Deuteronomo 4:1-49

4  “Tsopano inu Aisiraeli, mverani malangizo ndi zigamulo zimene ndikukuphunzitsani kuti muzitsatira. Mukatero mudzakhala ndi moyo+ n’kukalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akukupatsani, ndi kukalitenga kukhala lanu.  Musawonjezepo kalikonse pa mawu amene ndikukulamulani, ndipo musachotsepo kalikonse pa mawu amenewa,+ kuti musunge malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani.  “Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita pa nkhani ya Baala wa ku Peori, kuti munthu aliyense amene anatsatira Baala wa ku Peori,+ Yehova Mulungu wanu anamuwononga ndi kum’chotsa pakati panu.+  Koma nonsenu amene mukumamatira+ kwa Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo lero.  Taonani, ndakuphunzitsani malangizo+ ndi zigamulo,+ monga mmene Yehova Mulungu wanga wandilamulira, kuti muzikatsatira zimenezo pamene mukukhala m’dziko limene mukupita kukalitenga kukhala lanu.  Ndipo muyenera kusunga malangizo ndi zigamulo zimenezi, chifukwa mukatero mudzakhala anzeru+ ndi ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa. Pamenepo, anthuwo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi ndi ozindikira.’+  Pakuti ndi mtundu winanso uti wamphamvu+ umene milungu yake ili pafupi nawo, monga mmene Yehova Mulungu wathu alili pafupi ndi ife, tikamaitanira pa iye+ nthawi zonse?  Ndipo ndi mtundu winanso uti wamphamvu umene uli ndi malangizo ndi zigamulo zolungama zofanana ndi chilamulo chonsechi chimene ndikukuikirani pamaso panu lero?+  “Koma khalani tcheru ndipo musamale moyo wanu,+ kuti musaiwale zinthu zimene maso anu anaona,+ ndi kuti mitima yanu isaiwale zinthu zimenezo masiku onse a moyo wanu.+ Ana anu ndi zidzukulu zanu muziwauza za zinthu zimenezo,+ 10  za tsiku limene munaimirira pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebe,+ pamene Yehova anandiuza kuti, ‘Sonkhanitsa anthu kwa ine kuti amve mawu anga,+ naphunzire kundiopa+ masiku onse amene iwo adzakhala ndi moyo padziko, ndi kuti aphunzitsenso ana awo.’+ 11  “Choncho anthu inu munayandikira ndi kuimirira m’munsi mwa phiri. Phiri limenelo linali kuyaka moto mpaka kumwamba, ndipo kunali mdima ndi mtambo wakuda.+ 12  Pamenepo Yehova anayamba kukulankhulani kuchokera pakati pa moto.+ Inu munamva mawu koma simunaone kalikonse.+ Munangomva mawu osaona kalikonse.+ 13  Pamenepo anakuuzani pangano lake,+ Mawu Khumi,*+ ndipo anakulamulani kuti muzilisunga. Kenako analemba Mawu Khumiwo pamiyala iwiri yosema.+ 14  Ndipo Yehova anandilamula pa nthawi imeneyo kuti ndikuphunzitseni malangizo ndi zigamulo, kuti muzikazitsatira pamene mukukhala m’dziko limene mukuwolokerako kukalitenga.+ 15  “Chotero musamale moyo wanu,+ chifukwa pa tsiku limene Yehova analankhula nanu kuchokera pakati pa moto ku Horebe, simunaone kalikonse+ m’motomo. 16  Musamale kuti musachite zinthu zokuwonongetsani,+ kutinso musadzipangire chifaniziro, chifaniziro cha chinthu chilichonse, chachimuna kapena chachikazi,+ 17  chifaniziro cha nyama iliyonse ya padziko lapansi,+ chifaniziro cha mbalame iliyonse youluka m’mlengalenga,+ 18  chifaniziro cha chinthu chilichonse chimene chimayenda panthaka, ndi chifaniziro cha nsomba iliyonse+ ya m’madzi a pansi pa dziko.* 19  Musamale kuti musakweze maso anu kuthambo ndi kuona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la zinthu zakuthambo, zimene Yehova Mulungu wanu wazipereka kwa anthu onse okhala pansi pa thambo lonse,+ n’kunyengeka nazo, kuzigwadira ndi kuyamba kuzitumikira.+ 20  Musachite zimenezo chifukwa Yehova ndiye anakutengani n’kukutulutsani m’ng’anjo yachitsulo,+ mu Iguputo, kuti mukhale anthu akeake+ monga mmene zilili lero. 21  “Ndipo Yehova anandikwiyira chifukwa cha inu,+ kotero kuti analumbira kuti ndisawoloke Yorodano, kapena kulowa m’dziko labwino limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kukhala cholowa chanu.+ 22  Ineyo ndifera m’dziko lino.+ Sindiwoloka Yorodano, koma inu muwoloka ndi kutenga dziko labwinoli. 23  Samalani kuti musaiwale pangano la Yehova Mulungu wanu limene anachita nanu,+ ndi kuti musadzipangire chifaniziro, chifaniziro cha chinthu chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu anakuletsani.+ 24  Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wowononga,+ iye ndi Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi.