Deuteronomo 7:1-26
7 “Yehova Mulungu wako akadzakulowetsa m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako,+ adzakuchotsera mitundu ikuluikulu.+ Adzakuchotsera Ahiti,+ Agirigasi,+ Aamori,+ Akanani,+ Aperezi,+ Ahivi+ ndi Ayebusi,+ mitundu 7 ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iwe.+
2 Yehova Mulungu wako adzawapereka ndithu kwa iwe ndipo udzawagonjetse.+ Udzawawononge ndithu+ ndipo usadzachite nawo pangano kapena kuwakomera mtima.+
3 Usadzachite nawo mgwirizano wa ukwati. Usadzapereke ana ako aakazi kwa ana awo aamuna ndipo usadzatenge ana awo aakazi ndi kuwapereka kwa ana ako aamuna.+
4 Pakuti adzapatutsa ana ako aamuna kuti asanditsatire ndipo adzatumikira ndithu milungu ina.+ Pamenepo mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo adzakuwonongani ndithu mofulumira.+
5 “Koma inu mudzawachitire zotsatirazi: Mudzagwetse maguwa awo ansembe+ ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ Mudzadule+ mizati yawo yopatulika+ ndi kutentha zifaniziro zawo zogoba.+
6 Pakuti ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu.+ Yehova Mulungu wanu anakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera, mwa anthu onse okhala padziko lapansi.+
7 “Sikuti Yehova anakusonyezani chikondi ndi kukusankhani chifukwa chakuti munali ochuluka kuposa mitundu yonse,+ chifukwatu mtundu wanu unali waung’ono mwa mitundu yonse.+
8 Koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu+ kuti akulanditseni m’nyumba yaukapolo,+ m’manja mwa Farao mfumu ya Iguputo, chifukwa chakuti Yehova anakukondani,+ komanso chifukwa chosunga lumbiro lake limene analumbirira makolo anu.+
9 Ndipo iwe ukudziwa bwino kuti Yehova Mulungu wako ndi Mulungu woona,+ Mulungu wokhulupirika,+ wosunga pangano+ ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha kwa anthu amene amam’konda ndi kusunga malamulo ake ku mibadwo masauzande,+
10 koma wobwezera munthu wodana ndi Mulunguyo mwa kumuwononga+ pamasom’pamaso. Sadzazengereza kuwononga munthu amene amadana ndi Mulungu. Adzam’bwezera pamasom’pamaso.
11 Uzisunga malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene ndikukupatsa lero, mwa kuzitsatira.+
12 “Ndiyeno mukapitiriza kumvera zigamulo zimenezi ndi kuzisunga,+ Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano+ ndi kukusonyezani kukoma mtima kosatha, zimene analumbirira makolo anu.+
13 Ndipo adzakukondani ndithu, kukudalitsani,+ kukuchulukitsani+ ndi kudalitsa zipatso za mimba yanu+ ndi zipatso za nthaka yanu.+ Adzadalitsa mbewu zanu, vinyo wanu watsopano ndi mafuta anu, ana a ng’ombe zanu ndi ana a nkhosa zanu,+ m’dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.+
14 Inu mudzakhala odalitsika mwa anthu onse.+ Pakati panu sipadzapezeka mwamuna, mkazi kapena chiweto chosabereka.+
15 Yehova adzakuchotserani matenda onse. Ndipo sadzakugwetserani matenda onse oipa a ku Iguputo amene inu mukuwadziwa,+ koma adzawagwetsera pa onse odana nanu.
16 Muwononge anthu a mitundu yonse amene Yehova Mulungu wanu akuwapereka kwa inu.+ Musawamvere chisoni+ ndipo musatumikire milungu yawo+ chifukwa kuchita zimenezo kudzakutcherani msampha.+
17 “Ukaganiza mumtima mwako kuti, ‘Mitundu iyi yandikulira kwambiri. Ndingathe bwanji kuipitikitsa?’+
18 Usaiope.+ Nthawi zonse uzikumbukira zimene Yehova Mulungu wako anachitira Farao ndi Iguputo yense.+
19 Uzikumbukira mayesero aakulu amene maso ako anaona,+ zizindikiro, zozizwitsa+ ndiponso dzanja lamphamvu+ ndi mkono wotambasula+ umene Yehova Mulungu wako anakutulutsa nawo m’dzikolo.+ Umu ndi mmene Yehova Mulungu wako adzachitira ndi anthu a mitundu yonse amene ukuwaopa.+
20 Yehova Mulungu wako adzachititsanso mantha mitima yawo+ kufikira onse otsala+ ndiponso amene anali kubisala pamaso pako atawonongedwa.
21 Usachite nawo mantha pakuti Yehova Mulungu wako, Mulungu wamphamvu ndi wochititsa mantha,+ ali pakati panu.+
22 “Yehova Mulungu wako adzakankhira mitundu imeneyi kutali ndi iwe, kuichotsa pamaso pako pang’onopang’ono.+ Sadzakulola kuifafaniza mofulumira, kuopera kuti zilombo zakutchire zingakuchulukire ndi kukuwononga.
23 Yehova Mulungu wako adzawaperekadi kwa iwe ndi kuwabalalitsa atasokonezeka kwambiri, kufikira atawonongedwa.+
24 Adzapereka mafumu awo m’manja mwako,+ ndipo iwe udzafafanize mayina awo padziko lapansi.+ Palibe munthu amene adzaima kutsutsana ndi iwe+ kufikira utawafafaniza.+
25 Mudzatenthe zifaniziro zogoba za milungu yawo.+ Usadzalakelake siliva ndi golide wawo+ kapena kudzitengera zinthu zimenezi,+ kuopera kuti zingakutchere msampha,+ chifukwa zimenezi ndi zonyansa+ kwa Yehova Mulungu wako.
26 Usabweretse m’nyumba mwako zinthu zonyansa kuti iwenso ungawonongedwe mofanana ndi zinthuzo. Uzinyansidwa nazo kwambiri ndi kuipidwa nazo+ chifukwa zinthu zimenezi ndi zoyenera kuwonongedwa.+