Deuteronomo 32:1-52
32 “Tamverani kumwamba inu, ndiloleni ndilankhule.Ndipo dziko lapansi limve mawu a pakamwa panga.+
2 Malangizo anga adzagwa ngati mvula,+Mawu anga adzatsika ngati mame,+Ngati mvula yowaza pa udzu,+Ngatinso mvula yamphamvu pazomera.+
3 Pakuti ndidzalengeza dzina la Yehova.+Vomerezani ukulu wa Mulungu wathu!+
4 Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro,+Njira zake zonse ndi zolungama.+Mulungu wokhulupirika,+ amene sachita chosalungama.+Iye ndi wolungama ndi wowongoka.+
5 Iwo achita okha zinthu zowawonongetsa,+Si ana ake, chilemacho n’chawo.+Iwo ndiwo m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota!+
6 Kodi mukupitiriza kuchitira Yehova mwa njira imeneyi,+Anthu opusa ndi opanda nzeru inu?+Kodi iye si Atate wanu amene anakulengani,+Amene anakupangani ndi kukuchititsani kukhazikika?+
7 Kumbukirani masiku akale,+Ganizirani zaka za mibadwomibadwo ya m’mbuyomu.Funsa bambo ako ndipo akuuza,+Amuna achikulire pakati panu, ndipo akufotokozera.+
8 Pamene Wam’mwambamwamba anapereka cholowa kwa mitundu,+Pamene analekanitsa ana a Adamu,+Anaika malire a anthu+Poganizira chiwerengero cha ana a Isiraeli.+
9 Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake.+Yakobo ndiye gawo la cholowa chake.+
10 Anam’peza m’dziko lachipululu,+M’chipululu chopanda kanthu, molira zilombo zakutchire.+Pamenepo anayamba kum’zungulira,+ kum’samalira,+Kum’teteza monga mwana wa diso lake.+
11 Monga mmene chiwombankhanga chimagwedezera mwamphamvu chisa chake,Mmene chimaulukira pamwamba pa ana ake,+Mmene chimatambasulira mapiko ake, ndi kutenga anawo,N’kuwanyamula pamapiko ake,+
12 Yehova yekha anapitiriza kumutsogolera,+Ndipo panalibe mulungu wachilendo kuwonjezera pa iye.+
13 Anapitiriza kumuyendetsa pamapiri a dziko lapansi,+Moti anadya zokolola za m’minda.+Anapitirizanso kumudyetsa uchi wochokera m’thanthwe,+Ndi mafuta ochokera m’mwala wa nsangalabwi.+
14 Anamudyetsanso mafuta a mkaka wa ng’ombe ndi mkaka wa nkhosa,+Pamodzi ndi mafuta a nkhosa.Anamudyetsa nkhosa zamphongo za ku Basana, mbuzi zamphongo,+Pamodzi ndi tirigu wabwino koposa ngati mafuta okuta impso.+Ndipo anali kumwa magazi a mphesa monga vinyo.+
15 Yesuruni*+ atayamba kunenepa, anayamba kupanduka.+Iwe wanenepa, wakulupala, wakhuta mopitirira muyezo.+Pamenepo iye anasiya Mulungu amene anam’panga,+Ndi kunyoza Thanthwe+ la chipulumutso chake.
16 Anayamba kuputa nsanje+ yake ndi milungu yachilendo.+Anapitiriza kumukhumudwitsa ndi zinthu zonyansa.+
17 Iwo anali kupereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+Anapereka nsembe kwa milungu imene sanaidziwe,+Milungu yatsopano yongobwera kumene,+Imene makolo anu akale sanaidziwe.
18 Munaiwala Thanthwe limene linakuberekani,+Ndipo munayamba kuiwala Mulungu amene anachititsa kuti mukhalepo kudzera mwa zowawa za pobereka.+
19 Yehova ataona zimenezi anayamba kuwanyoza,+Chifukwa chakuti ana ake aamuna ndi aakaziwo anam’sautsa.
20 Choncho iye anati, ‘Ndiwabisire nkhope yanga,+Ndione kuti ziwathera bwanji.Pakuti iwo ndi m’badwo wokonda zoipa,+Ana osakhulupirika.+
21 Iwo andichititsa nsanje ndi milungu yachabe.+Andisautsa ndi mafano awo opanda pake.+Ndipo ine ndidzawachititsa nsanje ndi anthu achabe,+Ndidzawakhumudwitsa ndi mtundu wopusa.+
22 Pakuti pa kukwiya kwanga moto wayaka,+Ndipo udzayaka mpaka kukafika ku Manda,* malo a pansi penipeni.+Udzanyeketsa dziko lapansi ndi zipatso zake,+Ndi kuyatsa maziko a mapiri.+
23 Ndidzawonjezera masoka awo,+Mivi yanga ndidzaithera pa iwo.+
24 Adzalefuka ndi njala+ ndi kuwonongeka ndi matenda otentha thupi koopsa,+Ndi chiwonongeko chowawa.+Ndidzawatumizira zilombo za mano ataliatali,+Pamodzi ndi njoka zapoizoni za m’fumbi.+
25 Kunja lupanga lidzawasandutsa anamfedwa,+Ndipo mkati mwa nyumba, mantha adzawasandutsa anamfedwa.+Zimenezi zidzawaphera anyamata ndi anamwali,+Mwana woyamwa pamodzi ndi munthu wa imvi.+
26 Ndikananena kuti: “Ndidzawabalalitsa,+Ndidzachititsa anthu kuti asatchule n’komwe za iwo,”+
27 Ngati ndikanati sindikuopa kusautsidwa ndi mdani,+Kuti adani awo angamve molakwa,+Kutinso anganene kuti: “Dzanja lathu lapambana,+Ndipo si Yehova amene wachita zonsezi.”+
28 Pakuti iwo ndi mtundu wopanda nzeru,+Ndipo ndi osazindikira.+
29 Akanakhala anzeru,+ akanaganizira mozama zimenezi.+Akanalingalira kuti ziwathera bwanji.+
30 Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000,Kapena anthu awiri angapitikitse bwanji anthu 10,000?+
N’zosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+Komanso ngati Yehova atawapereka.
