Deuteronomo 5:1-33

5  Ndiyeno Mose anaitana Aisiraeli+ onse n’kuwauza kuti: “Inu Aisiraeli, mverani malangizo ndi zigamulo+ zimene ndikukuuzani lero, ndipo muziphunzire ndi kuzitsatira mosamala.+  Yehova Mulungu wathu anachita nafe pangano ku Horebe.+  Yehova sanachite pangano limeneli ndi makolo athu, koma ndi ife, tonsefe amene tili ndi moyo pano lero.  Yehova analankhula nanu pamasom’pamaso m’phiri, kuchokera pakati pa moto.+  Ine ndinaima pakati pa Yehova ndi inu pa nthawi imeneyo,+ kuti ndikuuzeni mawu a Yehova, (pakuti munali kuopa moto, ndipo simunakwere m’phirimo).+ Pamenepo iye anati,  “‘Ine ndine Yehova Mulungu wako,+ amene ndinakutulutsa m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo.+  Usakhale ndi milungu ina iliyonse motsutsana ndi ine.+  “‘Usadzipangire fano+ kapena chifaniziro+ cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cha m’madzi a pansi pa dziko lapansi.*  Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo,* chifukwa cha zolakwa za anthu odana ndi ine.+ 10  Koma ndimasonyeza kukoma mtima kosatha ku mibadwo masauzande chifukwa cha anthu amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga.+ 11  “‘Usagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wako mosasamala,+ pakuti Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina lake mosasamala osam’langa.+ 12  “‘Posunga tsiku la sabata ndi kuliona kukhala lopatulika, mmene Yehova Mulungu wako anakulamulira,+ 13  uzigwira ntchito zako zonse masiku 6.+ 14  Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wako.+ Usagwire ntchito iliyonse,+ iweyo kapena mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, kapolo wako wamwamuna, kapolo wako wamkazi, ng’ombe yako yamphongo, bulu wako, chiweto chako chilichonse, kapena mlendo wokhala mumzinda wanu,+ kuti nayenso kapolo wako wamwamuna ndi kapolo wako wamkazi, azipumula monga iwe.+ 15  Uzikumbukira kuti unali kapolo m’dziko la Iguputo+ ndipo Yehova Mulungu wako anakutulutsa kumeneko ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula.+ N’chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamula kuti uzisunga tsiku la sabata.+ 16  “‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako+ monga mmene Yehova Mulungu wako anakulamulira, kuti masiku ako atalike, ndi kuti zinthu zikuyendere bwino+ m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa. 17  “‘Usaphe munthu.*+ 18  “‘Usachite chigololo.+ 19  “‘Usabe.+ 20  “‘Usapereke umboni wonamizira mnzako.+ 21  “‘Usalakelake mkazi wa mnzako.+ Usalakelake mwadyera nyumba ya mnzako, munda wake, kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ng’ombe yake yamphongo, bulu wake, kapena chinthu chilichonse cha mnzako.’+ 22  “Yehova analankhula Mawu* amenewa mokweza kumpingo wanu wonse, kuchokera pakati pa moto m’phiri,+ pamene kunachita mtambo wakuda ndi mdima wandiweyani, ndipo pa Mawuwo sanawonjezerepo kalikonse. Kenako anawalemba pamiyala iwiri yosema n’kundipatsa.+ 23  “Ndiyeno mutangomva mawu amenewo kuchokera pamalo amdima, phiri likuyaka moto,+ munabwera kwa ine. Atsogoleri onse a mafuko anu ndi akulu anu onse anabwera kwa ine. 24  Pamenepo munati, ‘Yehova Mulungu wathu watisonyezatu ulemerero wake ndi ukulu wake, ndipo tamva mawu ake kuchokera pakati pa moto.+ Lero taona kuti Mulungu angalankhule ndi munthu, munthuyo n’kukhalabe ndi moyo.+ 25  Moto waukuluwu utipsereza.+ Tiferenji tsono? Tikapitiriza kumvetsera mawu a Yehova Mulungu wathu tifa basi.+ 26  Pakuti ndani mwa anthu onse amene anamvetserapo mawu a Mulungu wamoyo,+ akulankhula kuchokera pakati pa moto monga mmene tachitira ife n’kukhalabe ndi moyo? 27  Iweyo pita pafupi ukamvetsere zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena. Iweyo ndiye udzatiuze zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzakuuza,+ ndipo tidzamvera ndi kuchita zomwezo.’ 28  “Motero Yehova anamva mawu anu onse amene munalankhula nane, ndipo Yehova anapitiriza kundiuza kuti, ‘Ndamva mawu amene anthu awa akuuza. Mawu onse amene akuuza ali bwino.+ 29  Zikanakhala bwino kwambiri akanakhala ndi mtima wondiopa+ ndi kusunga malamulo anga+ nthawi zonse, kuti iwo ndi ana awo zinthu ziwayendere bwino mpaka kalekale!*+ 30  Pita ukawauze kuti: “Bwererani kumahema anu.” 31  Koma iwe ima pompano, ndipo ndikuuza malamulo onse, malangizo ndi zigamulo zimene uyenera kuwaphunzitsa+ kuti azikazitsatira m’dziko limene ndikuwapatsa kukhala lawo.’ 32  Ndipo anthu inu muonetsetse kuti mukuchita monga mmene Yehova Mulungu wanu wakulamulirani.+ Musatembenukire kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 33  Muyende m’njira yonse imene Yehova Mulungu wanu wakulamulani,+ kuti mukhale ndi moyo ndi kuti zinthu zikuyendereni bwino+ ndiponso kuti mutalikitsedi masiku anu m’dziko limene mudzalitenga kukhala lanu.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 20:4.
Kapena kuti “wolanga ana, m’badwo wachitatu ndi m’badwo wachinayi.”
Kapena kuti “Mulungu wansanje (wachangu); Mulungu wosalola aliyense kupikisana naye.”
Onani mawu a m’munsi pa Eks 20:13.
Pano, “Mawu” akutanthauza mawu olamula, kapena kuti malamulo. Onani Eks 34:28.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.