*+ 25  “Ukakakhala ndi ana ndi zidzukulu ndipo mwakhala nthawi yaitali m’dzikomo, n’kuchita zinthu zokuwonongetsa+ mwa kupanga chifaniziro,+ chifaniziro cha chinthu chilichonse, n’kuchita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wako,+ moti n’kumulakwira, 26  ndikutenga kumwamba ndi dziko lapansi+ lero monga mboni zokutsutsani, kuti mudzafafanizidwa mwamsanga m’dziko limene mukupita kukalitenga mutawoloka Yorodano. Simudzatalikitsa masiku anu m’dzikomo chifukwa mudzawonongedwa ndithu.+ 27  Ndipo Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo mudzatsala ochepa+ m’mayiko a mitundu imene Yehova adzakuingitsiraniko. 28  Kumeneko mudzatumikira milungu+ yopangidwa ndi manja a anthu, milungu ya mtengo ndi mwala,+ imene siingaone, kumva, kudya kapena kununkhiza.+ 29  “Mukadzafufuza Yehova Mulungu wanu muli kumeneko, mudzam’pezadi,+ chifukwa mudzam’funafuna ndi mtima wanu wonse ndiponso moyo wanu wonse.+ 30  Pamapeto pake, mawu amenewa akadzakwaniritsidwa pa inu, n’kukhala pamavuto aakulu, mudzabwereradi kwa Yehova Mulungu wanu+ ndi kumvetsera mawu ake.+ 31  Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo.+ Sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuiwala pangano+ la makolo anu limene anawalumbirira. 32  “Tafunsani tsopano, za masiku akale+ inu musanakhalepo, kuchokera pa tsiku limene Mulungu analenga munthu padziko lapansi,+ ndiponso kuchokera kumalekezero ena a thambo kukafika kumalekezero ena a thambo, Kodi chinthu chachikulu ngati chimenechi chinayamba chachitikapo, kapena kodi chinthu ngati chimenechi chinayamba chamvekapo?+ 33  Kodi anthu ena anamvapo mawu a Mulungu akumveka kuchokera pakati pa moto ngati mmene inuyo munawamvera, ndi kukhalabe ndi moyo?+ 34  Kapena kodi Mulungu anayamba wapitapo kukadzitengera mtundu wa anthu pakati pa mtundu wina ndi mayesero,+ zizindikiro,+ zozizwitsa,+ nkhondo,+ dzanja lamphamvu,+ mkono wotambasula,+ ndi zoopsa zazikulu+ zofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Iguputo inu mukuona? 35  Inuyo mwasonyezedwa zinthu zimenezi kuti mudziwe kuti Yehova ndiye Mulungu woona,+ ndipo palibenso wina.+ 36  Anakuchititsani kumva mawu ake kuchokera kumwamba n’cholinga chakuti akulangizeni kuti muzimumvera. Padziko lapansi pano, iye anakuchititsani kuona moto wake woopsa, ndipo munamva mawu ake kuchokera pakati pa moto.+ 37  “Koma mukupitirizabe kukhala ndi moyo chifukwa anakonda makolo anu ndipo anasankha mbewu zawo zobwera pambuyo pawo,+ ndi kukutulutsani mu Iguputo ndi mphamvu zake zazikulu,+ komanso anali kukuyang’anirani. 38  Anachita izi kuti achotse mitundu yaikulu ndi yamphamvu kuposa inu, ndi kulowetsamo inu, kukupatsani dziko lawo kuti likhale cholowa chanu monga mmene zilili lero.+ 39  Inu mukudziwa bwino lero, ndipo muzikumbukira m’mitima yanu, kuti Yehova ndiye Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi.+ Palibenso wina.+ 40  Muzisunga malangizo+ ndi zigamulo zake zimene ndikukulamulani lero. Muzitero kuti nthawi zonse zinthu zikuyendereni bwino,+ inuyo ndi ana anu obwera pambuyo panu, ndiponso kuti mutalikitse masiku anu panthaka imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.”+ 41  Pa nthawi imeneyo, Mose anapatula mizinda itatu kuchigawo chotulukira dzuwa cha Yorodano,+ 42  kuti munthu wopha mnzake mwangozi,+ amene sanali kudana naye kale n’kale,+ azithawirako. Ameneyu azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi ndi kukhala ndi moyo.+ 43  Mizinda yake ndi Bezeri,+ m’chipululu cha dera lokwererapo, wothawirako Arubeni, mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi, wothawirako Agadi, ndi mzinda wa Golani+ ku Basana, wothawirako Amanase.+ 44  Tsopano chilamulo+ chimene Mose anaika pamaso pa ana a Isiraeli ndi ichi. 45  Chilamulocho ndicho maumboni,*+ malangizo+ ndi zigamulo+ zimene Mose anauza ana a Isiraeli pamene anatuluka mu Iguputo. 46  Anawauza zimenezi ali pafupi ndi Yorodano, m’chigwa, moyang’anizana ndi Beti-peori.+ Dera limeneli ndi dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, imene inali kukhala ku Hesiboni.+ Mose ndi ana a Isiraeli anagonjetsa mfumuyi atatuluka mu Iguputo,+ 47  ndipo anamulanda dziko lakelo ndi dziko la Ogi+ mfumu ya Basana. Amenewa ndi mafumu awiri a Aamori amene anali kuchigawo chotulukira dzuwa cha Yorodano. 48  Dera limeneli linayambira ku Aroweli+ m’mphepete mwa chigwa* cha Arinoni mpaka kuphiri la Sione, limene ndi phiri la Herimoni,+ 49  ndiponso dera lonse la Araba+ m’chigawo cha kum’mawa kwa Yorodano, mpaka kunyanja ya Araba+ m’munsi mwa Pisiga.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 34:28.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 20:4.
Kapena kuti “iye ndi Mulungu wansanje (wachangu); Mulungu wosalola aliyense kupikisana naye.”
Kapena kuti “zikumbutso.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.