31 Pakuti thanthwe lawo silofanana ndi Thanthwe lathu,+Ndipo adani athu angavomereze zimenezi.+
32 Mtengo wawo wa mpesa ndi wochokera ku mtengo wa mpesa wa ku Sodomu,Ndi kuminda ya m’mapiri a ku Gomora.+
Zipatso zawo za mphesa ndi zakupha,Ndipo ndi zowawa.+
33 Vinyo wawo ndi poizoni wa njoka zikuluzikulu,Ndiponso ndi poizoni wakupha wa mamba.+
34 Kodi sindinasunge zimenezi,Ndi kuziikira chidindo m’nkhokwe yanga?+
35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+Pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo lidzaterereka poyenda,+Pakuti tsiku la tsoka lawo layandikira,+Ndipo zowagwera zikufika mofulumira.’+
36 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,+Ndipo adzamva chisoni chifukwa cha atumiki ake,+Chifukwa adzaona kuti thandizo lawachokera.Adzaona kuti pangokhala munthu wonyozeka ndi wopanda pake.
37 Pamenepo iye adzati, ‘Ili kuti milungu yawo,+Thanthwe limene anathawirako,+
38 Milungu imene inali kudya mafuta a nsembe zawo,+Ndi kumwa vinyo wa nsembe zawo zachakumwa?+Ibwere kudzakuthandizani.+Ikhaletu malo anu obisalamo.+
39 Onani tsopano kuti ndine Mulungu,+Ndipo palibe milungu ina pamodzi ndi ine.+Ndimapha ndiponso ndimapereka moyo.+Ndavulaza koopsa,+ ndipo ine ndidzachiritsa,+Palibe aliyense wonditsomphola m’dzanja langa.+
40 Ndikukweza dzanja langa kumwamba polumbira,+Ndipo ndikunena kuti: “Pali ine, Mulungu wamoyo wosatha,”+
41 Ndikanoladi lupanga langa lonyezimira,+Dzanja langa likagwira chiweruzo,+Ndidzalipsira adani anga,+Ndipo ndidzabwezera chilango kwa odana nane kwambiri.+
42 Ndidzaledzeretsa mivi yanga ndi magazi,+Magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa.Ndipo lupanga langa lidzadya nyama,+Pamodzi ndi mitu ya atsogoleri a adani.’+
43 Kondwerani, mitundu inu, pamodzi ndi anthu ake,+Pakuti adzabwezera magazi a atumiki ake,+Ndipo adzabwezera chilango kwa adani ake,+Nadzaphimba machimo a dziko la anthu ake.”
44 Pamenepo Mose anabwera ndi kulankhula mawu onse a nyimbo iyi m’makutu mwa anthu onse,+ iye pamodzi ndi Hoseya* mwana wa Nuni.+
45 Mose atamaliza kulankhula mawu onsewa kwa Aisiraeli onse,
46 anapitiriza kuwauza kuti: “Ganizirani mofatsa mawu onse amene ndikulankhula mokuchenjezani lero,+ ndipo muuze ana anu kuti aonetsetse kuti akuchita zimene mawu onse a chilamulo ichi akunena.+
47 Pakuti amenewa si mawu opanda pake kwa inu,+ chifukwa mawu amenewa ndiwo moyo wanu.+ Mwa kutsatira mawu amenewa mudzatalikitsa masiku anu panthaka imene mukupita kukaitenga kukhala yanu, mutawoloka Yorodano.”+
48 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose pa tsiku lomweli kuti:
49 “Kwera m’phiri ili la Abarimu,+ phiri la Nebo,+ limene lili m’dziko la Mowabu, moyang’anana ndi Yeriko, ndipo uone dziko la Kanani limene ndikupereka kwa ana a Isiraeli kuti likhale lawo.+
50 Pamenepo ukafera m’phiri limene ukukwera ndi kugona ndi makolo ako,+ monga mmene Aroni m’bale wako anafera m’phiri la Hora+ ndi kugona ndi makolo ake.
51 Izi zili choncho chifukwa anthu inu munachita mosakhulupirika kwa ine+ pakati pa ana a Isiraeli, kumadzi a pa Meriba+ ku Kadesi, m’chipululu cha Zini. Ndiponso chifukwa chakuti anthu inu simunandilemekeze pakati pa ana a Isiraeli.+
52 Pakuti udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa m’dziko limene ndikupereka kwa ana a Isiraeli.”+
Mawu a M'munsi
^ Kutanthauza “Wolungama.” Limeneli ndi dzina laulemu la Isiraeli.
^ Onani Zakumapeto 5.
^ Dzina lakale la Yoswa.