Deuteronomo 34:1-12
34 Ndiyeno Mose anachoka m’chipululu cha Mowabu kupita m’phiri la Nebo,+ pamwamba pa Pisiga,+ moyang’anana ndi Yeriko.+ Pamenepo Yehova anayamba kumuonetsa dziko lonse, kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani.+
2 Anamuonetsanso dziko lonse la Nafitali, dziko la Efuraimu ndi la Manase, dziko lonse la Yuda mpaka kunyanja ya kumadzulo.+
3 Anamuonetsa Negebu+ ndi Chigawo*+ cha Yorodano, chigwa cha ku Yeriko, mzinda wa mitengo ya kanjedza,+ mpaka ku Zowari.+
4 Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: “Dziko lija ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzalipereka kwa mbewu yako’+ ndi limeneli. Ndakuonetsa kuti ulione ndi maso ako chifukwa sudzawoloka kukalowa m’dzikolo.”+
5 Kenako Mose mtumiki wa Yehova+ anafera pamenepo m’dziko la Mowabu, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula.+
6 Iye anamuika m’manda m’chigwa, m’dziko la Mowabu moyang’anana ndi Beti-peori,+ ndipo palibe amene akudziwa manda ake kufikira lero.+
7 Mose anamwalira ali ndi zaka 120.+ Diso lake silinachite mdima+ ndipo anali adakali ndi mphamvu.+
8 Ana a Isiraeli analira Mose m’chipululu cha Mowabu masiku 30.+ Ndiyeno masiku onse olira maliro a Mose anatha.
9 Yoswa mwana wa Nuni anali wodzazidwa ndi mzimu wa nzeru,+ pakuti Mose anaika manja ake pa iye.+ Choncho ana a Isiraeli anayamba kumumvera ndipo iwo anayamba kuchita monga momwe Yehova analamulira Mose.+
10 Koma mu Isiraeli simunakhalebe mneneri aliyense wofanana ndi Mose,+ amene Yehova anali kumudziwa pamasom’pamaso,+
11 amene anachita zizindikiro ndi zozizwitsa zonse zimene Yehova anam’tuma kukachita m’dziko la Iguputo kwa Farao, kwa atumiki ake onse ndi m’dziko lake lonse.+
12 Simunakhalebe mneneri amene anachita zinthu zazikulu ndi zoopsa ndi dzanja lake lamphamvu, ngati zimene Mose anachita pamaso pa Aisiraeli onse.+