Deuteronomo 33:1-29

33  Tsopano ili ndi dalitso+ limene Mose, munthu wa Mulungu woona,+ anadalitsa nalo ana a Isiraeli iye asanafe.  Ndipo anati:“Yehova anafika kuchokera ku Sinai,+Anathwanima pa iwo kuchokera ku Seiri.+Anawala kuchokera kudera lamapiri la Parana,+Ndipo anali ndi miyandamiyanda ya oyera ake,+Kudzanja lake lamanja kunali ankhondo ake.+   Iye analinso kukonda anthu ake.+Oyera awo onse ali m’manja mwanu.+Iwowa anakhala pansi, pamapazi panu.+Anayamba kulandira ena mwa mawu anu.+   (Mose anatipatsa chilamulo,+Chimene mpingo wa Yakobo uli nacho monga chawo.)+   Mulungu anakhala mfumu mu Yesuruni,*+Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana pamodzi,+Chiwerengero chonse cha mafuko a Isiraeli.+   Rubeni akhale ndi moyo, asafe ayi,+Ndipo anthu ake asakhale ochepa.”+  Popitiriza, iye anapereka dalitso lotsatirali kwa Yuda,+ kuti:“Inu Yehova, imvani mawu a Yuda,+M’bweretseni kwa anthu ake.Manja ake amenya nkhondo pofuna kulanditsa zinthu zake.Mukhaletu mthandizi wake kwa adani ake.”+  Ndipo kwa Levi anati:+“Tumimu ndi Urimu+ wanu ndizo za munthu wokhulupirika kwa inu,+Amene munamuyesa pa Masa.+Munayamba kulimbana naye pafupi ndi madzi a Meriba.+   Munthu amene anauza bambo ndi mayi ake kuti, ‘Sindinawaone.’Ngakhale abale ake sanawavomereze,+Ndipo ana ake sanawadziwe.Pakuti anasunga mawu anu,+Ndipo anapitiriza kusunga pangano lanu.+ 10  Amenewa azilangiza Yakobo pa zigamulo zanu,+Ndi Isiraeli m’chilamulo chanu.+Azipereka nsembe zofukiza kuti muzinunkhiza fungo lake,+Ndi nsembe yathunthu paguwa lanu lansembe.+ 11  Inu Yehova dalitsani mphamvu zake,+Ndipo mukondwere ndi ntchito ya manja ake.+Muvulaze koopsa ziuno za amene akumuukira,+Ndi amene amadana naye kwambiri, kuti asamuukire.”+ 12  Kwa Benjamini anati:+“Wokondedwa+ wa Yehova akhale m’chitetezo cha Mulungu,+Pamene akumutchinjiriza tsiku lonse,+Ndipo iye akhale pakati pa mapewa ake.”+ 13  Ndipo kwa Yosefe anati:+“Dziko lake lipitirize kudalitsidwa ndi Yehova.+Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri zakumwamba, mame,+Ndi madzi akuya a pansi pa nthaka.+ 14  Lidalitsidwenso ndi zinthu zabwino kwambiri, zochokera ku dzuwa,+Ndi zinthu zabwino kwambiri, zokolola za miyezi yosiyanasiyana,+ 15  Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino koposa, za m’mapiri a kum’mawa,+Ndi zinthu zabwino kwambiri za m’mapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale. 16  Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri za padziko lapansi, ndi chuma chake chonse,+Komanso movomerezedwa ndi Iye amene anaonekera m’chitsamba chaminga.+Zimenezi zikhale pamutu pa Yosefe,+Paliwombo pa munthu wopatulidwa pakati pa abale ake.+ 17  Ulemerero wake ndi wofanana ndi wa mwana wa ng’ombe wamphongo woyamba kubadwa,+Ndipo nyanga zake ndi nyanga za ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+Nyanga zimenezo adzakankha nazo anthu.+Adzakankha nazo anthu onse pamodzi mpaka kukafika kumalekezero a dziko lapansi.Nyanga zimenezo ndi anthu masauzande makumimakumi a fuko la Efuraimu,+Ndiponso anthu masauzande a fuko la Manase.” 18  Kwa Zebuloni anati:+“Kondwera Zebuloni iwe, pa maulendo ako,+Ndiponso iwe Isakara, m’mahema ako.+ 19  Adzaitanira mitundu ya anthu kuphiri.Kumeneko adzapereka nsembe zachilungamo.+Pakuti adzayamwa chuma chochuluka cha m’nyanja,+Ndi chuma chobisika cha mumchenga.” 20  Ndipo kwa Gadi anati:+“Wodala ndi iye wofutukula malire a dera la Gadi.+Iye adzakhala ngati mkango,+Ndipo adzakhadzula dzanja, adzang’amba mutu paliwombo.+ 21  Adzatenga gawo labwino kwambiri kukhala lake,+Pakuti gawo loperekedwa ndi wopereka malamulo linasungidwa kumeneko.+Ndipo atsogoleri a anthu adzasonkhana.Iye adzachitadi chilungamo cha Yehova,Ndi zigamulo zokhudza Isiraeli.” 22  Kwa Dani anati:+“Dani ndi mwana wa mkango.+Adzadumpha kuchokera ku Basana.”+ 23  Ndipo kwa Nafitali anati:+“Nafitali wakhutira chifukwa chovomerezedwa ndi Yehova,Ndipo madalitso Ake amuchulukira.Tenga chigawo cha kumadzulo ndi kum’mwera.”+ 24  Kwa Aseri anati:+“Aseri ndi wodalitsidwa ndi ana aamuna.+Akhale wovomerezeka ndi abale ake,+Woponda phazi lake m’mafuta.+ 25  Chitsulo ndi mkuwa ndizo zokhomera chipata chako,+Udzayenda mtima uli phee, masiku onse a moyo wako. 26  Palibe wina wofanana ndi Mulungu woona+ wa Yesuruni,+Amene amayenda m’mlengalenga pokuthandiza,+Amene amayenda pamitambo mu ulemerero wake.+ 27  Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo,+Ndipo iwe uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale.+Adzapitikitsa mdani pamaso pako,+Ndipo adzanena kuti, ‘Awononge!’+ 28  Isiraeli adzakhala motetezeka,+Kasupe wa Yakobo adzakhala mosatekeseka,+M’dziko lokhala ndi chakudya ndi vinyo watsopano.+Ndipo kumwamba kwake kudzagwetsa mame.+ 29  Ndiwe wodala Isiraeli iwe!+Ndani angafanane ndi iwe,+Anthu amene akupulumutsidwa ndi Yehova,+Chishango chako chokuthandiza,+Amenenso ndi lupanga lako lopambana?+Adani ako adzakhala mwamantha chifukwa cha iwe,+Ndipo iwe udzayendayenda pamalo awo okwezeka.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa De 32:15.
Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.