene unakuyakirani, mpaka kufika pofuna kukufafanizani.+ Koma Yehova anandimveranso pa nthawi imeneyi.+ 20  “Yehova anakwiyiranso kwambiri Aroni, mpaka kufika pofuna kumuwononga.+ Koma ine ndinapembedzeranso Mulungu+ pa nthawi imeneyo kuti asawononge Aroni. 21  Ndipo mwana wa ng’ombeyo,+ amene munachimwa pomupanga, ndinamutenga n’kumutentha ndi moto ndi kumuphwanya, n’kumupera mpaka atakhala wosalala ngati fumbi. Kenako ndinamwaza fumbilo mumtsinje wotuluka m’phirimo.+ 22  “Kuwonjezera apo, pa Tabera,+ pa Masa+ ndi pa Kibiroti-hatava+ munaputanso mkwiyo wa Yehova.+ 23  Yehova atakutumani kuchokera ku Kadesi-barinea+ kuti, ‘Kwerani ndi kukatenga dziko limene ndidzakupatsani kuti likhale lanu,’ pamenepo munapandukiranso malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ ndipo simunasonyeze chikhulupiriro+ mwa iye komanso simunamvere mawu ake.+ 24  Mwasonyeza khalidwe lopandukira Yehova+ kuyambira tsiku limene ndinakudziwani. 25  “Chotero ndinadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova masiku 40, usana ndi usiku.+ Ndinadzigwetsa choncho chifukwa Yehova anati akufuna kukufafanizani.+ 26  Pamenepo ndinayamba kupembedzera+ Yehova ndi kunena kuti, ‘Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, musawononge anthu anu, amene ndiwo chuma chanu chapadera,+ anthu amene munawawombola ndi mphamvu yanu, amene munawatulutsa mu Iguputo+ ndi dzanja lamphamvu.+ 27  Kumbukirani atumiki anu Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.+ Musaone kuuma mtima kwa anthu awa ndi kuipa kwawo ndiponso tchimo lawo,+ 28  kuopera kuti anthu a m’dziko+ limene munatitulutsamo anganene kuti: “Chifukwa Yehova sanathe kuwalowetsa m’dziko limene anawalonjeza, komanso chifukwa chakuti anali kudana nawo, anawatulutsa kuti akawaphere m’chipululu.”+ 29  Iwo ndi anthu anube, chuma chanu chapadera,+ anthu amene munawatulutsa ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lotambasula.’+

Mawu a M'munsi